Nkhaniyi ikuti mai wina anamangilira mbuzi zake ku tchire komwe zimadya. Kenako mbavayo inazemba ndikuba mbuzi imodzi ndikukayimangirira ku mtsinje. Usiku mkuluyu anakatenga mbuziyo ndikuika mdengu kuti akagulitse koma atanyamuka anakhumudwa kuona kuti mdengumo munali chinjoka chachikulu chili fulukutu fulukutu, nthawi yomweyo mbavayo inagwa pansi nkukomoka. Usiku omwewo anthu ena anatengera mkuluyo kuchipatala china komwe anakaulula kuti anaba mbuzi ya mai wina . Anthu ena anakapempha maiyo kuti apite ku chapatalako kuti akaone odwalayo kuti mwina apeza bwino koma maiyo anakana ponenetsa kuti mbuzi zake zonse zikadali mkhola. Pakadali pano mbavayo siyinachre kwenikweni komabe yanenetsa kuti siyidzabanso.
Akuntha atate ake omupeza kamba ka nsanje
Mnyamata wina kwa Chiluzi m’boma la Dedza wathawa m’deralo atamenya atate ake omupeza chifukwa cha Nsanje. Nkhaniyi ikuti bambo wina anakwatila mai wina ndipo m’banjamo anapeza mwana wa mwamuna. Mnyamatayo wakhala akukhala ndi atate akewo kwa zaka zisanu popanda chovuta . Koma masiku apitawa mnyamatayo anakapapila bibida ndipo anayamba kulalatila atate akewo kuti achoke pakhomopo pomwe anati asiye ukwati mai akewo awasamala yekha. Bambowo akuti sanazitengere poganiza kuti mnyamatayo analedzera. Koma zinthu zinafika poyipa kwambiri pamene mnyamatayo anayimbila foni atate akewo ndikuwawuza kuti asamuke pa khomo-po chifukwa akusokoneza chikondi chomwe mai akewo amamupatsa komanso business yake ya grocery yasokonezeka. Kenaka atafika ku nyumba anangofikira kukuntha atate akewo mpaka thapsya. Pamenepa mnyamatayo atazindikira kuti atate akewo akomoka anathawa osabweleranso. Pakadali pano anthu ambiri mderalo akuganiza kuti mwina mai-yo anakhwimirana ndi mwana wakeyo ncholinga choti bizinesi ya golosaleyo idziyenda bwino.