Nkhani-yi ikuti mkulu wina anakwela minibasi yochokela ku Limbe kupita ku Blantyre ndipo anati akwanitsa kulipila 100-Kwacha ndikuti 50 kwacha yamusowekela. Koma m’malo momvetsela kondakitala akuti anayamba kulankhula mokweza kulimbana ndi mkuluyo yemwe amaoneka kuti mwina ndalamayo analibedi. Malinga ndi mtolankhani wathu yemwe anali mu minibasiyo kondakitala mpaka anauza mkuluyo kuti amulanda nkhuku yomwe anasiya pafupi ndi mpando wa dalaivala akapanda kupeleka ndalama yokwanila. Pa chifukwa ichi anthu omwe anakwela minibasiyo anakwiya kwambili nkuyamba kudzudzula kondakitalayo kuti ndi munthu odzikonda polingalila kuti atha kukweza anthu ena m’malo ena okwelela basi ndikubwezeletsa yomwe imachepayo. Komabe ngakhale anthu amalankhula zimenezi kondakitalayo akuti anapitilizabe kuti alanda nkhukuyo. Pamenepa mkulu wina akuti anakwiya kwambili mpaka kutsala pang’ono kuchiponya chibakela koma anthu ena anamuletsa. Komabe anthu ambili ati akadakonda ngati makondakitala atamamvetsa momwe anthu ena okwela galimoto zao akudandaulila.
Agwetsedwa mumpingo atamenya abusa
Mkulu wampingo wina amuthothola mu mpingo ku Mwaye mdela la mfumu Kachenga mboma la Balaka atamenya mbusa wa mpingo-wo. Nkhani-yi ikuti mbusa wampingo wina analandila nkhani kuti mkhristu wake m’modzi yemwe ndi mkulu wampingo wakwatila mitala. Pa chifukwa ichi, anaitanitsa mkuluyo kubwalo la akulu. Kufika kumeneko mkuluyo anamuuza kuti ayambe waima kaye kubwela kumpingowo kufikila atamufufuza pankhani yoti wakwatila mitala. Koma m’malo modekha mkuluyo akuti anapulumutsa chibakela mpaka kuunjika pansi abusa aja. Momwe amati aziphikanso abusawo anthu anamugwila mkulu wampingoyo ndipo panopa amuthotholelatu mu mpingowo. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi zikuonetsa kuti akulu akulu kuchokela ku likulu la mpingowo alemba kale kalata yodziwitsa mkuluyo kuti simembalanso wampingowo. Panopa, mkulu wandeuyo akuyenda mogwetsa nkhope yake pansi ngati napiye ogwela mvuwo chifukwa anthu akumulozaloza.