You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma26/06/15

26/06/15

Written by  Newsroom

Banja lisokonekela kamba ka kovinisa

Banja lina latekeseka m’dera la Mfumu Mkanda mboma la Mulanje mkulu wina atapeza mkazi wake akuvina ndi mphongo zina m’mudzimo.

29
May

  Nkahniyi ikuti m’mudzimo munali mwambo wa zochitikachitika zomwe anakonza a bungwe lina lazachitukuko.  Pa mwambowo anakonza magule osiyanasiyana kuphatikizapo tchopa. Tsono mkaz wa mkuluyo atamva za mbowo anaganiza zopita komweko ncholinga choti akavine nawo guleyo.  A Tchopa atalowa m’bwalo mayiyo anatengeka mtima mpaka analowa m’bwalomo ndipo mkulu wina yemwe amavina mwa kaso anamupanilira mayiyo posalabadira kuti ndi mkazi wa mwino.  Mkuluyo ataona izi anangochoka pa bwalolo ndipo apa mpamene anathu anadziwiratu kuti yalakwa.  Anthu ena anamukodola mayiyo kumuuza kuti mwamuna wake wanyanyala koma mayiyo akuti sanaimve mpaka guleyo anatuluka m’bwalo.  Atakafika ku nyumba mayiyo anafikira m’naja kumuthobotsa ndi zibakera mpaka anathawa pa nyumbapo kukagona kwa achibale.  Pakadali pano banjalo lakhululukirana koma akuti mwamunayo walamula kuti mayiyo asadzapezekenso akuvina pa mwambo uli wonse m’mudzimo.

 

 

Mbava ikunthidwa itagwidwa ikuba chimanga

Mbava ina yotchuka ya m’mudzi mwa Mandolo  m’dera la Mfumu Kanduku mboma la Mwanza yaona zakuda atayikuntha kodetsa nkhawa pamene anayipeza ikuba chimanga m’munda mwa eni.  Nkhaniyi ikuti m’mudzimo muli mkulu wina yemwe ambiri amamudziwa kuti ndi tsinzinantole.  Kwa nthawi yaitali wakhala akuzunguza m’mudzimo komabe anthu amangodikira  kuti lidzamukwanire la 40.  Sabata yathayi mkuluyo anatasa kuba chimanga m’munda wina koma mwatsoka anthu ena odutsa m’njira anamuona.  Anthuwo anamuzembelera nkumugwira  ndipo apa sanayembekeze mwini mundawo koma kungoyamba kumuphika kwinaku akukuwa.  M’mene anthu ena amatulukira kumundako anamupeza mkuluyo ali  thapsya.  Anthu ena achifundo ndi omwe anamukwekweza kupita naye kwawo ndipo mwini mundawo atamva anayamika kwambiri anthuwo. Kuyambira pa tsikulo  Mbavayo ikungobuula mnyumba ndipo yalumbira kuti siidzabanso ati kamba koti yaona kuti anthu am’mudzimo ndi olimba mtima akhoza kudzamupha.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter