Chomwe chinachitika ndichoti anthuwo amakhala nyumba zoyandikana ndipo mkazi wang’onoyo anali odzilimbikira pa nkhani ya ulimi kotero kuti anapeza dzokolola dzambiri. Tsiku lina mkazi wang’onoyo anayanika ufa ndipo anapita kukasamba ku bafa. Pamenepa mkazi wakuluyo anatenga litchelo lake ndikukagwada pa phasapo nkuyamba kusefa ufawo. Izi zinakwiyitsa mkazi wang’onoyo ndipo mkangano unakula ndipo anayamba kumenyana mpaka kugwetsana pansi. Kenaka mkazi wang’onoyo anangotenga mtengo ndikumenya mkazi wamkuluyo mpaka kumuthyola. Pamene zimachitika izi nkuti mwamuna wao ali ku msika akuyenda bawo. Anthu ena ndio anathamanga kukamuuza mkuluyu ndipo amabwera ali wefuwefu. Mkazi wang’onoyo sanalankhule chili chonse koma kumanga katundu wake mkuchoka pa khomopo ndipo mpaka pano sanabwerele. Anthu ambiri akudzudzula mkazi wamkuluyo chifukwa cha khalidwe lake losowetsa mzakeyo mtendere.
Afuna kupha mkazi wake ndi chikwanje
Mwamuna wina pa mudzi wa Tambwandira kwa Sinyala m’boma la Lilongwe ali m’chitokosi cha apolisi kamba kofuna kukhapa mkazi wake ndi chikwanje. Nkhaniyi ikuti mwamunayo ndi wamitala ndipo ukwati ndi mkazi wake wamkulu watha mwezi wathawu pa zifukwa zodziwa awiriwo. Kamba ka izi mwamunayo yemwe mkazi wake amakhala kuchitengwa anapitikitsa mkaziyo kuti azipita kwao omwe ndi mudzi woyandikana kusiyana mbeu zonse ku munda. Maiyo ataona kuti njala yalowa pa nyumba anaganiza zoti akakolole chimanga ku munda kwake. Anauyatsa ulendo pamodzi ndi abale ake kupita ku mudziko ndipo anakafikira kwa anyakwawa komwe anakapempha chilolezo, ndipo inawalola kutero. Koma anthuwo ali ku mundako kukolola chimanga munthu wina anaimbira foni mwamunayo paza nkhaniyi. Pa nthawiyo mwamunayo n’kuti ali ku msika kugulitsa nkhuni. Pomva izi mwamunayo anasiira m’nzake malonda akewo ndikuthamangira kumundako, koma pa nthawiyo nkuti chikwaje chakuthwa chiri wali-wali m’manja. Koma mwamwai sanampeze mkazi wake wamkuluyo pamodzi ndi abale ake. Mwamunayo anachoka kumundako ndikupita ku mudzi kwa mkazi wakeyo komwe anakazunngulira mudzi wonse chikwanje chakutwa chiri ku manja uku akufuula kuti ndipha munthu. Anyamata a dzitho anawendelera mwamunayo ndikumugwira ndikupita naye ku polisi komwe amutsekera kudikira kukayankha mlandu wosowetsa anthu mtendere.
Apeleka bulangete lakujoni kwa mkazi wachibwenzi
Mwamuna wina wapa mudzi wa Masinde kwa Chigalu m’boma la Blantyre akuyenda wela-wela ngati wataya singano mkazi wake atatulukira kuti wapereka bulangeti laku Joni kwa mkazi wachibwenzi. Nkhaniyi ikuti masiku apitawa pa mudzipo pafika mkazi wina yemwe banja lake latha. Mwamuna wa mchiunoyo anadyelera maso pa mkaziyo kotero kuti awiriwo anapalana ubwenzi wa nseri. Mwamuna wachisembwereyo anazembetsa bulangete kwa mkazi wake ndikukaipereka kwa mkazi wachibwenziyo. Anthu ena anatsina khutu mwini mwamunayo paza ubwenzi wa awiriwo komanso za gombeza lomwe mwamanuyo wapereka kwa mkazi wachibwenziyo. Mwini mwamunayo sanaimve kotero kuti tsiku lina mogwirizana ndi achibale ake anakachita ndeu ku nyumba kwa mkazi wakubayo ndikulanda bulangeteyo. Pakadalipano mkazi wa mkuluyo wachoka pakhomopo pamodzi ndi ana ake kupita kwao potopa ndi khalidwe lachimaso-maso la mwamuna wakeyo. Pakadalipano mwamunayo akuyenda zoli-zoli kamba koti mbiri yake yawanda pa mudzipo.