Watitumizila nkhaniyi wati mwamunayo anapita kumunda kukakumba chinangwa koma akuweruka kufika kunyumba anadzidzimuka kupeza mkazi wake ali ndi mphongo ina kunyumbako. Pospya mtima komanso podziwa kuti pamudzipo mpachikamwini mwamunayo anangolongedza katundu wake kumalunjika kwao. Atangokwera galimoto yopita kwawoko mkazi wake anatulukira ndipo mopsya mtima anatola mwala nkumugenda mwamuna wakeyo ku nkhongo ndipo akuti anavulala kwambili. Momwe mayiyo amachita izi nkuti akufuulira mwamunayo kuti ukachoka ana ako akudyetsela ndani. Panopa, mwamunayo amugoneka mchipatala komwe akuti akupezako bwino. Anthu ambili m’deralo adzudzula mayiyo pa nkhaniyi makamaka chifukwa cha nkhanza zomwe anaonetsa kwa mwamuna wakeyo.
Akanyanga mkulu wina ndi zibakera
Anthu am’mudzi wina kwa T/A Mpama mboma la Chiradzulu ayamika anyamata ena omwe aphika mkulu wina ndi zibakera pomwe ati zathandiza kuti mkuluyo asinthe khalidwe lake lomatukwana anthu akaledzera. Watitumizila nkhani-yi wati mkulu wina m’mudzimo akamwa mowa, nthawi zonse amayambila kunja kwa mudzi kulalatila aliyense pa nkhani zosadziwika. Ambili omwe amamudandaula mkuluyo anali amai omwe sali pa banja komanso amuna omwe akhala mbanja kwa nthawi yaitali koma opanda mwana. Patsikulo anyamata ena atatopa ndi khalidwe la mkuluyo anamutchingila pa njila ndikumukutumula mpaka thapsya. M’mawa kutacha mkuluyo anaitanitsa achibale ake pomwe anawafotokozera zoti wasiya khalidwe lake lomwa bibida nkumatukwana anthu osalakwa ndipo anapempha abale akewo kuti akamupepesere kwa mfumu ndi anthu onse m’mudzimo. Pakadali pano mkuluyo akuti wasiya kumwa mowa ndipo mmalo mwake wayamba kulalikira anthu mau a Chauta zomwe zasangalatsa anthu ambili m’mudzimo.
Mayi wina aba ufa wamaliro
Mayi wina kwa T/A Ganya mboma la Ntcheu amuchotsa mu gulu la amayi osonkhetsa thandizo lakumaliro ataba ufa omwe amafuna kuti aphikire adzukulu kumanda. Watitumizila nkhaniyi wati monga momwe zimakhalila m’mudzi mukagwa malilo, amai komanso amuna amagwila ntchito zosiyanasiyana. Tsono pomwe achinyamata amatolela nkhuni, amai ena amasonkhetsa ufa koma zikuonetsa kuti amaiwo anatolela ufa wambili malinga nkuti anthu akolola dzambili chaka chino. Apatu mayiyu anazembetsa beseni lina la ufa kupita nalo ku nyumba kwake ndipo winawo anaphika nsima ya adzukuluwo mpaka ufa winanso kutsala. Tsono chomwe chautsa mapiri pa chigwa nchakuti mwini beseni lomwe anaikamo ufawo analondola kunyumba kwa mayiyu ndipo anakapeza muli ufa wodzaza. Nkhaniyi inakafika kwa akuluakulu a mudzi ndipo anapita kukamulanda ufawo. Pakadali pano mayiyo akuyenda ali wela wela chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.
Abisa nkhata za maliro
Tili mboma lomwelo la Zomba anthu ena awakokela kubwalo atawatulukila kuti anabisa nkhata za malilo. Nkhaniyi ikuti pamudzi wina panagwa malilo ndipo mwambo onse unayamba bwino popanda zopinga mpaka kukafika kumanda. Koma anamfedwa ochokela kutauni omwe anali atagula nkhata zao anakhumudwa kwambili kuona kuti nkhata zomwe anagula sizikuoneka pamene amayala nkhata kumandako. Nkhaniyi ataitula kwa akulu akulu anayamba kufufuza ndipo mai wina anaulula kuti anaona nkhatazo m’nyumba ina. Pamenepa, nthumwi zinapita kunyumbako komwe anakapezadi nkhatazo. Anthu ambili ati akuganiza kuti mwina anthu omwe anabisa nkhatazo amafuna kuchita zizimba apo ayi amafuna kukagulitsa pofuna kukatamuka. Pakadali pano, mwini nyumbayo waulula anzake omwe anachita nawo zaupanduzo ndipo akuyembekezeka kuyankha mlandu ku bwalo la nyakwawa.