Nkhani-yi ikuti anyamata awili amacheza ndi anzao pamalo ena koma mosakhalitsa wina anafuna asute nao fodya yemwe nzake anapichila. Koma nzakeyo akuti anamukaniza podziwa kuti ati nayenso salola anzake kusuta nao fodya wake. Pa chifukwa ichi, mkulu opempha fodya uja akuti analanda fodya wa nzake uja atalephela kuugwila mtima chibaba chitamuswa. Pamenepa, mzakeyo akuti sanaimve koma kuponya chibakela chomwe chinamuunjika nzakeyo pansi. Kenaka akuti inalikitika ndeu ya fumbi mpaka onse kutuwitsana ndi zibakelazo ndipo anasiyana okha aliyense ali wefu wefu malinga nkuti anzao anati awasiye kuthetsane khama. Panopa, amuna awiliwo akuti akumaonana ndi diso lofiila.
Achititsa katapira ndalama zachopeleka
Akhristu ampingo wina kwa ku Kasinje mdela la mfumu Ganya mboma la Ntcheu wasemphana zochita zitadziwika kuti akulu akulu apa mpingowo akumachititsa katapila ndalama za chopeleka. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi akhristu kwanthawi akhala akuona kuti ndalama zao sizikupindula ngakhale akhala akupeleka moolowa manja. Pachifukwa ichi akhristu ena anayamba kuunika za nkhaniyi mpaka zinadziwika kuti pali azikulu akulu angapo a mpingowo omwe akhala akubweleketsa ndalama ya mpingowo kwa anzao ndipo akatelo amapezapo phindu. Nthawi zina akuti akulu akulu okha okha ampingowo amabwelekana ndalamazo koma nthawi zambili amalephela kubweza kamba koti zamachita nazo kanthu ndipo m’malo mwake zimangothela palilime. Chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke nyanga china mchakuti denga la tchalitchi linasasuka ndipo pa chifukwa ichi akhristu anagwilizana zoti akatenge ndalama kuthumba zoti akonzele tsindwi la kachisiyo. Koma kupita kwa msungi chuma akuti anakakhumudwa atawauza kuti ndalama zili m’matumba mwa akhristu ena omwe adabweleka. Panopa, akhristu apa mpingowo akuti ayamba kudomoka m’modzi m’modzi mu mpingowo pamene ena angobweza manja posapeleka momwe amachitila m’buyomo. Pakadali pano, mbusa wapa mpingowo pamodzi ndi akulu akulu ampingowo angoti kakasi kusowa mtengo ogwila ndipo atsimikiza kuti padziko pano palibe chinsisi. Ndipo akhristu ambili ati akadakonda akulu akuluwo akadawathothola pa udindo mu mpingowo.