Error
  • JUser: :_load: Unable to load user with ID: 43
You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma17/06/15

17/06/15

Written by 

Okonda kuzembelera akazi aeni alandidwa ndalama
Mkulu wina wakwa Chikowi m’boma la Zomba wotchuka ndikuzembera akazi a weni awona polekera atalandidwa ndalama zake zonse za malipilo ndi njinga yakapalase yomwe imamuthandizila kupita ku ntchito.

18
June

Nkhaniyi ikuti imodzi mwa zibwenzi za mkuluyo ndi mkazi wa mulonda wina mderalo ndipo anthu awiriwo anagwirizana kuti bamboyo afike ku nyumbako cha m’ma 9-koloko usiku. Ali mkati mwa macheza,mlonda uja pokhala kuti wakhala akukaikira mayendewdwe a mkazi wakeyo , pa tsikulo anapempha ku ntchito kuti sakumva bwino thupi ndipo anamuvomereza ndipo anapitadi kuyumba kwake. Atafika ku nyumba anaona ngati kutulo atapeza njinga ya bambo wopusayo pakhonde. Mlondayo pokhala kuti ndi nsilikali anakonzekeratu ndi chibonga komanso chikwanje ndipo anayamba kuyitana mkazi wake kuti amutsekulire msanga. Apa mkaziyo anadziwiratu kuti zinthu zavuta anatenga nthawi kuti atsekure, koma bamboyo anangothyola chitseko cha nyumbayo ndikuuza bamboyo kuti sakufuna zambiri, ngati akufuna moyo apereke ndalama zonse anali nazo pamodzi ndi njinga ndipo zinachitikadi. Apa wakubayo anapeza mpata wothawa uku akupumila m’mwamba. Mbuyomuno bambo uja anathetsa banja lake ndi mkaziyo, ndipo mayiyo akulilira ku utsi chifukwa chothetsa banja lake ndi manja ake. Bamboyo wanenetsa kuti wasiya khalidwe lake lachisembwere ndipo wayamba kupemphera kwambiri.

 


Ayendetsedwa bunobuno kamba ka chimasomaso
Mayi wina wachimasomaso ku Bunda kwa Chadza m’boma la Lilongwe waona polekera atayendetsedwa buno bwamuse anthu atamupezerela akuchita zachisembwere dzuwa likuswa mtengo ndi mwamuna wa mwini. Pa tsikulo mayiyo anauza mwamuna wakeyo kuti adzikhala moyo wa Gender ndipo anatuma bamboyo ku chigayo ndipo bamboyo sanawilingure koma osadziwa kuti anali ndi zolinga zina. Ali ku chigayo mayi uja anakakumana ndi chibwenzi chake ku nyumba ya nsuweni wake ndipo zinachitikadi. Nsuweni wa mayi uja pokhala kuti anali atatopa ndi khalidwe la mayiyo lozembera mwamuna wakeyo anathamanga kukauza mamunayo ndipo anamuuza kuti ngati sakavomera akakaitana akangokankha chitsekocho ndipo zinachitikadi. Bambo uja pamodzi ndi anzake aja kunali kumenya kosayang’ana nkhope anthu awiri onsewo, koma mwatsoka bambo wakubayo anathawa koma anthu anali atamuzindikira. Mayiyo anthu anamuyendetsa mbulanda pofuna kuti asiye khalidwe lake. Mikoko yogona ya m’mudzimo inachonderela anthuwo kuti amupatse zovala zake ndipo anawatsikimizila kuti akhala naye pansi, koma mayiyo pakadali pano wanenetsa kuti achimina koma banja lakelo latha. Bambo wopanda manyaziyo pakadali pano sakudzwika komwe ali koma mkazi wake watenga katundu wake ndipo wapita kwao ponena kuti banja sakulifunanso ndi bamboyo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter