You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma13/06/17

13/06/17

Written by  Newsroom

Mnyamata wina aba kabudula wachikazi musitolo

M’nyamata wina wa kabaza wapa mudzi wa Chipakuza ku Nchalo m’boma la Chikwawa watha masiku angapo asakupita ku geni yake mbiri itawanda kuti anamugwira akuba kabudula wa mkati m’sitolo ina yotchuka kumeneko.

13
June

Nkhaniyi ikuti tsiku lina m’nyamatayo ataweruka ku bizinesi yake ya kabaza analowa m’sitolo ina momwe amafuna kugula kabudula wa mkati. Koma m’nyamatayo atalowa m’sitoloyo pa zifukwa zodziwa yekha poganizira kuti wogwira ntchito m’sitoloyo sakumuona anatola kabudula m’modzi wa mkati ndikusunga pa chilolo. Koma pamene amachita zimenezi nkuti wogwira ntchito m’sitoloyo amamuona ndipo sanamfunse. Mosakhalitsa m’nyamatayo akutuluka m’sitoloyo wogwira ntchito anamuwakha ndi kumfunsa kuti akalipire zomwe wabisa pachilolo. M’nyamatayo anachita chibwibwi. Anthuwo anamutengera m’chipinda china m’sitoloyo komwe anakatulutsa kabudula wa mkati yemwe anabayo ndikumulamula kuti alipire kawiri mtengo wa kabudula wa mkatiyo. Ndipo pomaliza anamupaka penti ndipo anasanduka ngati chiboli. Kotero kuti pamene amapita kwao ana m’njira yonse amanka namuimba nyimbo. Pakadalipano m’nymatayo watha masiku akubindikira m’nyumba kamba ka manyazi ndi nkhaniyi.

 

Alowetsa mamuna wina mnyumba

Mai wina wapa mudzi wa Panapuruma m’boma la Thyolo waimitsa mitu ya mikoko yogona atalowetsa mwamuna wina m’nyumba mwamuna wake atangochoka kanthawi pang’ono. Nkhaniyi ikuti mkaziyo anakwatiwa ndi mwamuna wina yemwe kwao ndiku Mangochi. Mwamunayo anavomera kumakakhala kwao kwa mkaziyo m’boma la Thyolo kutanthauza kuti amakhala pa chikamwini. Banja la awiriwo limayenda bwino lomwe mpaka kukhala ndi mphatso ya ana. Masiku apitawa mwamunayo anatsazika mkazi wake kuti akupita ku mudzi kwao kukazonda abale ndi anansi. Ku ulendowo mwamunayo anakatha sabata ziwiri, pa nthawiyo mkazi wake sanachitire mwina koma kulowetsa mwamuna wina m’nyumba nkumakhala naye monga banja. Mwini mkaziyo atafika pakhomo pake kuchokera ku ulendowo anapezelera mwamuna m’nzakeyo m’nyumba atamfunsa mkazi wake kuti afotokoze za mlendoyo. Mkaziyo anayankha m’maso muli gwa!!! kuti ndi mwamuna m’nzanu ameneyu mizikhala awiri m’nyumba muno. Ndipo mkaziyo anauza mwamuna wakeyo kuti ngati asakufuna akhoza kuchoka pakhomopo. Pakadalipano amuna awiriwo akukhala nyumba ndi mkazi m’modzi. Mikoko yogona komanso anthu ambiri m’deralo akuganiza kuti mkaziyo anadyetsa amunawo mankhwala a kondaine.

 

Akamwini athilana diso la ntudzu

Akamwini awiri omwe akwatira ku banja lina kwa Msaka m’boma la Balaka akuyang’anizana ndi diso la nkhwezule. Nkhaniyi ikuti mwa amuna awiriwo wina ndi wodzilimbikira pakhomo pake pamene winayo ndi mlesi wotheratu. Pa khomo pa mkamwini wodzilimbikirayo ndipa mwana alirenji ndipo sasowa kanthu kamba ka khama lake. Koma mkamwini waulesiyo akungokhalira kuba mitengo yakumanda nkumatentha makala kuti azigulitsa, ndipo ndalama zake zimakathera kumwera bibida.Mopanda manyazi mkamwini waulesiyo masiku apitawa anakaponda-ponda mwa asing’anga a mankhwala a zitsamba komwe anampatsa mtela wophera m’nzakeyo chifukwa akumuchititsa manyazi pamudzipo. Koma ngakhale anayesera kuchita izi mankhwalawo sanagwire ntchito. Mwa manyazi mkamwini waulesiyo wapita ku mudzi kwao m’boma lina kumwera kuno ati kukafuna katakwe yemwe angampatse hamala ya ufiti kuti ati akong’onthe mkamwini m’zakeyo chifukwa cha kaduka.Naye mkamwini m’nzakeyo wadziwa za nkhaniyi ndipo wati iye amakhulupilira Chauta ndipo apitiriza kumuteteza kwa adani ake.

 

Chinthu chosadziwika chikuntha mkulu wina

Mwamuna wina wapa mudzi wa Mikochi kwa Makanjira m’boma la Mangochi ali mu ululu woopsya m’chipatala china m’bomalo momwe amugoneka chinthu china chosadziwika chitamukuntha. Nkhaniyi ikuti mwamunayo ndi wodzilimbikira pakhomo pake kotero kuti sipadutsa galu wakuda. Anthu ena wosafunira zabwino banjali akhala akufuna-funa njira zoti athane ndi mwamunayo kuti banjalo lisauke. Tsiku lina mwamunayo akuchokera ku munda mkazi wake ali pambuyo atatsala pang’ono kufika ku nyumba kwake. M’maso mwake munachita chidima kotero kuti anagwa pansi nkukomoka. Mwamunayo anakazindikira ali mchipatala atatsitsimuka. Uko ndi komwe amafunsa mkazi wake kuti ndapezeka bwanji m’chipatala muno? Koma mwamunayo wanenetsa kuti akangotuluka m’chipatalamo naye aponda-ponda kuti akhaulitse anthu omwe akumuseweretsa m’matsenga.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter