Koma vuto la mwamunayo ndi mlesi otheratu ndipo samagwira ntchito iliyonse yothandiza banja lake koma m’malo mwake amakhalira kupapila mowa ngati mawa kulibe. Pa chifukwachi mkazi wa chidakwacho pamodzi ndi makolo ake anayamba kuloza chala mkamwiniyo pomuuza kuti sakuwathandiza ndipo akhala akumuuza kuti achoke pakhomopo mpakana kumulamula kuti akakhale mkagowelo. Mkamwiniyo m’malo mwake amaponyera ku nkhongo malangizowo. Apa banjapo atatopa ndi khalidwe la mkamwiniyo sabata latha anapangana zokhaulitsila mkamwiniyo mcholinga choti achoke yekha pakhomopo. Mphuno salota mwamunayo anakautunga mowa mpakana mbandakucha nkufikira kudziponya ngati chipika mgoweloyo. Ali mtulo anthuwo anayamba kusasula nyumba yonse yomwe amagonayo ndipo kumapeto kwake kumuthila madzi kuti mwina angaone nsana wanjira. Koma choseketsa mwamunayo wamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sachoka ndipo anthu omwe anafika chaku m’mawa pa nyumbapo anaseka chikhakhali podabwa ndi zochita za mwamunayo. Pakadali pano apa banjapo nzeru zawathera chifukwa kwa iwo ayesetsa njira zonse zopitikitsila mwamunayo.
Mai wina achimina ku Machinjiri
Mai wina otchuka ndi nkhani zolalatila anthu ku Machinjiri m’boma la Blantyre wachimina. Malingana ndi yemwe watitumizila nkhaniyi wati maiyo amaopedwa kwambiri chifukwa cha nkhani zolalata. Mwa zina maiyo amakonda kuyambana ndi anthu pa zifukwa zosadziwika. Dzulu-dzulo laliwisili maiyo anayambana ndi atsikana ena omwe amadutsa pakhomo pake powadzudzula kuti akufuna mwamuna wake. Pa chifukwachi atsikanawo omwe anali anai anayamba kulalatila maiyo pogwiritsa ntchito nyimbo komanso mpakana kuchita kukhala pakhonde pa maiyo ndipo zinachitika kwa ola yathunthu nthawi ya nkhomaliro. Pamene izi zimachitika mwamuna wa maiyo anali ali ku ntchito ndipo anthu oyandikana nawo anakhala kumbuyo kwa atsikanawo kuti amukhaulitse maiyo. Maiyo zinamukoka manja mpakana kulephera kutuluka mnyumba mpakana ana ake omwe anapita kosewera kulephera kulowa mnyumba. Anthu ena akufuna kwabwino ndi omwe ananyengerela atsikanawo kuti achoke pakhomopo koma analonjeza kuti athana naye maiyo kulikonse atakumane naye. Mwamuna wa maiyo wachenjeza maiyo kuti akapitilira ndi khalidwe lakelo amupitikitsa pa banja. Pakadali pano maiyo akukhalira kutandala mnyumba chifukwa cha manyazi.
Ndeu yosaletsetsa ibuka pakati azimayi awiri
Ndeu yopanda oleletsa inabuka mdera la Kamenyagwaza m’boma la Dedza pakati pa amai awiri a ponda apa nane mpondepo. Nkhaniyi ikuti amaiwo akhala ali pa chimzache kuyambila chitsikana chao. Chosangalatsa china mchakuti amaiwo anakwatiwanso malo oyandikana mderalo ndipo ubale wa mabanja awiriwo wakhala uli osililitsa kwambiri kwa anthu ozungulira mabanjawo. Zaka zapitazo mwamuna wa banja linalo anadwala ndipo matenda atafika pothiphwa anamwalira. Pa chifukwachi mwamuna wa banja lina lija anayamba kudyerela maso kwa maiyo ndipo ubwenzi wa ntseri unafumbila pakati pao. Paja pali mau oti palibe chinsinsi pakati pa thambo, mai mzake uja anazindikira za ubwenziwo ndipo pa chifukwachi anamema anthu ena kuti ayambe kutsatila za ubwenziwo. Tsiku lina anthu omwe anapatsidwa ntchitoyo anapezerela mwamunayo ndi maiyo ali pa tchire ali buno bwamuswe. Apa kunali kumenya kolapitsa uku akuitana mai wina uja pa lamya nkudzaonerela zakumenyedwa kwa mwamuna wake komanso mzakeyo. Apa anthuwo analira ngati kwachitika maliro ndipo anapempha kuti awasiye koma sizinamveke. Anthu ambiri ati ubwenziwo unayambika chifukwa choti maiyo amakopeka ndi ndalama zomwe mwamunayo amapeza akagulitsa mowa wa mkarabongo ndipo banja la mwamunayo latha.
Ntchito itha kamba ka chibwana
Kondakitara wina ndi dalaivala wake omwe amayenda pakati pa Ndilande ndi Limbe mu mzinda wa Blantyre manja ali nkhongo ntchito itawathera chifukwa cha chibwana. Nkhaniyi ikuti anthuwo ananyamula anthu kuchokera ku Limbe kupita ku Ndirande koma njira yonseyo anthu akhala akuwadzudzula kuti samayenda bwino ponena kuti amathamangitsa kwambiri galimotolo. Koma m’malo mwake kondakitalayo anayamba kuchemerela mzakeyo zomwe zinakwiitsa anthu omwe anakwera basiyo. Pa chifukwachi atafika pa B&C anthuwo anapempha kuti awatsitse koma m’malo mwake dalaivala ndi kondakitarayo anauza anthuwo kuti akuwanyansa ndipo anawauzanso kuti akapitiliza kuwavutitsa akafikira kuwaomba makofi pa siteji yapa msika. Basi itafika pa sitejipo anthuwo anaona ngati zamalodza chifukwa dalaivala ndi kondakitalayo anayambadi kumenya m’modzimodzi ndipo apa ndeu yafumbi inabuka mpakana anthu awiriwo anamenyedwa mpakana kukodzedwa . Chipwilikiti chikupitilira anthu ena anakolopola ndalama zonse zomwe zinali ndi anyamata osimbwawo ndikuwasiya opanda kanthu. Apa amuna awiriwo m’malo molira chifukwa cha ululu anayamba kulilira ndalamazo. Pakadali pano mwini galimotolo wachotsa anthuwo ntchito ndipo awauza kuti ngakhale malipilo awo a mwezi uno sawapatsa chifukwa akaumilira akawasiya manja mwa apolisi. Amunawo akukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi komanso poganizila za mabanja awo.