You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma02/07/15

02/07/15

Written by  Newsroom

Alandidwa phone ya m'manja kamba kochulusa zibwenzi
Mkulu wina kwa Kanduku mboma la Mwanza waona mbwadza mkazi wake atamulanda phone ya m’manja chifukwa chowirikiza zibwenzi.

02
July

Nkhaniyi ikuti mkuluyo anakwatirana ndi mkazi wakeyo pakanthawi koma akuti Mayiyo amakhalira kulimba m’banjamo chifukwa cha khalidwe la mwamuna wakeyo lokonda akazi. Mayiyo wakhala akudzudzula mwamuna wakeyo paza khalidwe loipalo koma amangotayira malangizowo ku nkhongo. Masiku angapo apitawa mkuluyo akuti anaonjeza pomwe amalankhulana ndi zibwezi zakezo mkazi wakeyo ali pomwepo. Potopa ndi khalidweli mayiyo anatsomphola phone ya mwamuna wakeyo ndipo anamuuziratu kuti samupatsanso phone-yo. Mayiyo analamula mwamuna wakeyo kuti ali ndi ufulu kukadandaula kulikonse za nkhaniyi koma akuti mpaka pano mwamunayo sanakatule nkhaniyi kulikonse ngakhale kwa ankhoswe a banjalo. Chifukwa chpchita manyazi ndi nkhaniyi, mkuluyo akungobindikira m’nyumba poopa kuti anzake azimuseka.

 


Afukula manda a mwana wawo kuti awagulitse
Anthu a m’dera la Mfumu Chitukula mboma la Lilongwe ati akuda nkhawa ndi zomwe yachita nyakwawa ina ya m’deralo pomwe inalemba aganyu kuti akafukule manda a mwana wake ati ncholinga choti malowo awagulitse kwa munthu wina. Yemwe watitumizira nkhaniyi wati nyakwawayo inagwirizana ndi munthu wina kuti amugulitse malo. Polingalira, inaganizira za malo ena omwe ndi manda a mwana wake wa mwamuna yemwe anamwalira ku ndende masiku apitawa. Pachifukwachi nyakwawayo inalemba ganyu anyamata ena atatu a m’mudzimo kuti akafukule mandawo ndipo atachotsamo mtembowo anakakumba pa malo ena apatali mkatikati mwa mandawo ndikuikamo thupilo. Anyamatawo anachitadi zimenezi usiku ndipo zikumveka kuti anawapatsa 30 thousand kwacha. Kutacha m’mawa, anthu ena omwe amadutsa ku mandako anadabwa ndipo atafufuza mpomwe zinadziwika kuti anthu ena afukula mandawo. Pamenepa nkhaniyi inakafika kwa Mfumu yaikulu ya m’deralo ndipo itafufuza kunapezeka kuti mkuluyo anagulitsa malowo kwa munthu wina kuti amangepo nyumba. Pakadali pano mafumu a m’deralo ali mkati kukambirana kuti awone chomwe angachite pa nkhaniyi komabe zikumveka kuti nyakwawayo ayithothola pa udindo chifukwa cha zomwe inachitazo.

 

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter