You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma10/07/15

10/07/15

Written by  Newsroom

Mfumu ithetsa banja kamba ka nsanje
Mfumu yina kwa Nsamala m’boma la Balaka lathetsa banja lake chifukwa cha msanje.

10
July

Nkhaniyi ikuti Mkazi wa mfumuyo amagulitsa mowa wa kabanga pa khomopo koma mkuluyo wakhala akukaikira za mayendedwe a mayiyo kuti akuyenda ndi madoda ena omwe amadzamwa mowa pa khomopo. Kukaikirako kunayambika chifukwa choti m’modzi mwa anthu omwe amadzagula mowao ndi mamuna wakale wa mayiyo koma anasiyana naye pa zifukwa zina. Mfumuyo wakhala akudzudzula mkazi waoyo ponena kuti akupitilizabe kuzemberana ndi mzaoyo koma mkaziyo wakhala akutsutsa za mphekeserayo. Mfumuyo inaona kuti mkazi waoyo sakusintha anangoganiza zosiya banja mayiyo nakakhala ndi achemwali awo mu mzinda wa Blantyre ati ponena kuti ngati angakhalebe mudzimo akhoza kulakwa. Pakadali pano chemwali wa Mfumuyo ndi yemwe akugwirizila ntchito zonse za ufumuwo. Anthu mderalo akudabwa ndi zomwe wachita mfumuyo ponena kuti , Mfumuyo wakhala akungokayikira koma sanamugwirepo mayiyo.

 


Mfumu ichita zadama ndi mzukulu wake
Tili m’boma lomwelo la Balaka Mfumu yina ikukhala mobindikira mnyumba mpaka kulephera kuweruza milandu ataipezerela ikuchita zachisembwere ndi mdzukulu wake ku nyumba ina yogona alendo. Nkhaniyi ikuti Mkazi wa Mfumuyo wakhala akukaikira mayendedwe a mwamuna waoyo ndi mdzukuluyo. Apa mayiyo anangoti tsiku lina zidzaululika zokha ngati zili zoona. Mwana wa chemwali wa mayiyo tsiku lina ananyamula ganyu lokatula katundu wa alendo ku nyumbako, koma anaona ngati kutulo ataona a mfumuwo akulowa chipinda china cha alendo chapa malopo ndi mdzukulu waoyo. Iye anathamangira kukauza mayi akewo. Apa mayiyo anamema anthu kuti akawathandize kukaona za malodzazo. Gululo kunali kuthidzimula anthuwo koma mwatsoka a mfumu aja anavumbuluka kusiya mdzukulu uja ali m’manja mwa anthu. Anthuwo anathidzimula kolapitsa mtsikanayo. Pakadali pano mikoko yogona ndi nduna za mfumu anenetsa ati chita kanthu pa nkhaniyi.

 

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter