You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma17/08/17

17/08/17

Written by  Newsroom

Asiidwa banja kamba kosakhulupilika

Mkulu wina mboma la Salima manja ali ku nkhongo mwamuna wake atamusasa kuti sakumufunanso banja kamba kosakhulupirika.

17
August

Nkhaniyi ikuti mbomali mukuchitika kalembera ndipo anthu ambili akumapita m’mawa pamene ena akumalawira mbandakucha ncholinga choti akabwereko msanga. Patsikuli mayiyo akuti anadzuka cham’ma 1 koloko mbandakucha ati ncholinga choti akakhale oyambirira koma chonsecho akokakomana ndi chibwenzi. Mwatsoka popita kumaloko anasemphanitsa chiphaso cha mavoti nkutenga cha mwamuna wake. Cha m’ma 5 koloko m’mawa naye mwamunayo anadzuka kuti azipita ku geni, koma atayang’ana chiphaso chake sanachipeze ndipo m’malo mwake anapeza chiphaso cha mkazi wakeyo. Apatu anadziwiratu kuti mkazi wakeyo wasemphanitsa mwa ngozi ndipo anamuimbira foni kuti amudziwitse za nkhaniyi koma foniyo siyimapezeka. Kenaka anangoganiza zomulondola ku malo komwe amakalembetsera kaundulayo koma zachisoni anapeza mkazi wakeyo kulibe. Apatu mkuluyo anayamba kumusakasaka ngati nkhuku ndipo anakumanizana naye pa njira. Atamufunsa komwe anali anangoti kukamwa yasaa kusowa chonena. Popsya mtima mkuluyo anangopita ku nyumba nkukamutulutsira katundu wake nkumuuza kuti azipita kwawo. Pakadali pano mayiyo ali kwawo koma manja ali ku nkhongo kusowa mtengo ogwira.

 


Chindeu chibuka pakati pa amuna awiri 
Chindeu cha mtima bii chinabuka pakati pa amuna awiri ku Chingale mboma la Zomba. Nkhaniyi ikuti mwamuna wina m’deralo anachita ngozi ya njinga yakapalasa ndipo anthu achifundo anamutengera ku chipatala komwe anakamugoneka kwa nthawi yochepa. Mwa mwayi kuchipatalako anatuluka tsiku lomwelo koma anakhumudwa atakafika ku nyumba kupeza mkazi wake kulibe. Ndiye poti wakhala akumumvera mbili mkazi wakeyo kuti ali ndi chibwenzi , mwamunayo analondola kwa mwamuna yemwe amamuganizirayo ndipo anakamupezadi mkazi wakeyo kumeneko. Apatu chindeu chinabuka pakati pa amuna awiriwo koma mwa mwayi mwamuna wakubayo anapulumuka nkuthawa. Mwamunayo atatsala anapanilira mkazi wakeyo ndipo kenaka anamukwekweza mpaka kukafika naye kunyumba. Atakambirana mkuluyo analongedza katundu wake nkuona msana wa njira koma chomvetsa chisoni nchoti atapita kwawoko anakamubweza kuti abwelerenso kwa mkazi wakeyo. Pakadali pano mwamunayo wagwira njakata chifukwa atabwelera kwa mkaziyo anakapeza kuti wabweleranso kwa chibwenzi chakecho. Anthu ambili adzudzula achibale a mwamunayo kuti sakumufunira waoyo zabwino pomukankhizira kwa mkazi wa makhalidwe woipa chomwecho.

 

Chidakwa chiseketsa anthu
Chidakwa china mdera la Makwangwala m’boma la Ntcheu chinaseketsa anthu. Nkhaniyi ikuti mwamunayo anakwatila zaka zitatu zapitazo ndipo wakhala ali pa chikamwini mderalo. Koma vuto la mwamunayo ndi mlesi otheratu ndipo samagwira ntchito iliyonse yothandiza banja lake koma m’malo mwake amakhalira kupapila mowa. Pa chifukwachi mkazi pamodzi ndi makolo ake anayamba kuloza chala mkamwiniyo pomuuza kuti sakuwathandiza ndipo akhala akumuuza kuti achoke pakhomopo mpakana kumulamula kuti akakhale mkagowelo. Apa banjapo atatopa ndi khalidwe la mkamwiniyo anapangana zomukhaulitsa ncholinga choti achoke yekha pakhomopo. Mphuno salota mwamunayo anakautunga mowa mpakana mbandakucha. Ali mtulo anthuwo anayamba kusasula kagoweroko ndipo kumapeto kwake anamuthila madzi kuti mwina angaone nsana wanjira. Koma choseketsa mwamunayo wamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sachoka ndipo anthu omwe anafika chaku m’mawa pa nyumbapo anaseka chikhakhali podabwa ndi zochita za mwamunayo. Pakadali pano apa banjapo athedwa nzeru chifukwa kwa iwo ayesetsa njira zonse zopitikitsila mwamunayo koma zikulephereka.

 

Anthu ayima mitu ndi zomwe zamuonekela mkulu wina ku Mulanje
Anthu a m’mudzi wina kwa Mfumu Juma mboma la Mulanje ayima mitu ndi zomwe zamuchitikira mkulu wina kumeneko. Nkhaniyi ikuti m’mudzimo munali mwambo wolambula ku manda. Monga mwa mwambo anthu amakonza zakudya zosiyanasiyana kuti akatha kugwira ntchitoyo akaone kadaunda madzi. Tsono mkuluyo akuti anapha nkhuku ndipo anthu anadyera nsima nkutha yonse mu mphika. Koma chomwe chadabwitsa anthu pamudzipo nchoti madzulo nkhuku zikulowa, kunapezeka kuti nkhuku yomwe anayipha ija inatulukira nkulowanso m’nkholamo. Mkuluyo ataona izi anadodoma kwambili ndipo anaitana anthu kuti akaone za malodzazo. Anthuwo atafika anangogwira pakamwa koma ali jenkha chomwecho, kunatulukira mkulu wina wa m’mudzi momwemo yemwe anadzamuuza mkuluyo kuti nkhukuyo ndi yake yomwe idasowa kalekale. Posafuna kulimbana naye, mkuluyo anamulola nzakeyo kutenga nkhukuyo koma atagwidwa ndi mantha aakulu. Pakadali pano anthu ambili m’mudzimo ati akukhulupilira kuti zimenezi nzamasilamusi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter