Bamboyo yemwe kwao kwenikweni ndiku Mpherembe mboma la Mzimba wati akuda nkhawa ndipo akulingalira zobwerela kumudzi. Mkuluyo ndi m’modzi mwa anthu omwe akhala akulimbikitsa nkhani zachitetezo m’deralo ndipo anthu akhala akumuyamikira pa ntchito yake yachitetezo. Masiku apitawa mkuluyo anakwanitsa kugwira mbala zinayi zomwe zakhala zikusautsa anthu mderalo powabera zinthu zao. Anthu m’deralo apempha mikoko yogona komanso Mafumu a m’deralo kuti achitepo kanthu pa nkhaniyi polingalira kuti mkuluyo akabwerera kwao ku Mzimba m’deralo umbava uchuluka.
Mbusa wamalilime amulipilitsa chindapusa
Mbusa wa mpingo wina wotchuka ndikulankhula malirime kwa Kasiya mdera la Khongoni m’boma la Lilongwe amulipilitsa chindapusa cha ndalama zokwana 12-thousand kwacha chifukwa chopeputsa maliro a weni. Nkhaniyi ikuti Mbusayo ataitanidwa ku mwambo wa maliroko kuti akatsogolere zochitika pa maliropo, ananenetsa kuti mkotheka kulankhulana ndi Mulungu kuti munthuyo auke kwa akufa . Munthu wa Mulunguyo anauza anthu onse omwe anakomana ku siwako kuti asapite nsanga ndi thupi la munthu wakufayo ku manda ati ponena kuti ayambe apemphera kuti malemuyo auke kwa akufa . Anthu sanakane zomwe ananenazo, koma m’malo mwake anapemphera kwa nthawi yayitali koma sizinatheke mpaka anthu pa siwapo anatopa ndipo anayamba kung’ung’udza. China chimene chinadandaulitsa anthu pa khomopo mchakuti anayamba kutong’ola maso a thupi la Malemuyo uku akupemphera akulira kuti Mzimu woyera moto mobwerezabwereza. Pakadali pano Mfumu ya m’mudzimo yathamangitsa Mbusayo kuti asamukire mdera lina ndipo munthu wa Chautayo sakupezekanso mderalo.