Watitumizila nkhaniyi wati mkulu wina adakwatila mai wina yemwe anali ndi mwana kale wamkazi. Mkuluyo amakhala ndi mwanayo kufikila anakula bwino lomwe kotelo kuti amuna anafika pomamufuna koma bambo omupezayo amatchingila kwambili ponena kuti salola amuna ena kuti amukwatile ndipo anthu amadabwa ndi sanje yomwe mkuluyo amachita. Koma masiku apitawo mkuluyo anakhumudwa kwambili mpaka wachoka pa chikamwinipo atamva kuti mtsikanayo ndi woyembekezela ndipo akukamutula. Pa chifukwachi, mkuluyo akuti wakwiya kwambili kuti mimbayo amupatsa ndi amuna ena. Koma anthu ambili akudzudzula malume ake a mtsikanayo omwe amaikila kumbuyo mkamwiniyo kuti atha kuchita chibwenzi ndi mtsikanayo. Mwa zina, mkamwiniyo adagulila alamu akewo njinga ya moto kuti awathandize kuti agwe mchikondi ndi mwana wake omupezayo. Panopa mkuluyo wachoka pa chikamwinipo ponena kuti adzabwela pokhapokha ngati mtsikanayo atakhalabe pakhomopo kumuletsa kuti asapite kwa mwamuna yemwe wamupatsa mimbayo kwa Lemu mdelalo. Pakadali pano, mkuluyo akuyenda zamadulila chifukwa chamanyazi atadziwa kuti anthu ambili amutulukila kuti amanyengelela kuti azigona ngati banja ndi mwana wake omupeza.
Ayenda tang'atang'a kamba kokuba
Mwamuna wakwa Mankhaka mdela la Mfumu Kaomba mboma la Kasungu akuyenda tang’atang’a chifukwa choba ndalama za mwini. Nkhaniyi ikuti mdelalo munali anthu awili omwe akhala akukonda kwambili. Wina akuti wakhala akugula mbewu zosiyanasiyana koma nthawi zonse amatha kumuuza nzakeyo zomwe iye akuchita komanso amadziwa pomwe nzakeyo amasunga ndalama. Tsiku lina nzakeyo ali kogula mbewu anasiya m’nyumba ndalama yokwana 80-thousand Kwacha ndipo makiyi anasiila nzake. Nzake uja kuona m’buyo muno anangoti laponda lamphawi diwa ndipo anathyolela ndalama yonse ija mthumba nkusowa mdelalo. Nzake uja atabwela kugeni anadzidzimuka kupeza chitseko chili chotsekula ndipo kufufuza pomwe anaika ndalama anapeza pali ntchentche zokha nzakeyo atachitilapo chimbudzi. Pa chifukwa-chi mwina ndalama uja anapita kwa mkulu wina wa zitsamba komwe amuthandiza ndipo m’mawa wa dzana momwe kumacha nkuti wakuba uja atafika mdelalo akuyenda motang’adza miye ndo yake chifukwa cha zotupa ngati chitumbuwa zomwe zamutuluka mphechepeche. Panopa, akuti ngakhale buluku likumuvuta kuvala ngakhale anasyesela kupita kwa nzakeyo kukamuuza kuti wamubela ndalama iye akukanitsitsa ponena kuti ndalama zake zonse zilipo. Iye anachita zimenezi kamba koti poyambilila atamufunsa za ndalama adakana kuti sadabe. Panopa mkuluyo akulila usiku ndi usana ngakhale anthu ena amulangiza kuti apite akapepese kwa nzakeyo.
Apeza zodabwisa mu nyumba ya lendi
Chipwilikiti chinabuka pa nyumba ina kwa Safalao ku Ndirande mu mzinda wa Blantyre mai wina atapeza zinthu zokhala ngati mwana wa nkhanda m’nyumba ya lendi yomwe wangolowa kumene. Nkhaniyi ikuti banja lina lalowa nyumba ya tsopano pa 1 August koma tsiku lina mai wam’nyumbamo akusesa kukonzekela kukolopa anangoona simenti waguvukila. Kufufuza anapeza kuti panali chigaza cha mutu wa mwana komanso ziwalo zina. Pa chifukwachi, mayiyo anazizidwa kwambili mpaka nkhaniyi inafika kwa nyakwawa koma mpaka ku polisi. Zinthuzo akaziika kumanda ena aku Ndirande komweko. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi anthu ena aulula kuti mai wina yemwe wasamuka m’nyumbamo ndiye akumuganizila kuti adakwilila khandalo kamba koti mimba yake yomwe inali yotopa kwambili inazimilila osadziwika bwino. Anthu ena ati mayiyo adabwerekaponso khasu usiku kunena kuti ati madzi aphulika ndipo zimenez ndi zomwe zikutsimikiza kuti mayiyo atha kudziwapo kanthu panopa mayiyo akuti adasamukila mboma la Salima. Pa nyumbayo panakhamukila anthu ambili kuti akadzionele okha zamalodzazo. Panopa, anthu omwe akukhala mu nyumbayo akuti akukhala mwa mantha kwambili chichitikile nkhaniyi poona ngati malodza.