Nkhani-yi ikuti masiku apitawa mkulu wina anatuma nzake kuti akamusiile ndalama ku banki ndipo zimenezi zinachitikadi. Mkulu uja akuti anapatsidwa 115-Thousand Kwacha koma ali munjila anachotsapo 15-thousand Kwacha yomwe anathyolela mthumba. Kufika ku banki ali pamzele anapatsila mai wina yemwe amagwila naye ntchito moyandikana ndipo atafika posungitsa ndalama a banki anamuuza kuti ndalama sikukwana ndipo apa mayiyo anayesela kumimbila foni mkulu uja koma samayankha. Zitafika pothina anakafika ku ofesi kwao komwe onse anawaitanitsa koma mkulu uja amaumilila kuti mai uja wasololapo koma chonsecho lili bodza. Pa chifukwa ichi a banki anati sipanavute koma kutengela anthu onse mkachipinda kena komwe amakawaonetsa pa zithunzi zokhudza zinthu zochitika mu banki ndiopo zinaonetsa mai uja akulandila ndalama komanso akufika posiya ndalama. Mkulu uja ataona kuti zamuthina anaulula m’maso muli gwa kuti anathyolela mthumba ndalama ija ndikuti anagulila zofunikila zakunyumba. Panopa, mkuluyo amuuza kuti abweze ndalamayo koma akuti akukhala wamanyazi kwambili ndipo anzake ati sadzamutumanso ku banki chifukwa ndi kathyali.
Ayenda mwamanyazi kamba kochita chisembwere
Mkulu wina akuyenda mozemba m’dera la Mfumu Chikowi mboma la Zomba zitadziwika kuti amachita chisembwere ndimkazi wa mwini. Nkahniyi ikuti mwini mkaziyo amalawira kumunda m;mawa uli wonse nkusiya mkazi wakeyo kuti azigwira ntchito zina zapakhomo. M’malo moyamika chikondi cha mwamunayo, mayiyo anachita chibwenzi ndi mphomgo ina yoyandikana nayo nyumba. Patsikulo anthu awiriwo anagwirizana kuti akakomane ku nyumba ya mayiyo mwamuna wake akapita ku munda. Mphongo yakubayo inatchera nzakeyo ndipo atangonyamuka kupita kumundako anakagogoda pakhomo pa mayiyo nkulowa m;nyumbamo. Tsono chavumbulutsa mavu pa chisa nchakuti, mnyumbamo muli mwana wang’ono koma wodziwa kulankhula. Poopa kugwidwa, mayiyo anauza mwanayo kuti apite kwa bambo ake ang’ono pamudzi pomwepo ndipo anamunyengelera ndi chimanga chophika. Kumeneko anthu anadabwa kuona mwanayo kunja kusanache ndipo atamufunsa anaulula kuti kwawo kwabwera anthu ndiy mayi ake amuuza kuti akacheze ku nyumbako. Apa mlamu wake wa mayiyo anatsatira ku nyumbako nkukabisala pa malo ena kuti awone yemwe atuluke mnyumbamo. Posakhalitsa anaona mkuluyo akutuluka ndipo pofuna kumudziwitsa kuti anamuona anakhosomola mwa dala. Apa mkuluyo analiyatsa liworo kuthawa. Mwini mkaziyo atamva nkhaniyi palibe chomwe wachita kwa mwamuna nzakeyo koma m’malo mwake akumamutenga mkazi wakeyo kumundako tsiku ndi tsiku, pamen mwamuna wakubayo akuyenda mozemba poopa mwini mkaziyo.