Error
  • JUser: :_load: Unable to load user with ID: 3
You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma08/06/17

08/06/17

Written by 

Mai wina adzelezeka
Mai wina m’dera la Khonsolo m’boma la Mzimba wadzelezeka. Nkhaniyi ikuti mderalo muli mai wina yemwe ali pa banja ndipoi amakhala pamudzi wa mwamuna wake.

08
June

Koma mkaziyo sakondwera ndi ana omwe mwamunayo anabereka ndi mkazi wake woyamba. Choncho tsikulina anafuna kuchitira m’modzi wa anawo chiwembu pomuthira dala madzi amoto. Koma mwa mwai zinalephereka. Ndipo nkhaniyi inamufika bambo wa anawo yemwe analandula kuti mai-yo achoke pakhomopo. Koma mkaziyo sanakondwere ndi nkhaniyo ati poti wabereka naye ana atatu. Ngakhale wakakangamira pakhomopo mwamunayo wasamuka mnyumba yomwe ankakhalamo ndi mkaziyo. Izi zachititsa kuti mkaziyo ayambe mchitidwe woyenda-yenda pomapezeka ku malo omwela mowa komanso kumalo ogona alendo maka tsiku la msika wapa Jenda kambo koti akusowa munthu wumusamalira. Komanso akuti mkaziyo akufunsira amuna omwe iye akufuna kuti achite nao zachiwerewere maka ana achichepere. Pakadali pano anthu akumuseka maiyo kuti wadzelezeka.

 

Mwamuna wina akunthidwa kamba ka nsanje

Mwamuna wina yemwe ndi mkulu wachitukuko kwa Nkando m’boma la Mulanje amuswa kamba ka Nsanje. Yemwe watumiza nkhaniyi wati zaka zapitazo mkuluyo anasiya mkazi wake ndikukwatira wantchito wake. Koma banjalo silimayenda bwino kweni-kweni kamba nthawi zambiri mwamunayo amakaikira mkazi wake kuti akumuyenda njomba. Ndipo Lamulungu lapitali mwamuna wa nsanjeyo anapeza nambala yachilendo mu lanya yammanja ya mkazi wake. Koma mmalo mofunsa mkazi wake za nambala yachilendoyo mwamunayo adamema anyamata awiri ndikupita kunyumba kwa mnyamata wina yemwe amamukaikira kuti anali pa ubwenzi ndi mkazi wakeyo. Atafika ku nyumba kwa bamboyo ndeu yafumbi inabuka pakati pao. Ndipo mwini nyumbayo amaponya zibakera zoonetsa nyenyezi ndi masana omwe mpaka zomwe zatupitsa nkhope ya mwini mkaziyo ngati chitumbuwa cha nthochi. Koma nkhaniyi itafika kwa mikoko yogona yomwe inayesera kuimba nambalayo zadziwika kuti mwini nambalayo ndi m’bale wa mkaziyo yemwe amakhala mu mzinda wa Blantyre. Pakadali pano mwini mkaziyo yemwe ndi waudindonso wasowa mderalo ndipo sakudziwika komwe ali. .

 

 

Anthu akhumudwa ndi zamatsenga

Anthu okhala kufupi ndi mai wina m’boma lomwelo la mzimba koma ku Ekwendeni ati ndi okhumudwa ndi zamatsenga zomwe mai wina akukomana nazo. Watitumizila nkhaniyi wati mai wina banja lake lidatha mchaka cha 2005 ku Lilongwe komwe ankakhala. Koma chodabwitsa nchakuti chifikileni ku Ekwendeni amaona zoopsya kwambili usiku. Mwa zina, akuti m’nyumba mwake mumapezeka njoa zisanu pa kona pa nyumba komanso ti anthu tatifupi kwambili tomwe timamuopsyeza mayiyo pamodzi ndi mwana wake wamkulu yemwe sakupeza banja ngakhale amuna kumufunsila ai. Chowawa kwambili mayiyo akuti akagona amamva kuti akumubaya ndi ma singano koma omubaya osamuona akamatelo mpamene ti abathwa tija timagundika kuseka. Mwamuna wa mayiyo panopa akuti adakwatila mkazi zina komabe anthu ati nkutheka kuti mwamunayo akudziwapo kanthu paza matsenga zomwe mkazi wakeyo akukomana nazo. Panopa akukonza zopita kwa mkulu wina wa zitsamba kuti akaombeze ndikudziwa chomwe chikuchitika.

 

 

Gogo wina akunthidwa

Gogo wina wa zaka 70 wachimina kwa mfumu Mpando m’boma la Ntcheu atamuphika kodetsa nkhawa. Watitumizila nkhaniyi wati anthu ena ambumba akhala akulimbirana malo wolima ndipo nkhaniyi itapita kwa mfumu ya ndondo idakomera mbali ina ya mbumbayo. Izi zinapatsa mphamvu omwe nkhaniyo inawakomela kupitiliza kulima pamalowo ndipo momwe mvula yagwa mdelalo masiku apitawa omwe nkhani inawakomela aja anapita kuti akabzyale mbeu zao. Izi sizidakomele anthu omwe amagonja mlandu aja ndipo anauyana kupita kumundawo kwinaku atanyamula zida kuphatikizapo mikondo, zikwanje, mivi, nyundo komanso mankhwala azitsamba ati kuti akathambitse anzao aja. Chomwe chinadabwitsa anthu nchakuti gogo wina wa zaka pafupi-fupi 70 ndipo satha kuyenda chifukwa cha ukalamba analimbikila kuti nkhondoyo akamenya nao. Pamenepa, akuti anauza mdzukulu wake kuti amubereke kumbuyo ndipo apa anakalowa m’nyumba chokwawa momwe anakamangilila supa ndi mphinjili mchiuno komanso kuzipaka ufa kotelo kuti amachita kuopsya maonekedwe. Anthu omwe anali pamalopo anali ndi mantha ndi maonekedwe agogoyo. Koma atafika kumunda ambali ya gogoyo zinawavuta mpaka anawadzoka nazo dzibakela dzomwe dzinawatupitsa ngati chitumbuwa. Panopa anthu akumbali ya gogoyo akupitiliza kuopsyeza kuti achita chotheka pogonjetsa anzaowo pogwilitsa ntchito mankhwala azitsamba.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter