Nkhani-yi ikuti m’nyamata wina anamwalila ngakhale kuchipatala ananena kuti sadamupeze ndi matenda alionse. Mwambo onse pakhomo unayenda bwino kwambili koma zinthu zinaimitsa mitu mikoko yogona pa ulendo wopita kumanda ataona malemuyo ali patsogolo pagulu la anthu omwe amapita kumanda. Pa chifukwa ichi, nyakwawa inalamula adzukulu ndi anthu ena kuti athamangitse m’nyamatayo koma chodabwitsa mchakuti atayamba kumuthamangitsa analowelela m’madimba osaonekanso. Pa chifukwa ichi, nyakwawa yomwe inali yokhumudwa inalamula anthu-wo kuti akaikebe malilowo kumanda. Panopa, chomwe chikudabwitsa anthu mchakuti pakhomo la achibale am’nyamatayo akumamva kugogoda usiku ndipo akamatsekula akumamva kuti munthu akuthawa. Panopa anthu ambili m’mudzimo ati akuganiza kuti m’nyamatayo achita kumupha m’matsenga ndikuti m’mandamo adakaikamo chinthu chosadziwika. Panopa, achibale amalemuyo akuti akukonza zokaponda ponda kwa mkulu wina wa zitsamba ku Mozambique.
Adziipisila m'buluku kamba ka mowa
Mkulu wina m’dera la Mfumu Kalamba mboma lomwelo la Kasungu akungobindikira mnyumba chifukwa cha manyazi zitadziwika kuti anadziyipitsila mbuluku chifukwa chomwa mowa wa kachasu mopyola muyezo. Yemwe watitumizira nkhaniyi wati mkuluyo ndi mbiyang’ambe ndipo anthu anafika pomupatsa dzina loti njanje. Pa tsikulo mkuluyo anapita kukamwa mowa wa kachasu pa nyumba ina koma akuti anaonjeza chifukwa anamwa yekha mavelemoti asanu. Chifukwa choledzera amalephera kudzuka mpaka anadziyipitsila mbuluku. Anthu omwe anali pamalopo anangodabwa ntchentche zagilini zikumulondola mkuluyo ndipo atamuyandikira mpomwe anamva fungo loipalo. Pamenepatu wachifundo anasowa ndipo aliyense amangomuthawa. Kenaka anthu anamuunjilira nkuyamba kumuseka komabe mkuluyo sanachitepo kanthu chifukwa choti thupi lake lonse linali lolobodoka ndi mowawo. Mowawo utamukungunuka anayamba kudzikoka kumapita kwawo koma m’menemotu nkuti anthu akungomukuwiza. Kuyambira pa tsikulo mkuluyo akuyenda zamadulira pochita manyazi ndi nkhaniyi.