07/09/17

Written by  Newsroom

Azitsekera mnyumba kuopa zibagera

Mwamuna wina mdera la Chikowi m’boma la Zomba zinamukoka manja atazitsekera mnyumba kuopa zibagera  zochokera  kwa mkazi wake.

07
September

Nkhaniyi ikuti  mwamunayo ndi odziwika kwambiri pa nkhani yolimbikitsa chitetezo mderalo koma vuto la mwamunayo ndiwa  nchuuno ndipo akhala akusokoneza mabanja a weni kuphatikizapo ana asukulu. Pa chifukwachi anthu akamulangiza  wakhala akuyankha kuti akazi ambiri mderalo amakhalira kumufunsila zomwe ndi bodza la nkunkhuniza.  Masiku apitawa mwamunayo anapalana ubwenzi wa mtseri ndi mtsikana wina wapa sukulu yoyendera   mpakana kumuchitila lendi. Mphekesera itamupeza mkazi wake anapita kunyumba komwe amakhala mtsikanayo ndikumpeza ali ndi mwamuna wake ndipo apa ndeu ya fumbi inabuka  koma anyamata akabaza ndi omwe analeletsa ndeuyo. Apa mwamunayo anapeza mpata othawira kunyumba kwake ndikukadzitsekera  kuopa mkwiyo wa mkazi wakeyo. Mkaziyo  atapita kunyumbako anapeza kuti nkokhoma koma anthu ena amunong’oneza kuti njondayo inadzitsekera. Apa njondayo zinamukoka manja mpakana kulephera kutuluka kuti akadzithandize komanso kukodza kuopa zibagera. Chipwilikiti chinabuka pakhomopo ndipo mwamunayo anakwanitsa kuthyola  khomo la kumbuyo lomwe  simatsegulidwa. Pakadali pano mwamunayo akukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha m,anyazi ndi nkhaniyi.

 

 

Alepheretsa chinkhoswe cha ntseri

Nyakwawa ina   ku Area 49 mu mzinda wa Lilongwe yayamikira  anthu ena mderalo  chifukwa cholepheretsa chinkhoswe cha ntseri.  Nkhaniyi ikuti telala wina mderalo yemwe ndi katswiri pa ntchito yake akhala akudzudzulidwa kuti wakhala akusokoneza mabanja a weni.  Mwa zina telalayo sachedwetsa pa nkhani yofunsila mai aliyense yemwe angafike pa malo ake anthito. Izi zakhala zikuchititsa kuti banja lake lisamayende bwino ndipo mkazi wake akamudandaulira amayankha kuti ngati watopa ndi banja akhoza kupita kwao pamodzi ndi ana atatu omwe iwo anabereka.  Chifukwa chotopa ndi nkhaniyi mkaziyo amangokhalira kupemphera kwa Mulungu kuti tsiku lina adzayankha.  Masiku  apitawa telala uja anakonzekera kuchita chinkhoswe ndi mkazi wina ndipo patatsala tsiku limodzi kuti mwambowo uchitike anthu ena ofuna kwabwino ananong’oneza mkazi wa mwamunayo za chilinganizocho.  Apa mkaziyo kuphatikizapo anzake, achibale komanso nthumwi za nyakwawa anapita kunyumba komwe amakonzekera za mwambo wa chinkhoswecho. Zinali zomvetsa chisoni atapeza kuti nkhaniyi inali yoona chifukwa mwa zina anakapeza katundu wokonzekera mwambowo.  Atamukokera ku bwalo la nyakwawa mwamunayo anangoti kukamwa yasa kusowa choyankhula. Pakadali pano telalayo wasowa mderalo.

 

 

Namfedwa wina awona zodabwisa

Anthu a mdera la Kaphuka m’boma la Dedza akukhala mwa mantha chifukwa cha zomwe zinamuchitikira nafedwa wina. Nkhaniyi ikuti mderalo munthu wina yemwe anali otchuka pa nkhani yazitsamba wakhala akudwala kwa nthawi yayitali ndipo matenda atakula anatsamila nkono. Mwambo onse oika zovuta unayenda bwino lomwe popanda chovuta koma chomwe chinazwizwitsa anthu omwe amachokera ku manda mchakuti m’modzi mwa anafedwa  anayamba kuyenda dzandidzandi mpakana kugwa pansi. Pa chifukwachi anthu anatengera munthyo kunyumba ya siwa.  Koma atamufunsa kuti alongosole pa zomwe zamuchitikirazao nafedwayo   sanabise Chichewa koma kuuza anthuwo kuti Mzimu wa malemuyo umamudzudzula kuti anayamba kale kumuuza kuti adzaike zovala zake mbokosi zomwe iye amazikonda kwambiri  koma sizinachitike. Kupatula apo anamudzudzulanso kuti pa maliro ake sipanavinidwe gule yemwe amamafuna ndipo m’masomphenya mzimu wa malemuyo unachenjeza munthuyo kuti ngati izi sizichitika aona pomwe adameta nkhanga mpara. Pamene timalandila nkhaniyi mikoko yogona komanso anafedwa akukonza mwambo wa chikumbutso ndipo anenetsa kuti pa tsikulo adzachita zomwe malemuyo ananena. Anthu ambiri mderalo ati akukhala mwa mantha chifukwa cha nkhaniyi.

 

 

Mai wina alilephera banja

Mai wina ku Ekwendeni mu mzinda wa Mzuzu wamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti banja walilephera. Nkhaniyi ikuti mwamuna wa mkaziyo anamwalira zaka zingapo zapitazo ndipo m’malo mwake anapalana ubwenzi ndi mpondamatiki wina wa  mdziko la Tanzania mpaka kumanga oyera.  Koma kwa nthawi yayitali mkaziyo wakhala akupilira pa nkhanza zosiyana-siyana zomwe mwamunayo wakhala akumuchitira  kuphatikizapo nkhani zakuchipinda komanso zamatsenga .  Pa chifukwachi maiyo wakhala akudandaula kwa anzake komanso kwa achibale , koma anthuwo sanabise Chichewa koma kukumbutsa maiyo kuti iye wakhala akunena kuti akufuna kukwatilana ndi mwamuna olemera. Choncho anamutsimikizila kuti asadandaule chifukwa nzochita kufuna. Mkaziyo anachoka pa khomopo pakati pa usiku mwamunayo ali mtulo ndikuthawira kwa achibale ati ponena kuti akapume ku zolemetsa.  Anthu ena opemphera  akumbutsa maiyo kuti yemwe amapuma ku zolemetsa ndi munthu wakufa yekha yemwe wachita bwino pa maso pa Mulungu akadali ndi moyo.   Maiyo pakadali pano akukhalira kutandala mnyumba chifukwa cha manyazi chifukwa nkhani yake ili mkamwa-mkamwa mdera lonselo. 

Get Your Newsletter