Akunthana kamba ka mabodza
Amai awili ku Ndirande mu nzinda wa Blantyre akunthana kodetsa nkhawa wina atadziwa kuti nzake amanena mabodza kwa mwamuna wake yemwe ali ku joni.
Chilombo cha gule kamkulu chikwapulidwa
Chilombo china cha gule wamkulu anachikhaulitsa pochikwapula kolapitsa pa mudzi wa Dambo kwa Kuntaja m’boma la Blantyre.
Wamisala alira mokweza kamba kachipewa
Wamisala wina kwa Santhe mboma la Kasungu analila kwambili ataona chipewa cha mkulu wina chili pansi.
Anthu akuntha kondakitale
Anthu omwe anakwera mini bus ina kuchokera ku Limbe kupita ku Mangochi akuntha kondakitala wa galimotoyo mpaka thapsya ati chifukwa anachitila mwano mai wina yemwe anamupitiriza dale pa stegi yotsikira.