Nkhaniyi ikuti mkuluyo kwawo ndi m’mudzi mwa Kachulu kwa Mfumu Kuluunda mboma la Salima koma amakhala ku Kasungu ndi mkazi wake yemwe anamupeza ndi mwana kale ndipo anavomereza zolera mwanayo ngati wake. Mkuluyo ataona kuti mwanayo wayamba kufika pa chitsikana anayamba kudyerera maso mpaka kumalowa ku chipinda kwa mwanayo usiku. Masiku apitawa mayi ake a mwanayo anayamba kumudabwa ndipo atamufunsa za mimba yomwe ali nayoyo anatchula atate ake omupezawo. Nkhaniyi inayimitsa mutu mayiyo ndipo sanachitire mwina koma kukanena ku polisi. Pakadali pano mkuluyo akumusunga m’chitokosi cha apolisi podikira tsiku la mlandu.
Njoka yamatsenga ipezeka pakhomo pena
Mboma la Lilongwe koma m’mudzi mwa Lombwa kwa Mfumu Kabudula, anthu anakhamukira pa nyumba ina njoka yomwe akuiganizira kuti ndiya matsenga itapezeka pakhomopo. Nkhaniyi ikuti lero m’mawa mwamuna wapakhomopo anachokapo. M’mbuyomu mkazi wake akutakataka, anaona njoka ya mtundu wa chilere ili pa malo ena ndipo anatenga mtengo nkuikola kuti akayitaye kutali. Mwatsoka njokayo akuti inagwa ku mtengoko, koma chodabwitsa nchoti pamene imafika pansi inasanduka njoka ziwiri ndipo inayo inali ya mbuvu. Apatu mayiyo anachita mantha ndipo anakuwa kuitana anthu kuti akaone za malodzazo. Ambili mwa anthuwo anamuuza mayiyo kuti asaphe njokayo koma m’malo mwake angoyivundikira pa malo ena kudikira mwamuna wake. Mwamunayo atafika pakhomopo anamufotokozera ndikumuwonetsa njokayo koma anapeza kuti ya mtundu wa chilereyo yafa koma inayo ili moyo. Pamenepa mwamuna wakeyo anakhumudwa kwambili poganiza kuti mwina alipo wina yemwe akumulondalonda ati kamba koti dzulo dzuloli mwamunayo waphanso njoka ina ya mtundu wachilere akuchokera koyenda ndi anzake. M’mene timalandita nkhaniyi nkuti njokayo akuyisungabe podikira kuti akuluakulu ena pamudzipo awathandize nzeru pa zomwe angachite ndi nojokayo. Komabe mwamuna wapakhomopo wanenetsa kuti iye amadalira Chauta ndi ngati alipo amene akumulondalonda ndiye kuti athana naye.
Akunthana kamba ka matumbo a nkhuku
Anthu anaseka chikhakhali pa famu ya Bunda, kwa T/A Chadza mboma la Lilongwe, anyamata awiri ataponyerana zibakera chifukwa cholimbirana matumbo a nkhuku. Yemwe watitumizira nkhaniyi wati anyamatawo amagwira ntchito pa famuyo ndipo onse amagonera komweko. Pafamupo akuti amaweta zifuyo zosiyanasiyana kuphatikizapo nkhuku zomwe zikakula amapha nkukagulitsa. Mwa masiku onse, amati akapha nkhukuzo amachotsa matumbo ndipo yemwe akuwafuna amatha kutenga ngati wathandiza nawo ntchitoyo. Patsikulo anyamata awiriwo anachalira kutenga matumbowo koma samadziwana. Matumbowo atapezeka kunali kulimbirana mpaka m’modzi mwa iwo anapsya mtima nkuyamba kuponyera zibakera nzakeyo kuti amusiyire. Komatu nzakeyo naye sanalore mpaka kuponyerana zibakerazo mwakathithi. Anthu omwe anali pamalopo amangowayang’ana kwinaku akugwa ndi phwete mpaka okha anatopetsana. Pakadali pano anyamatawo akaonana akumayenda modzikunga ngati afinye.