You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma11/06/15

11/06/15

Written by  Newsroom

Chithumwa chigwa nchiuno
Mpondamatiki wina kwa M’nyanja m’boma la Kasungu akukhalira kubindikira m’nyumba chifukwa cha manyazi chithumwa cha bizinesi yake chitavuka mchuuno.

11
June

Nkhaniyi ikuti bamboyo anapita nawo ku msonkhano womwe a mfumu a mderalo anaitanitsa wokhudzana ndi kulembetsa mayina wofuna kulandila zithandizo zina. Mkuluyo ndi yemwe amathandizila amfumuwo ndipo anayima kutsogolo kwa anthu ndikuyamba kuwafotokozera za cholinga cha msonkhanowo. Mwa tsoka ali mkati kulongosola anagwetsa chithumwa kuchokera mchuuno ndipo mkuluyo zinamukoka manja, mpaka analephera kupitiliza kulankhula ndipo anachoka pa malopo chothawa chifukwa cha manyazi koma atapana chinthu chakecho. Pakadali pano akukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi.

 

 

Banja lina liyenda mwamanyazi ku Kasungu
Banja lina lodziwika bwino pa nkhani zotamanda Chauta mdera la Nsamala m’boma la Balaka ikuyenda ngati nkhuku yonyowa, anthu mderalo atazindikira kuti amasekerera mwana wao wa mamuna kuchita chibwenzi chikhalireni mpingo wao sulora konse mitala. Nkhaniyi ikuti mwana wa mamuna wa pakhomopo ndiwokwatira ndipo amakhala ndi banja lake pa mudzi wina woyandikana nawo, koma chodabwitsa nchakuti anayambanso kuzemberana ndi mkazi wina yemwenso ndiwokwatiwa. Chibwenzicho chitafumbira mpakana kumakafika kwa makolo akewo chikhalireni ali ndi banja lake. Tsiku lina mayi wopanda manyaziyo anapita kwa makolo a mnyamatayo kukacheza, koma anthu ena ofunila zabwino mkazi weniweni wa mnyamatayo anakatsina khutu nzawoyo za nkhaniyi ndipo iye pamodzi ndi nzakewo analiyatsa liwiro ndipo anakapeza kuti mayiyo akucheza ndi makolo a mnyamatayo. Apa ndeu yafumbi inabuka ndipo mayi wokubayo anathidzimulidwa kodetsa nkhawa mpaka milomo yonse kutupa. Posakhalitsa mnyamata ujanso anatulukira pa khomopo ndipo amati adzileletsa ndeuyo koma naye anathidzimulidwa kwa chakwanu leka mpaka anasowa mosadziwika bwino. Pakadali pano mwini mamunayo wanenetsa kuti banjalo sakulifunanso ndipo wapita kwao, koma anthu mderalo akudzudzula kwambiri makolo a mnyamatayo kuti ndi anthu amene amakolezera kuti zimenezi zichititike poganizilanso kuti ndi anthu omwe amasunga malamulo a Mulungu odana ndi chigololo. Mkazi wachimasomasoyo nayense akulirira ku utsi kamba koti mmwamuna wake nayenso wathetsa banja.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter