Nkhaniyi ikuti pamudzipo panagwa zovuta kotero kuti mkazi wa mbiyang’ambeyo pamodzi ndi amai ena anakhamukira ku zovutazo komwe anakakuta anamfedwa. Koma mbiyang’ambeyo itapotoloka ku nyumba kuchokera ku bibida ndikupeza kuti mkazi wake palibe pakhomo anafunsa ana omwe anafotokozera atate awo kuti maiyo awo apita kukakhala nawo pa zovuta pa mudzipo. Koma mwamunayo kamba kakudakwa analunjika ku nyumba ya siwayo ndikukagwira pa dzanja mkazi wake ndikumududuluzira ku nyumba uku akulalata kuti bwanjia sanamuphikire chakudya . Mikoko yogona komanso nduna za nyakwawa zomwe zinali pa siwapo pa nthawiyo zinatuma anyamata a dzitho omwe anagwira mbiyang’ambeyo ndikuimangilira ku mtengo kufikira mwambo wonse wa zovuta utatha. Pa nthawiyo mkazi anafotokozera anthuwo kuti ku nyumbako kunalibe chirichonse choti akanaphikira mwamuna wakeyo chifukwa ndalama zonse zomwe anagulitsa geni yake wakamwera mowa. Mwambo wa zovutazo utatha mbiyang’ambeyo anaimasula ku mtengo ndikududuluzira kwa nyakwawa komwe anailamula kulipira mbuzi imodzi komanso nkhuku zitatu.
Mkazi wina amumvera chisoni kamba kosintha amuna mowilikiza
Anthu apa mudzi wina kwa Siliya m’boma la Balaka akumvera chisoni mai wina wapa banja yemwe wawirikiza mchitidwe wosintha amuna monga malaya wosaganizira momwe kunjaku kuliri malinga ndi kachirombo ka HIV koyambitsa matenda a AIDS. Nkhaniyi ikuti mwamuna wa maiyo anapeza ntchito ku bungwe lina ku Lilongwe. Ndipo mwamunayo anatsazika mkazi wake kuti akukakonza malo ku Lilongweko kuti adzatenge mkazi wakeyo. Koma mwamunayo atangochoka kupita ku ntchitoko mkaziyo anatasa , kotero kuti anapalana ubwenzi wa nseri ndi amuna awiri omwe samadziwana. Koma achibale a mwamunayo atatulukira za njomba zomwe mkaziyo amadyetsa mwamuna wake sanachitire mwina koma kudziwitsa mbale waoyo za nkhaniyi. Mwamuna wakeyo wanenetsa kuti apeza mkazi wina wokhulupirika woti amange naye banja, ndipo wauza mkazi wakeyo kuti apitirize ndi zibwenzi zakezo. Pakadalipano mkaziyo wagwira njakati.
Mamisala wamkazi akakamila dalaivala wa minibus
Dalaivala wina wa mini bus ku Kamuzu Road m’boma la Salima anaona ngati malodza wamisala wina wa mkazi atamukakamira kuti akumufuna akhale naye pa ubwenzi. Watitumizira nkhaniyi wati dalaivalayo atafika ku depo ya bus m’deralo anatsika m’minibusimo podikira kuti nthawi ikwane kuti apotoloke kubwelera komwe amachokera. Koma dalaivalayo akutsika minibus-yo anakomanizana ndi wamisala wachikazi yemwe anampempha ndalama ataona kuti dalaivalayo sakuyankha zogwira mtima wamisalayo anauza dalaivalayo kuti akumufuna akhale bwenzi lake ndipo amamulondola kuli konse amapita. Zimenezi zinachititsa dalaivalayo kuzungulira mini bus yakeyo kangapo uku wamisalayo ali nyomi pambuyo. Kenaka anthu ena omwe anaona izi maka-maka amuna anathawanso pa malowo kuopa kuona zomwe dalaivala wa minibus-yo wakumana nazo. Nthawi yomweyo dalaivalayo anakakwera mini bus yake ndikuchoka pa malowo asakufuna. Pa nthawiyo nkuti anthu akufa ndi phwete malinga ndi zomwe zinachitikazo. Anthu ambiri maka-maka amuna nkuti akumwazikana kuthawanso wa misalayo poopa kuti chipako chingawafikire iwo.
Mtsikana wina apezeka ali moyo m'munda
Mtsikana wina kwa Gelemu m’boma lomwelo la Salima yemwe anthu amamuganizira kuti anamwalira zaka zinai zapitazo wapezeka ali moyo m’munda wa mlimi wina. Malinga ndi yemwe watitumizira nkhaniyi akuti mtsikanayo anadwala nthawi yochepa ndipo anatisiya zaka zinai zapitazo kotero kuti anamfedwa anachita mwambo wonse wa zovuta mpaka kukaika ku manda. Makolo a mtsikanayo anafika poiwala wokondedwa waoyo. Masiku apitawa anthu ena omwe amalima m’munda wina pa mudzipo anachita jenkha ataona mtsikana yemwe amati wamwalirayo ali buno bwa muswe. Apatu anthuwo poyamba anathawa poganizira kuti amaona mzukwa. Koma m’modzi mwa anthuwo analimba mtima mpaka kumuyandikira mtsikanayo ndikumfunsa kuti ndi yani. Koma poyamba mtsikanayo samayankha koma atamveka chovala anayamba kuyankhula kuti sanafe koma nthawi yonseyi wakhala akumutsekera ku chipinda cha nyumba ina yomwe sangaizindikire. Ndipo ataona kuti amavutitsa ndi pamene anadzamutaya m’mundamo pakati pa usiku. Ndipo anthuwo anatengera wouka kwa akufayo ku bwalo la anyakwawa. Khwimbi la wanthu linakhamukira ku bwalo la anyakwawa kukaoza za malodzazo komwe banja lina lanenetsa kuti mtsikanayo ndi mwana wao yemwe anamwalira zaka zingapo zapitazi. Pakadalipano makolowo atengera mwanayo ku chipatala kuti akamupime.