Nkhaniyi ikuti mai wina anali pa banja lomwe amakhala mwa mtendere koma pa zifukwa zosadziwika banjalo linayamba kusokonekera. Yemwe watitumizira nkhaniyi wati mwamuna wa mayiyo amapita ku nyanja kukapikula nsomba. Tsiku lina anagwa mchikondi ndi mkazi wina oyendayenda ndipo anapangana kuti akakomane ku malo ogona alendo ku Nayuchi. Mwatsoka anangoti gululu ndi mlamu wache yemwe anagona komweko poyembekeza ma Transport opita ku Liwonde kuti akapikulitse nsomba zake. Mkangano unabuka mpaka kuyamba kumenyana. Pamenepa mkazi wakubayo anapeza mpata nkuthawa ndipo kenaka mlamu wakeyo anamupulumukanso nkuthawa. Tsiku lina mwamunayo anayimbira foni mkazi wakeyo kuti atenge katundu yense ndipo banja latha. Apa mnyamatayo atamva kuti mlamu wakeyo sadzafikanso pamudzipo, analamula mchemwali wakeyo kuti amupatse matchini ndi njinga zomwe anasiya mwamuna wakeyo. Zomwe akuchita mnyamatayo zakwiyitsa anthu ambiri mderalo ponena kuti alibe gawo ku chuma cha mchemwali wakeyo chifukwa m’banjamo muli ana asanu ndi awiri omwe anasiya mwamunayo.
Mtsikana wina akunthidwa kamba koyenda ndi mamuna wa eni
Mtsikana wina wapa sukulu ina kwa Mposa m’boma la Machinga amuswa kodetsa nkhawa atamupezelela ali mchikondi ndi mwamuna wa mwini. Nkhaniyi ikuti mkuluyo anatsegula malo ogulitsira mpunga ku malosa ndipo masiku apitawa anagwa mchikondi ndi mtsikana wapa sukulu ina yoyendera mpaka chibwenzi chao chinafumbila. Kwa nthawi yaitali mkuluyo amati akamaliza kugulitsa mpungawo amapita kwa makolo ake a mtsikanayo ndipo makolowo amamulandila mwa chimwemwe. Koma mbiri inawanda mpaka mwini mwamunayo anadziwa za nkhaniyi. Patsikulo mayiyo anapeza awiriwo ali jijili-jijili pa malo ena ogona anthu apaulendo. Posakhalitsa ndeu ya fumbi inabuka mpaka mwini mwamunayo anang’ambira zovala mtsikana wakubayo ndikumuvulaza mlomo. Mtsikanayo anapeza mpata wothawa anthu ena achifundo ataleretsa ndeuyo. Pakadali pano mphunzitsi wamkulu wapa sukulu yomwe akuphunzira mtsikanayo wamuitanitsa kuti akafotokoze bwino za mkanganowo pamene atsikana anzake apa sukulupo akumulozaloza chifukwa choyaluka ndi mwamuna wa mwini.