You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma19/05/15

19/05/15

Written by  Newsroom

Mayi okonda zopemphera agwidwa akuchita zadama
Mayi wina wodziwika bwino ndi nkhani zopemphera ku Urongwe mboma la Balaka wakhumudwitsa anthu atagwidwa akuchita zachisembwere kunja kutachita kachisisila chakumadzulo  mtchalichi ina yomwe iye sapempherako.

19
May

Nkhaniyi ikuti kwa mfumu yayikulu Amidu mbomalo mayi wina amasintha amuna ngati mashati, chikhalirenicho mayiyo ndiwodziwika kwambiri pa nkhani zokhala chifupi ndi Mulungu. Anthu mderalo akhala akumudzudzula paza khalidwe lakelo, koma iye amaziponyera ku nkhongo. Paja amati chouluka chidakomana nchokwawa, tsiku lina mwachizolowezi mayiyo anagwirizana ndi Mtumiki wina wodziwa kugawa mau a Mulungu kuti akachite zachisembwere mchalichi china mderalo.  Ali mkati mwachikondi bambo wina yemwe amasamala pa mpingopo anaona ngati kutulo atapezerela anthuwo akuchita za nyansizo, koma iwo samamuona  bamboyo. Apa atakauza anthu ena kuti adzaone za malodzazo, apa ndi pamene anayamba kuphaphalitsa anthuwo ndi makofi. Pothawa anthuwo anasiya zovala za mkati ndi zinthu zina. Pakadali pano anthu awiri onyazitsa ntchito ya Mulunguwo sakudziwika komwe ali.

 

 

Bishop akakamila mkazi mpaka kutheta banja lake

Anthu a mdera la Tsabango m’boma la Lilongwe adzudzula zomwe achita Bishop wa mpingo wina mderalo pokakamila mkazi wa membala wina mpaka nkuthetsera banja lake . Nkhaniyi njakuti mwini mkaziyo yemwe amagwira ntchito yaulonda wakhala akudzudzula za makhalidwe oyipa a mkazi wake , koma iye sanafune kusintha. Tsiku lina mayiyo anatengana ndi anthu ena amu mpingowo kupita ku Blantyre kumapemphero pamodzi ndi Bishopyo, koma gulu lomwe linatsagana ndi anthuwo linayamba kukayikira za mayendedwe a mkulu wa mpingowo ndi mayiyo. Atabwerela ku Lilongwe anthu ena ofunila zabwino bamboyo anafotokozera nzawoyo za nkhaniyi, ndipo iye atafufuza bwino anapeza kuti nkhaniyo inali yoona. Mayiyo m’malo moti apepese mwamunayo anamuuza bamboyo m’maso muli gwa kuti banja sakulifunanso. Apa bamboyo anadziwa kuti mayiyo waponda mwala. Pakadali pano Mkulu woyang’anila nkhosa za Mulunguyo amupezera lendi mayiyo ndipo akukhala ngati banja, chikhalireni ali ndi banja lake. Anthu apa mpingopo akamang’ala ku likulu la mpingowo kuti Mkuluyo amuchotse pa udindo komanso pa mpingowo chifukwa choti wanyazitsa Ufumu wa Mulungu.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter