Nkhaniyi ikuti mayi wina m’mudzimo anadwala ndipo anthu ataona kuti matendawo ndi aakulu anaganiza zopita naye ku chipatala. Anthu akufuna kwabwino anapereka njinga yoti amunyamulirepo odwalayo ndipo chifukwa choti sakanatha kukhala yekha pa njinga, anthuwo amangokwawaza njingayo kwinaku ena atamugwirizira odwalayo. Tsono chautsa mapiri pa chigwa nchakuti mkatikati mwa amuna omwe amathandiza nawo pa ntchitoyo panali mkawini wina wapamudzipo yemwe amagwiragwira nchiuono mwa odwalayo. Anthu ena ataona izi anakodolana kuti awone zomwe mkamwiniyo amachita. Apa anthuwo anamudzudzula mkamwiniyo ndipo ena sanalekere pomwepo koma kukawadziwitsa agogo ake a odwalayo kumudzi. Zimenezi zinapsyetsa mtima gogoyo komanso achibale ena omwe anamuchenjeza mkuluyo kuti akapitiliza khalidwe lakelo adzaona chomwe chidameta nkhanga mpala.
Akhalira kuthawa mamuna wake mnyumba
Mboma lomwelo la Machinga koma m’dera la Mfumu Mchinguza, anthu akudabwa ndi zomwe zikuchitika m’banja lina pomwe mayi wa mnyumbamo akungokhalira kuthawa mwamuna wake. Nkhaniyi ikuti mkulu wina m’deralo anakwatira mayi wina yemwe anthu amamutayira ka mtengo kuti ndi chiphadzuwa komanso namadya bwino. Koma mayiyo wakhala akudabwitsa anthu m;mudzimo chifukwa cha khalidwe lake lomachoka pakhomopo wosatsanzika ndipo kumeneko amakhalako miyezi ingapo. Zimenezi zakhala zikuchitika kangapo konse koma chodabwitsa nchakuti mwamunayo samalankhula kalikonse mkaziyo akabwera komwe anapitako. Anthu ambiri m’mudzimo ati mwamunayo akufera maonekedwe a mkaziyo komabe ena ati akukhulupilira kuti mayiyo anadyetsa mwamunayo kondaine.