Nkhani-yi ikuti ku Chilomoni kunali malilo ndipo kumanda kunapita adzukulu ochepa omwe amakagwila ntchito yokumba dzenje. Koma momwe zimachitika zimenezi nkuti achinyamata ambili ali m’makwalala kumwa mowa. Tsono nthawi itakwana kuti amai akupita ndi chakudya kumanda achinyamata ambili analunjika kumandako kukadikilila chakudya chidya kotelo kuti adzukulu omwe anagwila ntchito mokhulupilika amadandaula kuti sadakhute. Pa chifukwa ichi, nyakwawa ina mdelalo inaima kumanda kuuza anthu onse kuti sidzalola adzukulu kulowa kumanda nthawi ikangopyola 9-koloko chifukwa omwe akumapita panthawiyo akumapitila kuti akadye chakudya basi. Chomvetsa chisoni china mchakuti akuti adzukulu omwe amapita mochedwa kumandako ndi omwe amalalata ndiwo kapena chakudya chikachepa kapenanso ngati palibe ndiwo zankhuli. Pakadali pano, zamveka kuti adzukulu ena anawabweza atafuna kunyozela lamulo lomwe nyakwawa yakhazikitsa kuti adzukulu azitsatila.
Akwatira mayi ongofeledwa kumene
Mkulu wina mdela la mfumu Mchinguza mboma la Machinga amudzudzula atakwatila mkazi wa mbusa wina yemwe wangomwalila kumene. Nkhaniyi ikuti mkulu wina adakwatila khomo limodzi ndi mbusa wina ngakhale amaiwo adabadwa kuchokela kumabere osiyana. Koma masiku apitawa mbusayo anadwala mpaka kumwalila, ndipo mwambo onse utatha zinamveka kuti mwamuna nzake wa mbusayo akumafika pakhomo pa mbusayo usiku. Zitachitika zimenezi anthu am’mudzi anayamba kukambilana za nkhani-yi koma mkuluyo sizimamukhudza kufikila panopa awiliwo atengana ndipo mkuluyo tsopano ali ndi akazi awili apa chibale. Anthu ambili akuti akudzudzula mkuluyo ndipo ati ali mchikhulupililo kuti mwina akudziwa chomwe chidachitika pa nkhani ya imfa ya mbusayo. Panopa, zamveka kuti mkuluyo amukokela kubwalo la nyakwawa chifukwa chochititsa manyazi mudzi atamtulukila kuti wakwatila mkazi wamwamuna nzake komanso mlamu wake chonsecho anali asadamusudzule mkomwe. Pakadali pano, mkuluyo akuti akuyenda mogwetsa nkhope yake pansi chifukwa cha manyazi atadziwa kuti anthu akumuloza loza m’mudzimo.