Nkhaniyi ikuti mwamunayo ngakhale ali pa banja koma saphethira akaona mkazi kotero kuti tsiku lina anaponya mau kwa mkazi wina wapa banja yemwe anagonekera khosi. Ndipo awiriwo anagwirizana kuti akakomane ku nyumba kwa mkaziyo mwamuna wake akachoka pa nyumbapo kupita ku mitala. Tsiku lina pakati pa usiku mwamuna wa mchiunoyo anauyatsa ulendo wopita kwa mkazi wa m’nzakeyo poganizira kuti mwamuna wake wakagona ku mitala, chifukwa chakuti n’kachisisila mwamuna wakubayo anamuona mwini mkaziyo kwa mkazi wake woyamba. Ndipo mwamuna wakubayo anafikira kugogoda pa zenera laku chipinda cha maiyo. Naye maiyo kapena mwini mkaziyo sanayankhe koma mwamunayo anangotuluka m’nyumbamo mwachinunu ndikukatsekula ku khomo chibonga chiri ku manja. Pa nthawi yomwe mwini nyumbayo amatsekula ku khomo mwamuna wakubayo nkuti akusekelera kuti zatheka osadziwa kuti aona chomwe chidameta nkhanga mpala. Mwini mkaziyo ataona kuti ndi mwamuna sanachitire mwina koma kupha nyani mosayang’ana nkhope. Ndipo mwamuna wakubayo pamene amathawa n’kuti mwazi ukuyendelera thupi lonse. Ngakhale anakwanitsa kuthawa koma mwini mkaziyo anamuzindikira mwamuna wakubayo. Pakadalipano nkhaniyi ili ku bwalo la anyakwawa.
Mkulu ogulisa ma foni zimuonekela
Mau aja akuti chikondi si ndalama aphelezera. Yemwe watitumizira nkhaniyi wati mkulu wina wodziwika bwino pa nkhani yogulitsa ndikukonza mafoni pa boma la Mchinji zamuonekera. Mwamunayo wakwatitsa kumene ukwati ndi mkazi wina miyezi iwiri yapitayi. Koma wadzidzimuka mkazi wake atathawitsana ndi telala wina yemmwe anawasokera zovala zawo zapa ukwati. Tsiku lina mwamunayo anatsazika mkazi wake kuti akupita ku mapemphero a usiku, koma atakafika ku mpingoko chifukwa chakuthima kwa magetsi komanso generator yapa malowo inaonongeka abusa analamula kuti mapemphero a usiku asakhale m’malo mwake anthu akumana masiku akudzawa. Mwamunayo anapotoloka kubwelera ku nyumba. Koma atakafika ku nyumba kwake mwamunayo anachita kakasi kupeza kuti mkazi wake mulibemo m’nyumbamo. Atafunsa anthu ena woyandikana nawo m’nyumba anamutsina khutu kuti mkazi wakeyo anamuona akuthawitsana ndi telalayo. Zikumvera kuti telalayo wathawitsira mkazi wa mwiniyo ku malo ena m’dziko la Zambia. Pakadalipano mwini mkaziyo akulilira ku utsi.
Akana kugawa thumba la soya
Mai wina wapa mudzi wa Maliro kwa Jenala m’boma la Phalombe wadabwitsa anthu atakana m’maso muli gwa kuti sagawana ndi munthu thumba la soya wolemera 25 Kilogrammes lomwe adalandira kuti agawane. Watitumizira nkhaniyi wati tsiku lina pa mudzipo panafika akulu-akulu a mabungwe omwe amapereka thandizo kwa anthu osowa. Lina mwa thandizolo nkuphatikizapo mafuta wophikira komanso soya mwa zina. A bungwewo analamula kuti thumba limodzi la soya lolemera 25-kgs azigawana anthu osachepera atatu. Mai waumbomboyo atalandira thumba la soyayo kuphatikizapo zinthu zina anangoti wereru phazi thandize kuthawa n’komweko osafuna kuti agawane soyayo ndi anzake. Anthu ena omwe amaganiza kuti m’nzawoyo amafumuka kuti akagawa ndi anzakewo pansi pa mtengo wina kumeneko anafiira maso kufufuza maiyo koma osamuona. Atafunsa-funsa anthu ena anawafotokozera kuti maiyo watha mtundu kotero kuti akulowera njira ya ku nyumba kwake. Anthuwo sanaimve mpaka ena anapalasa njinga kutsatira maiyo. Ndipo anakampeza ku nyumba kwake akukandira nthalo pamoto. Ndipo mai waumbomboyo amaonetsa kuti sizimamukhudza kotero kuti anafunsa anthuwo kuti amafunaji? Ngakhale anthuwo anayesera kumukumbutsa poganizira kuti mwina waiwala kuti soyayo ndi wofunika kugawana, koma maiyo anakana kwa mtu wa galu kugawana soyayo ndi aliyense. Anthuwo sanaimve kotero kuti anakatula nkhaniyi kwa nyakwawa. Pamene timalandira nkhaniyi nkuti maiyo akumududuluzira ku bwalo la anyakwawa ngakhale ali ndi pakati potopa.