Yemwe watumiza nkhaniyi wati masiku apitawa mpingo wina mderalo unakonza mapemphero apadera pofuna kuthandiza anthu ena omwe ndi osowa mu uzimu. Pa mwambowo panafika alendo ochokera mmadera osiyana-soyana kuphatikizapo ochokera mu mzinda wa Blantyre komwe kuli likulu la mpingowo. Ndipo alendowo anali okhutira ndi khwimbi la anthu omwe anafika pamalopo. Koma mwambowo uli nkati, pamalopo panafikanaso mtsikana wina wotha msikhu kuti nayenso apeze zosowa zake zamu uzimu. Ndipo mtsikakanayo anayamba kupemphela mmalilime komanso kugwa ndipemphero. Anthu ambiri omwe anali pamalopo anali okhutira kuti mzimu woyera ukuyenderadi anthu ake pamalopo. Koma mosakhalitsa pamalopo panafikanso mnyamata wina yemwe anangofikira kumenya mbama mtsikanayo. Apo mtsikanayo anayamba kulira mokuwa ndipo anthu ena anayesera kumpulumutsa kwa mnyamata wa upanduyo. Ndipo anthu omwe samawadziwa anthu awiriwo anayamba kuyankhula zonyazitsa mtsikanayo pomuganiza kuti mwina anali woyenda-yenda. Koma mmodzi mwa alendo omwe anafika kuchokera ku dera lina anakokera awiriwo padera ndikufunsa mnyamatayo chifukwa chomwe adapandira mtsikanayo. Apo iye adayankha mmaso muli gwa kuti sakufuna mchemwali wake kulowa mpingo wina wosiyana ndi mpingo wamakolo ake. Izi zinachititsa kuti anthu ena ayambe kumenya mnyamatayo. Koma alendo omwe amayendetsa mapempherowo adapempha kuti asalange mnyamatayo pomumenya kamba kuti mwina adali chida cha satana chomwe chimafuna kusokoneza mwambo wamapempherowo. Pakadali pano anthu mderalo adzudzula mnyamatayo posokoneza mwambo wamapempherowo.
Mtsikana wina alaula mudzi
Mtsikana wina walaulanso mudzi kachwiri kwa mfumu yaikulu Nkanda m’boma la Mulanje. Mtolankhani wathu kumeneko wati mtsikanayu yemwe m'buyomu adapezekanso akugonana ndi mlongo wake wina masiku apitawo wagwidanso ali mchikondi ndi mlongo wake amene wangofika kumene mderalo kuchokera m’boma lina komwe amakagwira ntchito pa estate ina. Ndipo atapeza ndalama zokwanira adaganiza zobwerera kumudzi kuti akamangire makolo ake nyumba. Koma atafika pakhomopo mchemwali wake anatengera mnyamatayo kumalo ena achisanagalalo mderalo ndi cholinga choti adye nao ndalama zomwe mnyamatayo wabweretsa kuntchito kwake. Ndipo onse awiri anayamba kupapila limodzi mpaka mnyamatayo kuledzera. Apo mtsikanayo anatengera mlongo wakeyo kunyumba yake. Koma makolo ao adali odadwa kuona kuti mnyamatayo sanafike pakhomo mpaka pakati pa usiku ndipo adayamba kumufuna-funa. Ali mkati momufuna-funa anthu ena adatsina khutu makolowo kuti adamuona mnyamatayo ali ndi mchemwali wake kumalo ena omwera mowa omwe ali mderalo. Apo makolowo sadachedwe koma kuthamangira kunyumba ya mtsikanayo ndipo adangofikila kulowa popeza kukhomo kunali kosatseka. Makolowo adangogwira pakamwa pomwe adapeza awiriwo ali mtulo tofa nato koma onse ali mbulanda limodzi pa kama. Pakadali pano mudzi wonse watekeseka kamba ka mkhalidwe la mtsikanayo.
Anthu akhala mwa mantha kamba ka malodza
Anthu a m’mudzi wina kwa sub T/A Ndanga m’boma la Phalombe akukhala mwa mantha kamba kamalodza omwe achitika kumeneko. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mderalo muli bambo wina yemwe ngozilimbikira pankhani ya ulimi. mwa zina ali ndi munda waukulu ndipo amakolola dzambiri chaka chili chonse. Kuonjezera apo amasunganso ziweto monga mbuzi, nkhunda, nkhuku komanso abakha. Ndipo pakhomo pake ndipa mwana alilernji. Koma masiku apitawo banjala lakhala lodadwa kambiri imodzi mwa nkhuku zake itatswa mwanapiye wa miyendo inayi. Nkhaniyi yaimisa mitu anthu mderalo kamba izi nkoyamba kuti zichitike kumeneko. Ngakhale eni ake sakuonapo vuto lilonse koma anthu ena ati nkutheka kuti izi ndi zamasilamusi kamba mwini nkhukuzo pakhomo pake sipadutsa galu wakuda. Pakadali pano anthu ena alangiza mwini nkhukuzo kuti aponde-ponde.