Nkhaniyi ikuti mwamuna wa mkaziyo adapita ku Mozambique kukasaka maganyu poganizira za mavuto apa khomo pake. Ali kumeneko, mphekesela inamupeza kuti mkazi wake kuno ku mudzi waonjeza uhule. Apatu iye anaganiza zopotoloka kumudzi ndipo sanadziwitse mkazi wakeyo kuti akubwera ncholinga choti adzagwire ngatidi maiyo akuzembetsana ndi amuna ena. Atafika pa khomo cha m’ma eight koloko usiku nkugogoda, mkazi uja anatsekula chitseko ndipo anadzidzimuka ataona kuti ndi mamuna wake. M’malo molandila chikwama anangotuluka m’nyumbamo nkuyamba kuthawa. Apatu mpamene mphongoyo inadamwa ndipo inalowa m’nyumbamo msanga kuti ikaone kuti munali ndani. Atalowa anangoti maso gululu ndi mamuna wina ali gadaa pa bedi. ndipo nthawi yomweyo anamugwila ndikuyamba kumuswa. Akuyitikita, mbavayo inapeza mpata ndikuthawa mnyumbamo koma pa nthawiyi nkuti ili mbulanda. Mwini mkaziyo anangoola zovala za mamuna wakubayo ndipo anakatula nkhaniyi ku anyakwawa. Mkazi wakeyo chichokele tsiku limenelo, sakudziwika komwe ali, koma anthu akuti mwina anapita kwa amake ku Chiladzulu.
Akunthana kamba ka galu okudya ndiwo
Amai ena awiri a nyumba zoyandikana ku Makata mu mzinda wa Blantyre akutumula kwambiri, galu wa m’modzi mwa amaiyo atadya chambo chomwe mzakeyo anachiyanika pakhonde mu lichero. M’modzi wa amaiyo akuti anakagula chambo ku msika mamuna wake atamuyimbila telefoni kuti akazinge m’mafuta kuti adyele chakudya cha madzulo kapena kuti mgonero. Munthu wa maiyi anapitadi ku msika nkukasankha chambo chiwri chikuluchikulu chomwe anagula 3-thousand kwacha chonse. Ndipo atafika ku nyumba anachidula nkuchiwaza mchere ndipo kenaka anachiyanika mu lichero kudikila kuti achikazinge. Tsono akukangalika ndi kukoleza mbaula, galu wa neba anadutsa pa khomopo mpaka kutengapo nsomba zonsezo kukadyela kuseli kwa nyumba. Mwana wina ndi amene anaona galuyo atapana somba yomaliza ndipo nthawi yomweyo anakadziwitsa mwini ndiwozo yemwe anakwiya kwambiri. Maiyo anafunafuna mwini galuyo ndipo atamupeza anamuuza kuti sombazo ndiza 3-thousand kwacha ndipo akuyenera kubweza. Mzakeyo sanamuyankhe bwino ndipo mkangano unabuka mpaka amai awiriwo kumenyana. Pakadali pano amuna a amaiwo omwe amagwirizana kwambiri akambilana nkhaniyi ndipo awayanjanitsa akazi awowo.