You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma15/08/17

15/08/17

Written by  Newsroom

Amai ena akhumudwisa mpingo

Amai ena apa mpingo wina m’dera la Mayaka m’boma la Zomba akhumudwitsa mamembala apa mpingowo.

15
August

Nkhaniyi ikuti mderalo m’modzi mwa mamembala apa mpingopo anadwala ndipo matenda atakula anatsamila mkono. Zonse zokonzekera kuika maliro zinachitika ndipo thupilo analitengera kwao kwa malemuyo ku Monk-bay m’boma la Mangochi. Anthu ambiri anaperekeza zovutazo kuphatikizapo amai koma chodabwitsa mchakuti nthawi ya chakudya itakwana kumudziko, amai ena awiri anakanitsitsa kudya pa gulu zomwe zinadabwitsa mamembala enawo. Pofufuza za nkhaniyi zinadziwika kuti ati amaiwo satha kudya pagulu pa zifukwa zodziwa okha. Apa anthu ambiri omwe anaperekeza malirowo anali okhumudwa koma m’malo mwake amaiwo anakagula zakudya zao ku malo ena odyera anthu apaulendo omwe ndi oyandikana ndi pa siwapo. Atafika kuchokera kumaloko nkhani inali yao koma sizimawakhudza chifukwa mwa zina anakanitsitsa ngakhale kuyandikana ndi amzaowo. Chinanso chodandaulitsa pa ulendowo mchakuti pamene mamembalawo amabwerela kuchokera ku Mangochi-ko mai winanso anayamba kulalatila mkazi wa gulupa wina mpakana ndeu ya fumbi inabuka pakati pao zomwe zinapangitsa kuti akuluakulu a mpingowo omwe anali nawo pa ulendowo ayambe kupemphera malirime mcholinga choti Mzimu wa Ambuye udzetse bata pakati pa anthuwo. Koma anthu ena omwe sanali a gululo samalabadila za mapempherowo. Pamene timalandila nkhaniyi amai atatu onsewo awakokera ku bwalo la mpingo chifukwa chonyazitsa komanso kuonetsa khalidwe loipa zomwe sizigwirizana ndi malamulo a mpingowo.

 

Mwambo wa maliro usokonekela ku Neno

Mwambo wa maliro unasokonezeka kwa ola lathunthu mdera la Kanduku mboma la Neno. Nkhaniyi ikuti munthu wina wakhala akudwala mderalo ndipo matenda atafika pothiphwa anamwalira. Akubanja anakadziwitsa nyakwawa ya mderalo za zovutazo ndipo nyakwawayo nayo inachita chimodzimodzi polengeza za malirowo. Tsiku loika maliro litakwana anthu ambiri anasonkhana mwaunyinji kuphatikizapo ampingo potsatila ntchito zabwino za malemuyo ngakhale anali ochokera mdera lina. Pa nthawi yazolankhulalankhura, anafedwa anadzudzula nyakwawayo kuti sinawalore kuti m’bale waoyo akagone kumudzi kwao monga momwe akubanjawo anakonzera. Nyakwawayo inalamula kuti malirowo aikidwe m’mudzimo chifukwa mwa zina malemuyo amamutenga ngati mbabdwa. Pa chifukwachi nyakwawayo inangochoka pa siwapo anafedwa ali mkati kulankhula zomwe zinapangitsa kuti mwambo wa maliro usokonezeke ndikuchedwa ndi ola la thunthu. A mpingo komanso mikoko yogona kuphatikiza anafedwa atakambilana anagwirizana kuti mwambowo upitilire ngakhale panalibe yemwe anayankhula m’malo mwa nyakwawa. Pakadali pano anthu mderalo adzudzula mbali zonse chifukwa mwa zina anafedwa analakwitsa poyankhulira pagulu nkhaniyi pamene nyakwawayo nayo inalakwitsa ponyanyala malirowo.

Nyamata wina asowa mosadzika bwino
Anthu a mdera la Namadzi m’boma la Zomba akukhala mwa mantha ndi kusowa kosadziwika bwino kwa mnyamata wina. Nkhaniyi ikuti mnyamatayo zaka zapitazo anapita ku Joni kogwira ntchito ndipo anasiya banja lake mbuyo. Ali ku Joni-ko mkazi wake wakhala akuvutitsa pimba terefoni komanso kulemba kalata kuti mwamunayo abwerere chifukwa choti ati anali ndi chifundo kuti amuone. Izi zitachita kwa nthawi yayitali mwamunayo anabwereladi kuno kumudzi ndipo tsiku lofika anakafikira kuchipongozi. Koma zodabwitsa makolo a mkaziyo sanamulandile mpakono pomwe mkamwiniyo chifukwa mwa zina mai wa mkazi wakeyo wakhala akulangiza mwana waoyo kuti asakwatiwe ndi mwamunayo. Maiyo ataona kuti mkamwiniyo akuumilira pakhomopo anakamusumila ku bwealo kuti akufuna kuchita chipongwe mwana waoyo pomuzembetsa. Nkhaniyi inakafika mpakana ku polisi ndipo mwamunayo wakhala akuyendera mlanduwo. Ku bwalo la milandi mlanduwo unamukomera mwamunayo zomwe ena akukhulupilira kuti ndi zimene zinachititsa kuti asowe mosadziwika bwino. Anthu ambiri mderalo akuloza chala kubanja la mkazi wake kuti nkutheka kuti anamuchitila zamatsenga.

Nyakwawa ayikokera kubwalo
Nyakwawa ina ayikokera ku bwalo la mfumu mdera la Madisi ku Dowa chifukwa choikira kumbuyo zidakwa zina za mderalo. Nkhaniyi ikuti achinyamata ambiri mderalo awirikiza kumwa mowa wachilendo monga wa mkarabonga komanso midoli koma chodandaulitsa kukachitika Maliro achinyamatawo salabadila za zovutazo. Izi zakhala zikukhumudwitsa anthu ambiri mderalo kuphatikizapo mikoko yogona komanso anafedwa. Nkhani zakhala zikupita kwa nyakwawa, koma zimaonetsa kuti salabadila chifukwa mwa zina nyakwawayo nayo ndi yimodzi mwa zidakwazo. Dzanadzana laliwisili mwana wina anadwala mwadzidzidzi mpakana kumwalira. Chodabwitsa bambo wa malemuyo anakhotera kopapila mkarabongo pamene amachokera kumanda zomwe zinadabwitsa komanso kuchititsa mantha anthu ambiri omwe anasonkhana pa maliropo. Kunyumba ya siwa pa nthawi yolonjera anthu ochokera kumanda anthu anagwira pakamwa atazindikira kuti nafedwayo palibe ndipo anthu ena sanabise mau pouza anthuwo kuti mwamunayo wakhotera komwa bibida. Mwamunayo atamukokera ku bwalo anthu anagwira pakamwa nyakwawa italankhula m’maso muli gwa pa bwalolo, kuti palibe mlandu chifukwa sizikuwakhudza. Apa mikoko yogona komanso anthu ena akokera ku bwalo nyakwawayo kuti akafotokoze bwino pa nkhaniyi. Pakadali pano sizikudziwika kuti nkhaniyi yatha bwanji.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter