You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma03/06/15

03/06/15

Written by  Newsroom

Anjatidwa kamba kochita chisembwere ndi mkazi wa mwini
Mwamuna wina wa zaka 75 wapa mudzi wina m’boma la Thyolo akupika jere ya chaka chimodzi khothi la Majistrate m’bomalo litamupeza wolakwa pa mlandu wovulaza mwini mkazi komanso kuchita chisembwere ndi mkazi wake.

03
June

Khothilo linamva kuti mwamunayo Jackson Mokowa wakhala akuzemberana ndi mkazi wa a Faduweki Masamba pomakumana m’dimba la ndiwo zamasamba pafupi ndi m’jigo wina pa mudzipo. Mkaziyo wakhala akudyetsa njomba mwamuna wake, ndipo mwamunayo ponyumwa ndi mayendedwe a mkaziyo tsiku lina n’kachisisila anamutsatira ku m’jigo komwe anati akukatunga madzi. Atafika pa m’jigopo mwini mkaziyo anadabwa kupeza ndowa yokha ndipo atakweza maso anaona mkazi wakeyo ali ndi mwamuna wakubayo m’dimba la ndiwo zakudimba pafupi ndi pamalopo. Mwamunayo anafuula kuitana ena kuti amuthandize kugwira mwamuna wakubayo , koma pa nthawiyo mkaziyo anathawo kusiya mwamuna wakubayo pa malowo. Mwini mkaziyo anayesera kugwira mwamuna wakubayo koma mwamuna wa mchiunoyo anatema mwini mkaziyo ndi chikwanje m’mutu ndikumusiya ali kwala mwazi ukuyendelera mthupi lonse. Anthu ena ndi omwe anathandiza mwini mkaziyo pomutengera ku chipatala. Ndipo poweruza nkhaniyi Majistrate Mtunduwatha Mpaso wadzudzula kwambiri mwamuna wa mchiunoyo kuti anayenera kukhala wachitsanzo ndipo amulamula kukakhala ku ndende miyezi khumi ndi iwiri kuti anthu ena akhalidweli atengere phunziro.

 

 

Abaja mkazi wake kamba ka nsanje
Mkazi wina wapa mudzi wa Kakhobwe ku Tsangano mboma la Ntcheu manja ali mkhosi apolisi atamugwila chifukwa chobaya mkazi mzake ndi mpeni polilira nsanje. Nkhaniyi ikuti mwamuna wa mkaziyo ndiwa mitala ndipo kwa mkazi wachiwiri anabeleka-konso mwana. Pa tsikuli, mphongoyo inanyamuka kwa mkazi wake woyamba kupita kuchiwiri komwe anakapeza mwana akudwala. Pamenepa, mwamunayo anatengana ndi mkazi winayo pamodzi ndi mwana wodwalayo kupita ku nyumba kwa mai wa bamboyo ncholinga choti akaone mwanayo. Ali komweko, mkazi woyamba anamva zoti mzakeyo anali kwa apongozi ake ndipo anasolola mpeni ndikuyamba kuwunola ncholinga chofuna kukathana naye. Kenaka, anaubutsa ulendo kupita kwa apongozi akewo komwe anakafikila kubaya mkazi mzakeyo pakatumba mpaka mpeniwo kutulukira mbali ina ya katumbayo ndipo pomaliza anathawa. Nkhaniyi inakafika kwa apolisi omwe anamusaka mpaka kumugwila kotero kuti panopa ali mchitokosi ndipo akudikira tsiku lokalowa mkhothi pa nkhaniyi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter