Chomwe chachitika mchoti mnyamatayu yemwe amatchuka ndi dzina loti Jump Gear amayendetsa Mini Bus yomwe imayenda kuchokera ku Chilomoni kupita ku Blantyre . Zimkuveka kuti pa tsikuli Dalaivalayo anamuuza kondakitala wake kuti adikire malo ena kamba koti anthu ena anamuchita hayala. Koma kondakitala uja atadikira kwa nthawi yaitali , anaimbila foni dalaivalayo kuti afotokoze komwe ali. Pamenepa munthu wina ndi amene anayankha foniyo ndikumuuza kondakitalayo kuti dalaivala wake wachita ngozi. Nthawi yomweyo kondakitalayo anaimbila foni bwana wake ndikumufotokozera za malozazo ndipo anamufunafuna dalaivalayo koma sanamupeze. Patatha tsiku limodzi mwini mni-busyo analandila telefoni kuti mini-busyo yapezeka ku malo okwerel;a bus a Wayenela. Koma zodabwitsa ndi zoti atafika pa malopo anapeza kuti Mini-busyo ilibe Engineer ndi battery. Koma anthu ena anaulula kuti anaona dilaivalayo akuchotsa enginer uku akunene kuti yanokola. Pakadali pano achitetezo akufunafuna mbavayo ndipo ikapezeka ikuyembekezeka kudzayankha mlandu wakuba.
Azembelerana ndi mlamu wake
Mnyamata wina wapa mudzi wa Magileta kwa Likoswe m’boma la Chiradzulu wadabwitsa anthu atazemberana ndi mlamu wake yemwe ndi mkazi wa mkulu wake. Nkhaniyi ikuti pa mudzipa pali anyamata ena awiri apa chibale omwe ndi munthu ndi m’ng’ono wake. Wang’onoyo amakhala pakhomo pa mkulu wakeyo. Wamkuluyo anapeza ntchito nkumagwira ku kampani ina ku Mapanga pa mseu wopita ku Zomba. Atagwira ntchito kwa zaka zingapo m’nyamata wa mkuluyo anapezeranso ntchito m’ng’ono wakeyo ku kampaniyo. Koma mphuno salota kuti amachitira izi kwa munthu woti anali ndi kampeni ku mphasa. Masiku apitawa zadziwika kuti m’ng’ono wakeyo amazembarana ndi mkazi wa mkulu wakeyo. Apa mkulu wakeyo sanachitire mwina koma kupitikitsa pakhomopo m’ng’ono wakeyo kamba ka nkhaniyi. Pakadalipano banja la mkulu wakeyo lasokonekera. Ndipo zikumveka kuti wam’ng’onoyo akuzemberanabe ndi mlamu wakeyo.
Mwambo wamaliro usokonekera
Mwambo wa maliro unasokonezeka kwa kanthawi pa mudzi wina kwa Mayaka m’boma la Zomba. Nkhaniyi ikuti nyakwawa yapa mudzipo inadwala mpaka kutsikira kuli chete. Ndipo aku banja lachifumu podziwa kuti ali ndi manda awo-awo pafupi ndi pakhomopo analamula adzukulu kuti akagwire ntchito yokumba dzenje la manda. Koma m’nyamata wina wa bere laling’ono sanakondwere ndi zimenezi kotero kuti analetsa adzukuluwo kugwira ntchito yokumba dzenje la mandalo. M’nyamatayo anafika pokagona m’dzenje la mandalo kuletsa adzukuluwo kuti asapitirize kugwira ntchitoyo. Mikoko yogona itamupha ndi mafunso m’nyamatayo chifukwa chomwe amachitira izi , anayankha zinthu zosagwira mtima. Mikoko yogona inalamula anyamata a dzitho omwe anagwira m’nyamatayo ndikumangilira ku mtengo pakhomopo kufika mwambo wonse utatha. Anthu ambiri akuganiza kuti m’nyamatayo amachita izi kamba kosuta chamba.
Mwana atumikila chibwenzi cha mayi ake
Anthu apa mudzi wa Katewere kwa Khosolo m’boma la Mzimba akuloza-loza chala mai wina wapa banja yemwe mwana wake woyamba akutumikira ubwenzi wa maiyo ndi mphongo ina. Nkhaniyi ikuti maiyo wakhala pa banja ndi mwamuna wake kwa zaka khumi ndi chimodzi . Koma masiku apitawa mwamuna wake anauza mkaziyo kuti akufuna kukwatira mkazi wachiwiri zomwe mkazi wakeyo sanagwirizane nazo. Koma mwamunayo mosagwirizana ndi mkaziyo anakafunsira mbeta mkazi wina yemwenso anam’mangira nyumba pa mudzipo. Koma mwamunayo amalephera kuyendetsa mitala chifukwa amakhalitsa kwa mkazi wa m’ng’ono, kamba ka izi mkazi wa mkuluyo naye anapeza mphongo ina yomwe amazemberana nayo. Koma chomwe chikudabwitsa anthu ambiri pa mudzipo nchakuti mwana woyamba yemwe ndi mtsikana ndi amene amatumikira ubwenzi wa mai wakeyo. Koma mwamuna wa mitalayo atazindikira kuti mkazi wake wamkuluyo akumudyetsa njomba analamula mkaziyo kuti achoke pakhomopo. Koma mkazi woyambayo watemetsa nkhwanga pa mwala kuti zivute zitani sachoka pakhomopo.