You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma09/06/17

09/06/17

Written by  Newsroom

Gogo wina auka kwa akufa
Anthu akwa Gunda mdera la Jenala ku Phalombe akukhala mwa mantha chifukwa cha zomwe zawachitikira.

09
June

Dzulo laliwisili gogo wina wa zaka 65 anamwalira ndipo uthenga unapita kwa nyakwawa ya mderalo ndipo pachifukwachi nyakwawayo inayamba kuyendetsa za mwambowo , koma ali mkati kuyendetsa mwambowo analandila malipoti oti gogoyo yauka kwa akufa. Mikoko yogona komanso anthu ena omwe anafika pa malopo anauza anthuwo kuti abalalike pa siwapo koma asanafike m’makomo mwao analandilanso uthenga wina oti mdzukulu wa gogoyo wa zaka khumi ndi ziwiri wamwalira osadwala ndipo apa anthu anagwidwa nkhongono komabe nyakwawa ya mderalo ndi anthu apa khomopo anagwirizana zotumiza mauthenga . Muthenga onse okhudza maliro atalengezedwa anthu pa siwapo anali ndi mantha komanso odabwa atamvanso kuti gogo ija yamwalira tsopano. Pamene timalandila nkhaniyi nkuti pakhomopo pakuliridwa maliro awiri zomwe ena akukhulupilira kuti mzochititsa mantha koamanso nzodabwitsa mbiri ya deralo. Koma mikoko yogona inatsikimizila anthuwo kuti asachite mantha chifukwa choti mwa zina gogoyo imafuna ntsamilo. Pa chifukwachi magulu ena opemphera alangiza anafedwa kuti mpofunika kuitanitsa mapemphero kuti achotse mizimu yoipa chifukwa nkhani za mtunduwu mzamakedzana.

 

Abindikila myumba kamba ka manyazi 
Mkulu wa mpingo wina kwa Gulupu Chibuli mdera la Ndamera ku Nsanje akukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi. Masiku apitawo mwana wa mkazi wa mwamunayo banja lake linatha pa zifukwa za mbanja ndipo pa chifukwachi anabwerela kudzakhala ndi makolo eke. Ali pa khomopo mkulu wa mpingoyo analangiza mwana wakeyo kuti mpofunika kuchita zizimba kuti athenso kupeza banja. Mwanayo pofuna kumvetsa za nkhaniyi, mtumiki wa Ambuyeyo mopanda manyazi analangiza mwanayo kuti aonetseredwa kuti adzikhalira limodzi ngati njira imodzi yopezera banja mofulumira. Mkazi wa mkulu wa Mulunguyo anayamba kudabwa za makhalidwe a bamboyo ndi mwana wakeyo ndipo tsiku lina anthu ena anamutsina khutu za mayendedwe a anthuwo. Paja pali mau oti lafote limakwana tsiku lina anthu ena akufuna kwabwino anapezerela anthu awiriwo ali pa chikondi pa nyumba ina yogona alendo. Ku maloko kunali kuthidzimula anthu awiriwo ndipo mtumiki wa Ambuyeyo pofuna kudziteteza anauza anthuwo kuti mzimu wa Satana ndi omwe unamunyenga. Apa anthuwo sanaimve koma kufafantha gulupayo mpakana thapya. Pakadali panomkuluyo amuimitsa mu mpingo ndipo akukhalira kubindikira mnyumba ina chifukwa cha manyazi.

 

Abeledwa masanasana 
Mau oti wakuba alibe malemba apherezera pamudzi wa Mgunda mdera la Sub- TA Ngwerelo m’boma la Zomba . Nkhaniyi ikuti mai wina yemwe amapita ku chigayo anakomana ndi njonda ina yomwenso inaoneka kuti njachifundo ndipo inauza maiyo kuti amuthandize pomunyamulira mphale yake pa njinga mcholinga choti apepukidwe ndi katunduyo. Maiyo sanavute ndipo m’malingaliro ake anangoti laponda la mphawi ndipo anapereka mphaleyo kwa mwamunayo. Koma chodabwitsa mwamunayo yemwe anthu ambiri akukhulupilira kuti ngwa kabaza atayenda mtunda ochepa anayamba kutchova njingayo mofulumira kwambiri zomwe zinadabwitsa maiyo mpaka kuyamba kukuwa mokweza kuti anthu amuthandize koma zachisoni mwamunayo sanaonekenso. Apa maiyo anagwira njakata polingalira kuti chakudya chinali chomwecho. Pakadali pano mikoko yogona komanso anthu aza chitetezo mderalo atsimikizila banjalo kuti apitiliza kufunafuna mbavayo ndipo ati akaipeza iona chomwe chidameta nkhanga mpala. Mwamuna wa maiyo akukhalira kuzazila maiyo kuti ndiosa changamuka chifukwa sangangokhulupilira munthu yemwe sakumudziwa.

 

Agwidwa utambwali wa nchiuono 
Mau oti ukatambatamba udziyang’ana ku m’mawa apherezera mdera la Nkula mboma la Machinga. Nkhaniyi ikuti mai wina yemwe mwamuna wake anapita ku Joni zaka zingapo zapitazo wakhala akuyenda ndi amuna a weni. Anthu akamulangizi kuti asinthe paza khalidwe lakelo iye wakhala akuponyera malangizowo ku nkhongo. Chodabwitsa anthu pa nkhaniyi mchakuti mwamuna wa maiyo wakhala akusamalira maiyo pomuchitila chili chonse koma maiyo samakhala pansi ndi khalidwe lake lachimasomaso. Masiku apitawa mkaziyo anazindikira kuti mwamuna wake mphekekesera inamupeza ndipo anayamba kumalalatila aliyense polankhula mwa thamo kuti samutha chifukwa iye ndi sadyeka. Masiku apitawa mkaziyo anagwidwa ali pa chikondi ndi mwamuna wa mwini kunyumba yogona alendo ndipo kunali kuthidzimula kolapitsa pamodzi ndi mwamunayo. Koma mwatsoka njondayo inawapulumuka anthuwo ndipo akubanja anakokera mkaziyo ku bwalo ndikumulandula pa banja. Anthu ambiri kuphatikizapo amai amzake akukhalira kumuseka maiyo kuti sadyeka lero wadyeka. Pakadali pano maiyo akuyenda njira zodula chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter