31/08/17

Written by  Newsroom

Anamiza mamuna kuti ali ndi pathupi

Mai wina kwa Ndakwera mboma la Chikwawa amuthamangitsa pa ukwati zitadziwika kuti amanamiza mwamuna wake kuti ali ndi pathupi.

31
August

Nkhaniyi ikuti mayiyo anakwatiwa zaka zingapo zapitazi ndipo amakhala ndi mwamuna wakeyo kwawo ngati mtengwa. Ataona kuti zaka zikupita opanda mphatso ya mwana, anayamba kulingalira mapulani woti anamize mwamuna wakeyo kuti ali ndi pathupi ati kuti asamusiye ukwati. Izi zinachitikadi ndipo mayiyo anauza mwamuna wake kuti ali ndi pathupi ndipo akuti mimbayo imakula monga amachitira amayi akakhala woyembekezera. Yemwe watumiza nkhaniyi watinso mayiyo amatsanzika mwamuna wake kupita ku sikelo kuyambira miyezi yoyambilira mpaka kumapeto kwinaku akumasala zakudya zina zomwe zimachititsa kuti mwamunayo asamukayikire. Itafika nthawi yochira mayiyo ananyamuka ndi amayi ena omwe anamunamiza za mapulaniwo kupita ku chipatala ndipo kumeneko anakachotsa masanza omwe anamanga pamimbapo nkuimbira lamya mwamuna wake kuti wapita pachabe. Ndiye poti padziko lapansi palibe chinsisi, mwamuna wakeyo ndi achibale ena anapita kukafufuza kuchipatalako koma zinali zokhumudwitsa ndi zochititsa manyazi kumva kuti mayiyo sanafike kuchipatalako komanso sanayenderepo sikelo. Pachifukwachi, mwamunayo wathamangitsa mkaziyo komabe ena akumudzudzula kuti zinali zogwirizana kamba koti mwamuna wachikondi amaona momwe mkazi wake akusinthira akakhala woyembekezera.

Mwambo wa maliro osokonekela
Mwambo wa Maliro a gule wina wamkulu unasokonezeka m’mudzi mwa Kangumbwe kwa T/A Chadza mboma la Lilongwe. Yemwe watitumizira nkhaniyi wati m’mudzimo munachitika Maliro a gule wamkulu ndipo monga mwa mwambo anthu ambili anasonkhana kuti akaonelere mwambo wa malirowo. Mwambowo utayambika, anthu anali ndi chidwi ndi mphekesera zomwe zimamveka kuti malemuyo anauza adzukulu ake awiri zodzachita pa mwambowo. Mwa zina malemuyo anauza adzukulu akewo kuti akawaze mankhwala chitandacho asanatsitsire m’dzenje komanso asananyamule m’nyumba ya siwa. Anthu ambili makamaka amayi anali ndi chidwi ndi zonmwe zimachitikazo ndipo pachifukwachi amayandikira komwe kumachitika mwambowowo. Pamenepa gule wamkuluyo anapsya mtima ndipo anayamba kulimbana ndi amayiwo kuti asayandikire pa dzenje lamandalo. Apatu amayiwo sanalole koma kuyamba kukankha gule wamkuluyo mpaka anachoka chothawa pamalopo. Pakadali pano nkhani ili mkamwamkamwa ndiya adzukulu a malemuyo pomwe anthu akuwanena kuti anawasiyira nyanga.

Gogo apeleka pathupi kwa mdzukulu
Gogo wina ku Malomo m’dera la mfumu Chilooko mboma la Ntchisi wakhumudwitsa anthu atapereka pathupi kwa mdzukulu wake. Nkhaniyi ikuti gogoyo anayamba kukhala ndi mwanayo pakanthawi ndipo atafika mu Standard 6 anamuuza kuti asiye sukulu ncholinga choti azisamala chuma. Masiku apitawa zadziwika kuti mtsikanayo ndi woyembekezera ndipo mikoko yogona itamufunsa mwini pathupipo anaulula kuti amupatsa ndi agogo akewo. Izi zinakwiyitsa akumpingo kwa gogoyo ngakhalenso anthu ena omenyera za ufulu wa ana m’deralo. Anthuwo anagwirizana kuti amutengere mkuluyo ku polisi koma mphepo itamupeza gogoyo wasowa m;mudzimo moti komwe akukhala sikukudziwika ngakhale ena akuti akumapezeka usiku okhaokha pakhomopo.

 

Mayi wina apasula banja kamba kazadama

Tili ku Lilongwe komweko koma ku area 25 mayi wina wapasula banja chifukwa cha chimasomaso. Nkhaniyi ikuti mayiyo anakwatiwa ndi mwamuna wina zaka zingapo zapitazi koma chifukwa chosakhutitsidwa anayamba kuzemberana ndi amuna ena. Mchitidweu utamera mizu mwa mayiyo, anatayilira mpaka kumakumana ndi zibwenzi zakezo mopanda mantha. Tsiku lina mwamuna wake anamupezelera ali ndi chibwenzi chake china ndipo apa analephera kuugwira mtima mpaka anayamba kuponyerana zibakera. Mwatsoka mwini mkaziyo amachepera mphamvu moti anamuvulaza kwambili. Achibale ake a mwamunayo atamva nkhaniyi anapita kukamulongedzetsa katundu mlamu wawoyo dzuwa likuswa mtengo moti tikunena pano mayiyo wapita kwawo.

 

Mwana wina atandala ku depot ku Zomba

Mwana wina ku Zomba akutandala pa depot ya Bus podikilira mai ake omwe anamwalira. Chomwe chachitika nchoti mai a mwanayo amadwala ndipo patapita masiku anamwalira. Mwambo onse wa Maliro unayenda bwino ndipo tsiku lobalalika pa siwapo, mng’ono wawo wa malemuwo anadzipereka kuti amutenga mwanayo kuti adzikamulera. Patangopita masiku ochepa mwanayo anasowa pa khomopo mpaka chaka chatha osapezekanso. Mwadzidzidzi mwanayo wapezeka mu mzinda wa Zomba akungoyendayenda. Chokhumudwitsa kwambiri ndi choti mwanayo akumapezeka pa malo ena omwetsera mafuta ndipo akungothamangira minibus yomwe ingafike pa malopo ndikuuza dalaivala kuti akufuna mai ake omwe ali m’minibusmo. Mwanayo anaopsyezanso dalaivala wina kuti atentha galimotoyo ngati mai ake sawatsitsa. Pakadali pano nkhnaiyi yakhumudwitsa anthu ambili makamaka omwe akumudziwa mwanayo pomwe ena ati nkutheka kuti mwina malemu mai a mwanayo anamwalira ndi imfa ya matsenga.

Get Your Newsletter