You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma08/07/15

08/07/15

Written by  Newsroom

Wamisala azunguza mayi wina kamba kabuluku othina
Mayi wina pa malo okwelera bus yopita ku Mulanje waona ngati malodza wamisala atayamba kumuzazila ati kamba koti anavala buluku lothina.

08
July

Nkhaniyi ikuti mayiyo anachoka ku nyumba kwake akuzimva kuti watchena koma anakhumudwa wamisala wina atayamba kumuzazira ndi kumulalatira pamene amaonetsa chovala cha mkati komanso mikanda. Wamisalayo akuti anauza mayiyo kuti alibe nzeru zaumunthu chifukwa choti akunyoza chilengedwe cha Mulungu pomulenga iyeyo kukhala mkazi. Anthu omwe anali pamalopo amangomvetsera ndi chidwi koma m’menemo nkuti mayiyo atanyowa kwambiri. Itafika minibus yopita kwa Goliati mboma la Thyolo mayiyo anangodumphiramo koma chonsecho amapita ku Mulanje. Anthuwo atatsala anayamba kusonkhetsa ndalama zomwe anamupatsa wamisalayo ati pomuthokoza chifukwa chodzudzula mayiyo. Anthuwo ati akukhulupilira kuti mayiyo sadzavalanso buluku lothina chifukwa cha zomwe wazionazo.

 

 

Awona zakuda atamupezelera ndi mkazi wamwini
Mkulu wina m’dera la Mfumu Chipeta mboma la Mzimba waona zakuda atamupezelera ndi mkazi wa mwini mnyumba. Nkhaniyi ikuti mkuluyo ali pa banja koma anachita chibwenzi ndi mayi wina yemwenso ndi okwatiwa. Mwini mkaziyo wakhala akumva mphekesera kuti mkuluyo akuyenda ndi mkazi wake koma amadikira la 40. Patsikulo mkuluyo anatsanzika mkazi wake kuti akuchokapo koma chonsecho amafuna kugwira mwamuna nzakeyo. Mkati mwa usiku, mkuluyo anatulukira pakhomopo ndipo atagogoda anadabwa chibwibwi cha mkazi wakeyo. Atalowa mnyumbamo anapezadi mwamuna nzakeyo ndipo apa chindeu chinabuka pakati pa amuna awiriwo. Pa ndeuyo, mwamuna wakubayo anachepera mphamvu koma mwa mwayi anapulumuka nkuthawa. Panopa mkuluyo sakuoneka m’mudzimo ndipo mabanja onse awiri omwe akhudzidwa ndi nkhaniyi asokonezeka.

 

 

Achosa mkata pamanda uyikayika
Mkulu wina kwa Wimbe mboma la Kasungu wadabwitsa anthu atakachotsa nkhata pa mtumbira wa mbale wake yemwe anaikidwa pa manda ena m’mudzimo. Nkhaniyi ikuti masiku apitawa mbale wake wa mkuluyo anamwalira ndipo monga mwa mwambo achibale anayifera kugula nkhata zapamwamba zokaika pa mtumbira wa malemuyo. Koma mkuluyo atapita ku nyumba mtima unamukanika mpaka anapita kumandako kukachotsa nkhatazo nkukaziika m’nyumba mwake. Zimenezi zinadabwitsa anthu ambiri m’mudzimo ndipo ena anakadziwitsa mfumu ya m’deralo. Mfumuyo itamufunsa mkuluyo chifukwa chomwe anachitira zimenezi anayankha zosagwira mtima ponena kuti akuopa kuti mbava zingayambe kuba nkhata zapamwambazo. Anthu ambiri ati sakumvetsa chifukwa chomwe mkuluyo wachitira zimenezi ndipo ena akuti mwina mkuluyo ndi wokhwima.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter