Nkhaniyi ikuti pamalo ena omwela mowa mdelalo kunamveka kuti kubwela amai anai omwe ali ndi luso la mavinidwe ndipo pa chifukwa ichi amuna omwe amamwa mowa anali ndindindi kudikilila kuti aone akaziwo. Mosakhalitsa mwini malo omwela mowa uja analengeza kuti amai aja afika ndipo anthu ena akuti anasiya malonda ao pamsikawo kuti akaone amaiwo. Anthu ali mkati molimbilana nkuti aone bwino lomwe, amai aja anatulukila kwinaku atavala tizovala toonetsa tchafula pa mtunda. Kenaka, amaiwo akuti anayamba kuvina modolola mitima ya amuna omwe anali pamalowo. Koma akuti m’nyamata wina analephela kuugwila mtima mpaka anakalowa mubwalo kuti ati avine ndi amaiwo. Dansi itafika pokoma m’nyamata uja akuti anakupatila mai m’modzi koma anamutsina makutu mpaka kulila ngati khanda. Anthu ena anauza mwini malowo kuti amaiwo azipita kwao ndikuti asokoneza mabanja a eni koma zakanika kamba koti nao amaiwo ati apeza amuna amsangala. Panopa, amai ena ambili akudandaulabe kuti amuna ao akukhalila kumaloko kusilila mbina za amaiwo.
M’busa wina ali kakasi ku joni mkazi atamuthawa
Akhrisitu a mpingo wina kwa maliri m’boma la Lilongwe akusokhetsa ndalama za Transport kuti amutumizira m’busa wao yemwe wangoti kakasi kusowa mtengo wogwira ku John mdziko la South Africa mkazi yemwe anatsogana naye atamuthawa. Masiku apitawa m’busayo amafalitsa bwino uthenga wa chauta ndipo akhristu ambiri amamukonda. Kenaka ‘busayo anapasidwa masiku atchuti ndipo anaganiza zopita mdziko la South Africa kuti akaone zinthu zina. Koma chodandaulisa ndi choti m’busayop anali ndi khalidwe lokonda akazi ndipo anagwa mchikondi mtsikana wina. Chibwezicho chitafika pamponda chimera anthu awiriwo anathawisana ndikupita ku John kuti akapumule ali limodzi ndipo izi zinathekadi. Koma pamene anafika ku johnko mkaziyo anamuuza m’busayo kuti amudikire mu pa sitejipo ndi cholinga choti amuitane m’bale wake yemwe amamuchingamila. Mwatsoka mtsikanayo ndi amene anatenga zikalata zonse zoyendela kuphatikazapo ndalama zogonera. Ndipo m’busayo atadikira kwa nthawi yaitali mtsikanayo sanabwerenso mpaka kunada . Pamenepa m’busayo anagona mu sitejimo koma movutika. M’mawa kutacha anayetsela kumuchayila foni mtsikanayo koma samayankha. Pamenepa m’busayo anaganiza zoyimbila lamya kumudzi komwe anafotokozera akomiti pamodzi ndi achibale kuti zamuvuta. Pakadali pano akomiti ya mpingowo akupempha chithandizo kuti mwina atumizire m’busa wawoyo kuti abwere ku maloko.