You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma20/06/17

20/06/17

Written by  Newsroom

M'busa agwidwa akusamba usiku panja
Mbusa wampingo wina kwa Mgona A ku Kanengo mu mzinda wa Lilongwe akuyenda mogwetsa nkhope yake pansi chifukwa cha manyazi atamutulukila kuti amasamba usiku uli onse 10 –kokolo kwinaku akuzungulila nyumba.

20
June

Watitumizila nkhaniyi wati mbusayo poyamba adamuimitsa kuti asaimenso ku gome atamutulukila kuti anali pa chibwenzi ndi mai wina mu mpingo womwe amatumikila. Chibwenzi chao chitafumbila awiliwo adawapeza ali mchikondi mchimbudzi china pa kachisipo. Pa chifukwachi anthu ambili anadomoka mu mpingowo kukalowa mpingo wina. Koma masiku apitawa mbusayo anamuitanitsa kuti akayambe kutumikilanso pa mpingowo zomwe anthu ena sizinawasangalatse. Kenaka, zamveka kuti mbusayo anapita kwa sing’anga wina komwe anakapeza mankhwala omwe amasamba usiku uli onse kuti ati azikhala ndi chikoka mpaka amai ena anamupezelela akuzungulila nyumba kwinaku akumadzithila madzi. Pakadali pano, mbusayo akumayenda ali zoli zoli ngati napiye ogwela mvuwo.

 

Apasalu banja ndi manja awo

Anthu apa mudzi wa Konyolo kwa Kachere m’boma la Dedza akuseka mai wina wapa banja yemwe wapasula banja lake ndi manja. Nkhaniyi ikuti mkaziyo amakhala bwino lomwe pa banja ndi mwamuna wake popanda chovuta. Ngakhale kuti mwamunayo yemwe kwao ndiku Mitundu m’boma la Lilongwe analolera kukhala ku chikamwini ku mudzi kwa mkazi wakeyo malinga ndi chikondi. Masiku apitawa mwamunayo anawambala chimanga chokwana 2-kilogrammes chomwe anakagulitsa wosauza mkazi wakeyo ndi cholinga choti akonzetsere njinga yake yakapalasa. Mkaziyo atamva za nkhaniyi anapsya mtima mopyola muyezo kotero kuti mwamunayo atalowa m’nyumba anakhomera momwemo mpaka usiku. Mwamunayo anaimbira foni mlamu wake yemwe ndi mkulu wake wa mkazi wakeyo ndi kumufotokozera nkhani yonse. Mlamu wakeyo anakalanda makiyi kwa m’ngono wakeyo ndikutsekulira mwamunayo. Pakadalipano mwamunayo waola katunndu wake ndi kuona msana wa njira kutanthauza kutha kwa banja. Anthu ambiri pa mudzipo akumuseka mkaziyo kamba kopasula banja ndi manja ake.

 

Azimayi apamitala akunthana

Amai aiwiri apamitala anapindalana ndewu mkamwa pa sitolo za Kamboni mdera la Kawamba m’boma la Kasungu. Nkhaniyi ikuti tsabata yatha amaiwo adakomana pa malo pomwe mwamuna wao amachita malonda a golosale. Anayamba kufika pamalopo anali mkazi woyamba. Ndipo ali pamalopo analowa m’golosalemo mkumagulitsa katundu mwamuna wake akucheza bawo ndi anzake pafupi ndi pamalopo. Posakhalitsa mkazi wachiwiri nayenso anafika pamalopo koma anali okwiya kuona mkazi mzake akugulitsa m’golosalemo mutsutsana ndi lamulo lomwe mwamuna wao anapereka loti amai-wo sayenela kugulitsa katundu ati pofuna kupewa mkangano pakati pao. Mkazi wachiwiriyo anaona ngati mwamunayo amakondera mkazi woyambayo. Apo mkazi wachiwiriyo nayenso analowa m’golosalemo. Ndipo anayamba kuyalula katundu kwinaku akuponya katunduyo mu thumba la chiguduli lomwe anabweretsa pamalopo. Mkazi wamkulu nayenso sanachedwe ndipo anayala chitenje chomwe anavala ndikumba kutsosola katundu mu alumale ya golosaleyo. Izi zinakwiitsa mkazi wachiwiriyo ndipo amai awiriwo anayamba kuthirana makofi. Momwe zimachitika izi anathu amangonelera osawaleretsa. Pakadali pano, amai onse awiri achoka pakhomopo ndipo mwamunayo akuyenda khuma khuma popeza golosaleyo yake yasatsuka.

 

Maphunziro asokonekela pa sukulu ina

Maphunziro anasokonekera pasukulu ina kwa Nkando kwa Gulupu Kalilima m’boma la Mulanje. Nkhaniyi ikuti mderalo muli banmbo wina yemwe amachita malonda pa msika wa Nkando. Ngakhale mwamunayo zake zimayenda bwino iye amakaikila mkazi wake kuti akumudyetsa njomba. Mwa zina mkaziyo wakhala akubisa lamya yake ya mmanja moti akafuna kuimba mkaziyo amapita kuchimbuzi kapena kubafa komanso kutali ndi nyumba yake ati pofuna kuti mwamuna wake asadziwe zomwe akukamba. Mwamunayo atafunsa mkazi wake za foni mkaziyo amakna kuti alibe foni popeza iye safuna kusokoneza banja lake pomayankhula pa foniyo. Koma mwamuna sanakhutire ndi mayankho amkaziyo pankhani yokhuza foniyo. Ndipo tsiku lina mwamunayo anabisalira mkaziyo pasukulu ina mderalo pomwe mkaziyo amachita malonda ogulitsa zakudya za wana. Ndipo apo mkaziyo mosadziwa anatulutsa foni yake kumaonetsa mai wina mauthenga a pafoni omwe wakhala akulandira kuchokera kwa chibwenzi chake. Mwadzidzidzi mwamunayo anafika pamalopo kuti alande foniyo. Apo panaterera kamba mkaziyo sanalore kuti mwamunayo atenge foni ati pofuna kuteteza misika yake. Banjalo linayamba kugubuduzana pafumbi mpaka onse kukhala ali mbu! Ngati ogaitsa mchigayo polimbilana foniyo. Panthawi nkuti ana asukulu kuphatikiza ana a banjalo anatuluka mkalasi kudzachemelera awiriwo. Pakadali pano banjalo laweyedzeka.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter