You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma18/07/15

18/07/15

Written by  Newsroom

Akunthana kamba ka nsanje
Amai ena awiri kwa Chadzunda ku Blantyre akunthana kwambiri chifukwa cha nsanje.

21
July

Nkhani-yi ikuti mkulu wina adakwatira mai wina mpaka kumbelekela ana awiri. Koma anthu-wo atasiyana maganizo pa nkhani zina banja-lo linatha. Patapita ka nthawi mwamuna-yo anakwatilanso mai wina. Koma tsiku lina mkazi wa kale-yo anaganiza zopita kwa mwamuna wake wa kale-yo kuti akatenge katundu wake. Mai-yo atafika uko anayamba kulongedza katundu-yo ndipo mwamuna uja sanamuletse chifukwa choti amadziwa kuti katundu amatengayo ndi wakedi maiyo. Koma mkazi watsopano wa bambo-yo atafika pakhomo-po ndi kuona momwe awiri-wo amachitila akuti anachita nsanje ndipo mtima unamuwawa kwambiri. Apa mkazi watsopano-yo akuti anayamba kuchita phokoso mpaka kuyamba kugwirana ndi mkazi mzakeyo mamuna uja ali duu osaleletsa. Anthu oyandikana nawo nyumba ndiwo analeletsa nduyo.


Banja liweyeseka kamba kogulisa chimanga
Banja lina kwa Mthilamanja ku Mulanje laweyeseka mkazi atazindikila kuti mwamuna wake wakhala akugulitsa chimanga mobisa ndalamazo mkumamwera mowa. Mai wa pakhomo-po akuti amatakataka pochita bizinezi pamene mwamuna wake ndi mlimi. Koma ngakhale kuti chaka chino banjalo silinakolole chimanga chambiri mamunayo anayamba kuba chimanga m’nyumba nkumakagulitsa ndipo nthawi zina amatenga chimangacho nkumakasinthanitsa ndi mowa. Tsono tsiku lina mai-yo atasunzumila mchipinda chomwe amasungamo dzokolola, anadabwa kuona kuti matumba achepamo. Iye atafunsa ana apakhomopo anaulula kuti atate awo ndiwo amatenga chimanga-cho. Mkazi wa bambo-yo anakwiya kwambiri ndipo atafunsa mwamuna-yo za chimanga-cho anayankha mmaso muli gwaa kuti anagulitsa chimanga-cho kuti apeze ndalama zokadzipepesela pomwera kabanga. Pakadali pano banja-lo silikugwilizana monga kale chifukwa cha nkhani-yi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter