Malinga ndi amene watitumizila nkhani-yi mdelalo muli nyakwawa ziwili zomwe ndipa chibale ndipo kwanthawi yaitali zakhala zikudelelana kuti wina ndiye akuyenela kulamulila dela lonse. Wina mwa amuna awiliwo ndi nyakwawa pamene wina ndi gulupu ndipo ndi munthu ndi malume wake. Tsono mwambo olambula kumanda utatha mwa mwambo woyendetsa mwambowo anapempha agulupu kuti alankhule. Asadayambe kulankhula mwana wa nyakwawa inayo anaimilila ndikuyamba kuloza zala kukamwa agulupu kuti awaswa akapitiliza kulankhula ndipo m’malo mwake anadzutsa bambo ake kuti azilankhula ndikuti akamaliza akalowe m’nyumba ina akakhwasule. Pa chifukwa icjhi, mafumu awili onse amalankhula pamwambowo zomwe zinadzetsa kusamvana. M’malo mwake agulupu akuti anaimilila akusasa m’matako kumapita kwao ndi nduna zao ponena kuti a Tambala awili salila khola limodzi. Anthu ambili akuti anafa ndi phwete pa zomwe anthu awiliwo akuchita ndipo akulu akulu ena m’mudzimo ati akukonza zokatula nkhaniyi kwa mfumu ya ndodo podziwa kuti ati ndi yomwe ithetse kusamvanako ngakhale akuti nkhani yakula ndiyolimbilana mswahala. Panopa, makosana awiliwo akuti akuonana ndi diso lofiila ndipo nkhaniyi sikuguga mdelalo.
Apeza mutu ndi chikopa cha galu
Anthu okhala mdela lina mu mzinda wa Blantyre akhumudwa atamva kuti ana ena omwe amasewela pamalo ena anapeza mutu wa Galu komanso chikopa chake chili pomwepo kusonyeza kuti alipo amene amasenda kuti akagulitse kanyenya. Malinga ndi amene watumiza nkhani-yi wati ana ena anapita pa thengo lina komwe amasaka ziwala ndipo akuti anadzidzimuka kupeza mutu wagalu woonetsa kuti anachita kuudula ndi mpeni. Atayenda pang’ono akuti anapezanso chikopa cha galu uja ndi mapazi ake ndipo nthawi yomwe-yo anapita kukanena kunyumba kwao, malinga nkuti anali ataona kale mkulu wina atanyamula thumba lomwe linali ndi magazi dzulo lake. Mkuluyo yemwe akuti amaotcha kanyenya anadzela pathengo ataona kuti anao amamuyang’ana ndi chidwi kwambili. Panopa, akulu akulu a mdela lomwe nkhaniyi yachitika ati akukukonza zothamangitsa mkulu wophika kanyenya pamsika wa mdelalo. Anthu ambili omwe amva nkhani-yi ati ndiwokwiya kwambili kuti mkuluyo wakhala akuwadyetsa nyama ya galu.