You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma28/05/15

28/05/15

Written by  Newsroom


Mayi wina achita zodabwitsa nkachisi
Akhristu ampingo wina mtaunishipi ya Bangwe mu mzinda wa Blantyre aima mitu ndi zomwe anachita mai wina mkachisi atamaliza kulandila mgonelo.

29
May

Nkhani-yi ikuti pa mpingo wina linali tsiku la mgonelo masiku apitawa ndipo mwambo onse unayamba bwino kwambili. Koma zinthu zinasokonekela nthawi itakwana yopeleka mgonelo kwa amai aja amavala zoyela kumtunda zofanana ndi masiketi akuda. Amene watipatsila nkhani-yi akuti zinali zodabwitsa kwambili mai wina atayamba kuchita zinthu ngati wagwa majini kubwebweta mpaka anzake kumutengela panja. Zimenezi akuti zinadabwitsa anthu ambili mu mpingwo ndipo amai anzake akuti anangoti zyoli kuchita manyazi ndi nkhani-yi. Panopa, sizikudziwika ngati mayiyo akubwelabe ku kachisiyo momwe amachitila nthawi zonse. Anthu ena ati mwina mayiyo analandila mgonelowo asadakonzeke bwino lomwe.

 

 

Asiya mwana wachichepele kwa nyakwawa
Mai wina yemwe adakwatila ndi nyakwawa ina kwa Chadza ku Bunda mboma la Lilongwe wasemphana maganizo ndi Azilamu ake atakasiya mwana wachichepele kunyumba kwa nyakwawa-yo. Nkhani-yi ikuti nyakwawayo ili ndi akazi awili ndipo ena akuti imalephela kuthandiza akazi awili ndi mwanayo. Malinga amene watumiza nkhani-yi mkazi wam’ngono amakhumudwa kwambili chifukwa choti nyakwawayo imakhalitsa kwambili kwa mkazi wamkulu. Tsono pa chifukwa ichi, anangotenga khandalo kupita nalo kwa nyakwawa-yo iye nkumapita kwao omwe ndi mudzi oyandikana zitadziwika kuti akumusasa kuti banja latha. Mayiyo akuti akamusiilanso mwanayo kwao atamuopsyeza kuti akamunenela ku polisi. Mayiyo akuti sakumvetsa kuti banjalo latha koma anthu ena ati nkutheka kuti mkazi wamkuluyo adakapeza kapasule kwa mkulu wina wazitsamba kuti ati azidya yekha mswahala omwe nyakwawayo imalandila. 

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter