Agwidwa ndi chibwenzi pa filling station
Mkulu wina anaona ngati malodza mkazi wake atamutukwana zamu nsalu pamene anamupeza ali ndi chibwenzi pa malo ena omwetsera mafuta ku Chilimba mu mzinda wa Blantyre. Nkhaniyi ikuti mkuluyo ali pa banja ndipo wakhala ndi mkazi wakeyo zaka zambili popanda kukayikilana kulikonse. Ndiye poti mtima wa nzako ndi tsidya lina, mayiyo wakhala akumva zoti mwamuna wakeyo ali ndi chibwenzi koma samakhulupilira mpang’ono pomwe. Patsikulo mayiyo amachokera ku Machinjiri ndipo ali m’minibus anaona galimoto ya mwamuna wakeyo ili pa Filling Station koma atayang’anitsitsa anaona kuti m’galimotomo muli mkazi yemwe pa nthawiyo amaseketsana naye mwachikondi. Posaugwira mtima maiyo anapempha adalaivala kuti atsike koma mkazi wachibwenziyo atangomuona, anatuluka m’galimotomo nkuliyatsa liwiro kuthawa. Anthu omwe anali pamalopo anayamba kumukuwiza koma akuti sanayang’ane m’mbuyo. Apa mkuluyo anadziwiratu kuti yachimwa ndipo pofuna kuonetsa mtima wogonja anayitana mkazi wakeyo mwaulemu kuti akwere galimotoyo azikambirana momwemo. Koma chifukwa chopsya mtima maiyo anamutukwana mwamuna wakeyo zamu nsalu zomwe zinaoneka kuti mwamunayo sanayembekezere. Mkuluyo anapitilizabe kupepesa mkazi wakeyo koma zinakanika moti aliyense anayenda ulendo wakewake. Sizikudziwika kuti kunyumbako zinatha bwanji koma anthu ena omwe akuwadziwa anthuwo, ati banjalo ndi lokondana kwambili ndipo nchachidziwikire kuti panopa anakhululukirana.
Agonana ndi bamboo ake omubeleka
Mtsikana wina akuyenda mogwetsa nkhope pansi mdela la makatani mu mzinda wa Lilongwe atamutulukila kuti wathetsa banja la mai ake chifukwa chochita zadama mdi bambo ake omubeleka. Nkhani-yi kwanthawi yaitali mtsikanayo wakhala akumachita zadama ndi bambo ake omubeleka. Koma mai ake akuti samakhulupilila nkhani-yi kufikila dzulo pamene anapezelela mtsikanayo akuchita zachisembwere ndi bambo ake. Pa chifukwa ichi, mai ake atuta katundu wao apita kwao kusiya mtsikanayo ndi bambo ake m’nyumbamo. Anthu ambili mdelalo akuti adzudzula zomwe mtsikanayo wachita ngakhale ati akukhulupilila kuti bamboyo chilipo chomwe akufuna kukhwimila mwana wake-yo. Malinga ndi amene watumiza nkhani-yi sizikudziwika kuti mai ndi mwana wakeyo azionana bwanji ngati onse atakumana kumudzi kwao.