11/08/17

Written by  Newsroom

Mwamuna wanchiuno avulalitsa mkazi wa chibwenzi
Mwamuna wina wa mchiuno wapa mudzi wa Chiphe kwa Kachere m’boma la Dedza wavulalitsa chibwenzi chake cha nseri.

11
August

Nkhaniyi ikuti mwamunayo yemwe akukhala ku chikamwini pa mudzipo anapalana ubwenzi wa nseri ndi mkazi wina wapa mudzi wa Chimombo womwe ndi woyandikana ndi komwe amakhala. Chibwenzi cha awiriwo chitafumbira mwamunayo amapereka kwa mkaziyo zinthu zosiyana-siyana kuphatikizapo ndalama pokometsera ubwenzi wao. Tsiku lina mwamunayo anakaba nyemba ku nyumba kwake ndikukapereka kwa mkazi wachibwenziyo. Anthu ena anatsina khutu mwini mwamunayo yemwe mosakhalitsa analondola ku nyumba kwa mkazi wachibwenziyo ndikukachita nkhondo mpaka kuvulaza paliwombo mkazi wakubayo ndi duka la njerwa. Mwini mwamunayo anaphulanso mpoto wa nyemba pamoto ndikulunjika nawo ku nyumba kwake komwe anafikira kukapiza nyemba za moto kwa mwamuna wake. Kamba ka izi mkangano unabuka m’banjalo zomwe zinachititsa mwamunayo kufumuka pa nyumbapo kupita kwao. Nkhaniyi inakafika ku polisi komwe mwamunayo inakamufera kamba komenyanitsa akazi, ndipo amulamulanso kuti alipire chindapusa cha 4-thousand Kwacha. Ngakhale mwamunayo akukhala kwao koma akuzemberanabe ndi mkazi wachibwenziyo.Koma alongo ake a mwamunayo aopsyeza kuti akhaulitsa mkazi wakubayo akapitiriza kusokoneza banja la mlongo wao.

 

Aphunzitsi achilapa kufunsira ana asukulu

Aphunzitsi atatu apa sukulu ina ya Private mtauniship ya Bangwe mu mzinda wa Blantyre anenetsa kuti sadzafunsiranso chibwenzi atsikana pasukuluyo. Watitumizira nkhaniyi wati aphunzitsiwo amakakamiza atsikana ena pasukulupo kuti akhale nawo paubwenzi ndikuwaopseza kuti ngati salola, awalepheretsa mayeso. Ndipo atsikanawo anakafotokozera nkhaniyi mwini sukuluyo yemwe anayitanitsa aphunzitsi atatuwo. Atawapha ndi mafunso pa nkhaniyi anavomeradi m’maso muli gwa kuti anafunsiradi atsikanawo. Izi sizinasangalase mwini sukuluyo ndipo anawafunsa aphunzitsiwo kuti asankhe chinthu chimodzi kuwatengera ku polisi kapena awalange yekha. Aphunzitsiwo anasankha kuti alangidwe ndi mwini sukuluyo. Kenako mwini sukuluyo anatsekera aphunzitsi atatuwo mu office yake pasukulupo ndikuwakwapula zikwapu makumi-awiri aliyense. Kenako iye anayamba kukwapula aphunzitsiwo m’matako ndi ndodo mpaka zikwapu twenty’zo. Atamaliza, aphunzitsiwo analephera kuyenda ndipo anangogona kwala mu office’yo mpaka madzulo ana onse ataweruka. Kenako iwo anazikwakwaza mpaka kukafika m’makomo mwawo. Malinga ndi yemwe watitumizira nkhaniyi, ati aphunzitsiwo sakupitanso ku sukuluko kamba koti akulephera kukhala pansi ati kamba koti atupa zokhalira.

Agalu achita zodabwitsa

Anthu apa mudzi wa Mpale kwa Nankumba m’boma la Mangochi ati ndi wozizwa ndi zomwe akuchita agalu ena awiri pa mudzipo pokhala pa mitala. Watitumizira nkhaniyi wati anthu akuba anakaba ku banja lina pa mudzipo chikhalirecho ku banjalo kuli galu. Eni galuyo anazindikira kuti izi zachitika kamba koti galu waoyo amadwala ndipo atafotokozera nkhaniyi banja lina lomwe amagwirizana nalo sanachitire mwina koma kuthandiza banjalo popereka agalu awo awiri. Banja lomwe analiberalo limakhala chakummtunda pamene lomwe linabwereketsa agalulo limakhala chaku Nyanja pa mudzi pomwepo. Banja lomwe linabwereka agalulo linamangilira agaluwo pa chingwe kwa mwezi wathunthu kuti azolowere. Ndipo pakutha pa mwezi umodzi agaluwo anayamba kuwamasula, koma chodabwitsa nchakuti agalu wonse anapita kwa mbuye wao ndikukakhalako masiku anai pakutha pa masiku anai agaluwo anabweleranso komwe anawabwereketsako ndikukakhalanso masiku anai. Kuyambira pa nthawiyo mpaka pano agaluwo akuyendetsa mitalayo pa ntchito yolondera nyumba za mabanja awiriwo, zomwe anthu ena akudabwa nazo.

Get Your Newsletter