30/08/17

Written by  Newsroom

Mwamuna wina atandala mnyuma kamba ka manyazi

Mwamuna wina mdera la Mazengera m’boma la Lilongwe akukhalira kutandala mnyumba chifukwa cha manyazi ndi zomwe zamuchitikira.

30
August

Nkhaniyi ikuti mwamunayo wakhala akugwira ntchito yaulonda pa sitolo ya mpondamatiki wina mderalo kwa nthawi yayitali . Komabe chodabwitsa mwamunayo akalakwitsa kanthu mwini sitoloyo samamudzudzula mwamunayo zomwe zakhala zikukaikitsa anthu kuti anthu awiriwo amagwirizana pa zinthu zina. Masiku apitawo mwamunayo anamupezerela atasongoka mlomo uku ali buno-buno mchigawo cha munthu wina chaku mbandakucha. Izi zinali chomwechi chifukwa mlonda mzake yemwe amalondole pa chigayocho naye pokhala kuti ngodziwa zitsamba anapezerela mzakeyo ataona mwamunayo m’matsenga. Pomufunsa mwamunayo anangoti kukamwa yasa kusowa choyankhula koma atamuwaza mankhwala mwamunayo anayamba kubwebwetuka kuti wakhala akutumidwa ndi bwana wake kuti adzimubera zinthu m’matsenga. Mikoko yogona komanso aza chitetezo ataitanitsa bwana wakeyo anthuwo anagwidwa nkhongono pomva kuti bwanayo ali mdziko la Mozambique zomwe zinapereka chikaiko kuti bwana wa mwamunayo naye ndi nthakati. Ku bwalo la nyakwawa mwini chigayocho anakhululukira mwamunayo ndipo pakadali pano akukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.

Anthu akhala mwa mantha

Tili m’boma lomwelo la Lilongwe kwa Chadza anthu mderalo akukhala mwa mantha ndi zomwe zachitika panyumba ina ya siwa. Nkhaniyi ikuti mderalo munthu wina anadwala ndipo matenda atakula anamwalira. Mikoko yogona mogwirizana ndi nyakwawa ya mderalo analengeza za zovutazo ndipo anthu ambiri anafika mwauchinji pa maliropo. Koma chodabwitsa komanso kuchititsa mantha galu wina analowa mnyumbamo nkuyamba kuseweretsa mtembo. Anthu omwe anali pa siwapo anagwidwa ndi mantha aakulu chifukwa malowedwe a galuyo palibe anamuona chikhalireni pakhonde ponsepo panali a mpingo ndi anthu ena. Anthu ena olimba mtima anayamba kuthamangitsa galuyo koma akanadziwa sakanatero chifukwa galuyo analusa kwambiri mpakana kubalalisa anthu omwe anafungatila chitanda uku akufuna kuwaluwa. Posakhalitsa anyamata ena okwiya anakwanitsa kugwira galuyo ngati m’mene tichitila mbuzi uku akumumenya ndi zitsulo komanso zipika za nkhuni. Malinga ndi yemwe watitumizila nkhaniyi wati anthu omwe anali pa siwapo sakukaika kuti zachitika m’matsenga komanso kuti nzochititsa mantha. Mikoko yogona mogwirizana ndi anafedwa agwirizana kuti apeze cheni-cheni pa nkhaniyi. Pakadali pano sizikudziwa kuti nkhaniyi yatha bwanji.

Ndewu ibuka pakati pa mayi wina ndi mtsikana

Ndeu yopanda oleletsa inabuka pakati pa mai ndi mtsikana wina yemwe ndi apachibale mdera la mphonde mboma la Nkhota-kota. Maiyo akhala ali pa banja kwa nthawi yayitali koma mphuno salota osadziwa kuti mwamuna wake wakhala ali pa ubwenzi wa ntseri ndi mwana wa mchimwene wa mwamunayo yemwe ndi mtsikanayo. Kwa nthawi yayitali maiyo akhala akuuzidwa za nkhaniyi koma samakhulupilira ndipo amatsimikizila anthu ambiri kuti akungofuna kuipitsa mbiri ya mwamuna wake. Chifukwa choti anthu ambiri kuphatikizapo amzake a maiyo akhala akumuuza za nkhaniyi maiyo anakonza pulani yofuna kupeza choona pa nkhaniyi. Tsiku lina maiyo anatsanzika mwamuna wake kuti akupita ku mapemphero omwe mpingo wao unakonza ndipo mwamunayo anali mchimwemwe chodzadza tsaya. Pa chifukwachi anaitana mwana wa mchimwene wakeyo kuti adzacheze kuti kwinaku agwirizane za tsogolo la mwana yemwe mtsikanayo anabereka ndi atate akewo. Macheza ali mkati maiyo mogwirizana ndi amuna ena adzitho anafikira kuthyola chitseko ndipo mwa manyazi anapeza mwamunayo ndi mtsikanayo ali maliseche. Apa mtsikanayo sanaimve koma kugwirana ndi maiyo koma chodabwitsa anyamata aganyu aja sanalowerele kufikira anthu aja anatopetsana kenako analeletsa nkhondoyo. Ku bwalo la milandu mwamunayo komanso mtsikanayo anamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sasiyana ndipo maiyo wathetsa banja ndi mwamuna wakeyo.

Mtimiki wa Ambuye achita zodabwisa

Anthu apa mpingo wina mdera la Sub T/A Ngwerelo m’boma la Zomba ati sakumvetsa ndi zomwe wakhala akuchita mtumiki wina wa Ambuye wapa mpingopo. Kwa nthawi yayitali anthu apa mpingopo akhala akuuzidwa kuti Gulupayo amakhalira kupanilira mowa wa mkarabongo m’malo ambiri omwera mowa mderalo. Nkhaniyi yakhala ikuipila mamembala ambiri komabe ambiri a iwo amangoti Mulungu yekha ndiye adziwa. Tsiku lina mwambo wa mapemphero unasokonezeka mkuluyo atayamba mkonono pa nthawi yolalikira chifukwa chogona ndi mowa m’mutu. Pa chifukwachi mamembala ena amuna apa mpingopo akhala akuyendayenda m’malo ena omwela mowa ndipo anatsala pang’ono kulira ataona mtumiki wa ambuyeyo atapanilira chipanda cha mowa uku atakhumbatila akazi awiri oyenda-oyenda. Apa mamembalawo anatsimikiza kuti zomwe akhala akumva ndi zoona kuphatikizapo kuchita maubwenzi a ntseri ndi akazi apabanja apa mpingopo. Nkhaniyi itakafika ku likulu la mpingowo, mtumikiyo ayamba amuchotsa pa mpingo chifukwa mwa zina tsiku lina mwamunayo anagona kutsogolo pa nthawi yomwe iye amalalikira. Ngakhale izi zili chomwechi anthu ambiri mderalo adzudzula mamembala apa mpingowu kuti akanangopepherela kwambiri gulupayo komanso kumusalira chakudya m’malo mokamufuna-funa ku mabala ati chifukwa choti sizikuthanthauza chili chonse. Malinga ndi yemwe watitumizila nkhaniyi ati mtumiki wa Mulunguyo ndi otchuka kwambiri pa mau ake achikoka olangiza nkhosa za Mulungu kuphatikizapo kuphunzitsa anthu zakubadwa kwatsopano komanso malilime.

Get Your Newsletter