You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma13/07/15

13/07/15

Written by  Newsroom

Akana kusegula manda kamba ka ngongole ya malemu
Nyakwawa ina kwa Mphuka m’boma la Thyolo yakhumudwitsa anthu pokana kutsekula ku manda kuti ati malemu womwalirayo wapita ndi ngongole.

13
July

Nkhaniyi ikuti malemuyo anali ndi ngongole ndi nyakwawayo ya ndalama zokwana K5,000.00 koma chifukwa choti wakhala akudwala kwa miyezi isanu analephera kubweza chikweretecho, kamba ka izi nyakwawayo imaonjezera ngongoleyo ndi five-thousand kwacha pa mwezi mpaka ndalama zonse zinakwana 25-thousand kwacha. Koma mwatsoka mkulu yemwe amadwalayo anamwalira , ndipo achibale atatumiza uthenga kwa nyakwawa inayankhula m’maso mu gwa!!! kuti akufuna aku banja ayambe abweza ndalama zomwe malemuyo adabwereka asanakatsekule ku manda ndikuika zovutazo. Kamba ka izi malirowo anakhala m’nyumba kwa masiku angapo achibalewo akufuna-funa ndalama zobweza kwa nyakwawayo. Achibalewo atabwereka ndalamazo , nyakwawayo inalamula adzukulu kupita ku manda ndikukakumba dzenje la manda ndipo malirowo anaika patatha masiku angapo. Mikoko yogona komanso anamfedwa anakadandaula nkhaniyi kwa mfumu ya m’deralo. Anthu m’deralo akudikira ndi chidwi kuti amve momwe nkhaniyi ithere. Pakadali pano nyakwawayo yathawa pa mudzipo ndipo komwe yalowera sikukudziwika mphepo itampeza kuti ikufunika ku bwalo la mfumu ya mderalo.

 


Athamangitsa abusa kamba kachimasomaso
Akhristu okwiya a mpingo wina kwa Mziza m’boma la Kasungu apitikitsa mbusa wawo pamalopo kamba ka khalidwe lake lachimaso-maso komanso kudya za mkachisi. Mbusayo wakhala pa mpingowo nthawi yochepa yokha kotero kuti akhristu akusiyanitsa ndi yemwe amatumikira ku malowo mpingowo mbuyomu. Potopa ndi khalidwe la mbusayo a komiti atakambirana naye kwa nthawi yaitali. Akhristuwo anakachita hayala lorry ndikulongedza katundu wa mbusayo komanso kukhoma nyumba ya mpingo ndikumulozera msana wa njira kutanthauza kuti achoke pa mpingowo. Mbusayo anagwira njakata poganizira kuti palibe komwe aku likulu la mpingowo akumutumiza kuti akagwire ntchito yake. Ngakhale akhristu wokwiyawo anamuumiriza kukwera galimoto ya lorry-yo cholinga chawo nkuti akamutule kumudzi kwao. M’mene timalandira nkhaniyi nkuti dalaivalayo akunyamula ku Kasungu kupita kumudzi kwa mbusayo. Sitikudziwa kuti akulikulu la mpingowu atani pa nkhaniyi.

 

 

Makolo alipira K25,000 kamba ka mwana wawo
Makolo a m’nyamata wina wa zaka khumi ndi chimodzi apa mudzi wa Mwaza kwa Santhe m’boma la Kasungu awalipitsa K25,000 yoonjezera mwana wao atabera venda wina wogulitsa sawa K25,000. Nkhaniyi ikuti m’nyamatayo amazungulira-zungulira pa msika wapa Mwaza popanda chochita. Ndipo amayang’anitsitsa venda wina yemwe amagulitsa malonda a mtedza pamalowo.Vendayo atangofumuka pang’ono m’nyamatayo anathamanga ndikukhwatula ndalama zokwana 25-thousand Kwacha pa malo a geni ya vendayo ndikuthawa. Anthu ena ndiwo anaona m’nyamatayo akuthawa ndipo atamuthamangitsa anamugwira ndikukamupereka kwa wapampando wa mu msikawo. M’nyamatayo atamukwenya anabweza ndalamazo koma makolo ake awalamulanso kuti alipire chindapusa cha K25,000. Makolowo akupusa mutu wopanda m’nyanga kuphelezera mwambi uja wakuti nkhuyu zodya mwana zimapota wamkulu.

 

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter