Chomwe chinachitika nchoti mwamuna wina anayambana ndi mkazi wake mpaka kuundana m’dothi. Mchemwali wake wa mkaziyo ataona kuti mbale wake avulala, anapita kukamulanditsa koma akadadziwa sakadachita chifukwa mlamu wakeyo anayambanso kumuthibula mosaopa kuti ndi mkazi wa mwini. Anyamata ena ataona izi analowererapo nkulanditsa ndeuyo koma m’nenemo nkuti mwamunayo akutukwana anthuwo koopsya mophatikiza ndi mfumu yomwe ya m’mudzimo. Pamenepa eni mbumba alamula mkamwiniyo kuti achoke pamudzipo ndipo achenjezanso mkamwini wina yemwe ali ndi khalidwe lotukwana anthu apamudzipo kuti alekeretu chifukwa akapitiliza nayenso adzamuthamangitsa pamudzipo. Pakadali pano sizikudziwika ngati mkamwiniyo wapitadi kwawoko koma anthu omwe akumudziwa bwino mkuluyo akuti ndi khalidwe lake lomamenyana ndi mkazi wakeyo komanso kutukwana anthu onse pamudzipo.
Apasula banja kamba ka banki nkhonde
Tili ku Machinijiri komweko mayi wina wapasula banja ndi manja ake chifukwa chosamvera malangizo a mwamuna wake yemwe anamupempha kuti asalowe m’mavillage banki ambilimbili chifukwa choti akakongola ndalama akumakanika kubweza mpaka kumalanditsa katundu. Yemwe watumiza nkhaniyi wati m’deralo muli magulu a banki nkhonde ochuluka ndipo mayiyo analowa m’magulu angapo ati ncholinga choti asamavutike akafuna kukongola ndalama. Masiku apitawa mayiyo analanditsa katundu wam’nyumba atalephera kubweza ngongole ku gulu lina ndipo pachifukwachi mwamuna wake anamulangiza kuti akhale membala wa gulu limodzi lokha. Apa mayiyo anavomera ngati wamva koma chonsecho akuzembera mwamuna wakeyo kukalowanso m’magulu ena komwe anakatengako ngongole. Tsono pano mwamunayo watulukira zimenezi ndipo poopa kuti amulandanso katundu wangosamuka panyumbapo nkukapanga lendi kwina kusiya mayiyo manja ali mkhosi. Panopa sizikudziwika ngati kuli kutha kwa banja koma akuti mayiyo zamukoka manja chifukwa sakuchita bizinesi iliyonse ndipo anzake akungomuseka.
Apenga kamba kofuna kukhwima
Anthu a m’mudzi wina kwa mfumu Msakambewa mboma la Dowa akuganizira mkulu wina kuti wapenga chifukwa chofuna kukhwimira bizinesi yake yogulitsa mbeu zosiyanasiyana. Nkhaniyi ikuti m’deralo muli mkulu wina yemwe anayamba bizinesi pakanthawi koma samatukuka. Pachifukwachi anapita kwa sing’anga wina kukafuna mankhwala woti zinthu zizimuyendera. Kumeneko sing’angayo anamuuza kuti ngati akufuna kulemera, chizimba chake nchoti akagone ndi mchemwali wake wa bere limodzi. Podziwa kuti mchemwali wakeyo sangalole zamalodzazo, anapempha ng’angayo kuti imusinthire chizimbacho koma sing’angayo anakana ponena kuti akanena wanena. Apa mkuluyo ananyamuka kupita kumudzi ndipo akuti anatha sabata asanamuuze mchemwali wakeyo za chikonzerocho poopa kuti amusambwadza. Kenaka mkuluyo analembera kalata mchemwali wakeyo kumufotokozera za nkhaniyi koma zinali zamanyazi ndi zomvetsa chisoni mchemwali wakeyo atayima pachulu nkuyamba kulalatira mchimwene wakeyo. Apatu mkuluyo anangodziwiratu kuti yalakwa ndipo kuyambira pa tsikulo mutu wake wasokonekera moti sakupitanso ku bizinesi yakeyo chifukwa choti wayamba kudwala matenda a misala.