Nkhaniyi ikuti gogo wamamuna wa maiyo akudwala ndipo chifukwa chosowa omuyang’anila mwamuna wa maiyo yemwe ndi mkamwini wapa khomopo amakagona ndi gogoyo mnyumba yake mcholinga choti adzimuyang’anila bwino. Maiyo m’malo moyamika zomwe mwamunayo akhala akuchita posamala gogoyo, mwamunayo anapezerela yekha mkazi wakeyo ali buno-buno ndi mwamuna wamwini mnyumba yake yomwe anamanga ndi maiyo. Izi zinachitika pamene mwamunayo anabwerela kunyumbako mcholinga choti akatenge nyali ya solar ndi machesi. Apa mwamunayo anadzimvera chisoni polingalira kuti amangothandiza ndipo anaitana anthu kuti adzaone zamalodzazo uku atatseka chitseko ndi miyala komanso zipika kuti anthuwo alephere kuthawa. Chifukwa cha kuipidwa ndi zomwe maiyo anachita anthu omwe anadzathandizawo kunali kumenya kwa chakwanu leka ndikusiya anthu awiriwo ali thaphya uku ali buno-buno. Anthu atalangiza kuti akokere anthuwo ku bwalo mwamunayo anakana ndipo m’malo mwake anathetsa banjalo pa malo omweo. Malinga ndi yemwe watitumizila nkhaniyi maiyo akukhalira kubindikira nyumba chifukwa cha manyazi koma mwamuna wa nchuunoyo wathawa mderalo. Anthu ambiri mderalo akhumudwa kwambiri ndi zomwe achita maiyo poganizila zakudwala kwa agogo ake.
Akokeledwa ku bwalo la mpingo
Mamembala atatu a mpingo wina ku Mtandire mdera la Njewa m’boma la Lilongwe akokera ku bwalo mpingo wao. Nkhaniyi ikuti chikhazikitsireni mpingowo, wakhala ukulekerela kuti amuna adzikwatila akazi opitilira m’modzi komanso kumwa mowa mwauchidakwa. Pa chifukwachi mamembala amuna ambiri akhala akukwatila akazi awiri ngakhalenso atatu ndikumwa mowa mwauchidakwa poyera. Izi zakhala zisakusangalatsa mamembala ena ambiri amu mpingowo ndipo akhala akusiya kupemphera mu mpingowo zomwe zakhala zikudzetsa mpungwe-pungwe mu mpingowo. Nkhaniyi itafika ku likulu la mpingowo anakhazikitsanso malamulo ena atsopano kuti mchitidweu utheretu ndikulangiza mamembalawo kuti yemwe satsatila lamulo latsopanolo amuchotsa mu mpingo. Ngakhale izi zinali chomwechi mkulu wapa mpingowo,mlembi komanso gulupa wina anamenyetsa nkhwangwa pa mwala ndipo amapitilizabe ndi makhalidwe akumwa mowa mwauchidakwa komanso kusintha akazi ngati Malaya makamaka amu mpingo omwewo. Nkhaniyi itafika ku likulu la mpingowo ayamba achotsa komanso kuimitsa maudindo atumiki a Mulunguwo koma m’malo mwake atumiki Ambuyewo akokera ku bwalo mpingowo pa nkhaniyi. Koma anthu ambiri ati akudabwa ndi zomwe achita anthuwo chifukwa ati m’malo mongopepesa kapena kulapa mchifukwa ninji akukasuma chikhalireni nkhaniyi ndi yauzimu. Anthu amipingo ina adzudzula mpingowo ponena kuti anaziyamba okha chifukwa pamene amakhazikitsa mpingo samayenera kuyenda limodzi ndi satana chikhalireni njira za Mulungu ndi zoyera.
Achenjezedwa za mowa
Tili mboma la Ntche kwa Mfumu Makwangwala, achinyamata ena awalangiza kuti apewe kumwa mowa mwauchidakwa. Malinga ndi amene watitumizila nkhani-yi, nyakwawa kumeneko zinakhalilana pansi zitaona kuti mchitidwe wokumwa mowa pakati pa achinyamata wanyanya m’deralo pomwe ambili akutupikana ndi mowa wa midoli komanso mkalabongo ndipo ena akufa kumene. Imodzi mwa nyakwawayo inalankhula modandaula kuti achinyamata asanu afa m’mudzi mwake mokha chaka chino chifukwa cha mkalabongo. Panopa, nyakwawazo zagwilizana kuti zizikhaulitsa achinyamata omwe azipezeka akumwa mowa mwauchidakwa ndipo awalangiza kuti azilawilira kumunda osati kokamwa bibida .
Mwambo wa maliro usokonekela kamba ka gule wamkulu
Mwambo wa malilo unasokonezeka pamudzi wina kwa Santhe mboma la Kasungu gule wamkulu atayamba kubalalitsa anthu. Nkhaniyi ikuti mkulu wina ometa anamwalila kotelo kuti mwambo onse amayendetsa anali agule wamkulu. Koma gule wina anavina mochititsa kaso ndipo anthu anamufupa. Koma mutalowa gule winanso m’bwalo, anavina kuposa nzake oyamba uja. Pa chifukwa-chi, gule uja anayamba kuchita nsanje kotelo kuti amalowa m’bwalo kumakasokoneza nzake uja sitepe. Kenaka ataona kuti sakuphula kanthu anayamba kukwapula anthu omwe anafika pa siwapo zomwe zinachititsa kuti anthu ayambe kubalalika. Pa chifukwachi, nyakwawa ya m’mudzimo yalamula akulu a dambwe kuti abwere ndi gule wamkuluyo kubwalo komwe akayankhe mlandu onyazitsa mwambo wa malilo. Anthu ambili ati nkutheka kuti guleyo anali ataledzela kamba koti anamupeza ali ndi mowa wa mkalabongo m’manja.