10/08/17

Written by  Newsroom

Banja litha dzuwa likuswa mtengo

Mai wina mdera la Kasisi m’boma la Chikwawa manja ali ku nkhongo banja lake litatha dzuwa likuswa mtengo.

10
August

Nkhaniyi ikuti maiyo mwamuna wake anapita mdziko la South Africa kogwira ntchito ndipo ali ku Joniko wakhala akutumiza ndalama zoti amangitsire nyumba ndipo ntchitoyo imayenda. Maiyo chifukwa chosaugwira mtima anapalana ubwenzi ndi m’modzi mwa amuna omwe amamanga nyumbayo ndipo ubwenzi utafika pofumbila mkaziyo amachita mkomya kwa mphongoyo pomuonjezera malipilo ake komanso kumugawira zinthu zina zomwe mwamuna wake amatumiza kuchokera ku Joni. Mphuno salota ngakhale maiyo amachita mkomya, mwamunayo anapalananso ubwenzi ndi mai wina mderalo. Mphekesera itamupeza maiyo anayamba kuchitila nsanje mkazi winayo mpakana kumuophyseza pomulembera kalata pomuuza kuti asamusokonezere ufulu wake. Mkazi winayo atalandila kalatayo sanachedwe koma kulembera kalata mwamuna wake waku Joniyo poiphatikizila ndi kalata yomwe analemba maiyo. Nkhaniyi itakamupeza mwamunayo ku Joni sanapupulume koma kusunga kalatayo. Masiku apitawo mwamuna wa maiyo waku Joniyo anafika mderalo ndipo anangofikira kwa ankhoswe a mbali zonse komwe banja linatha dzuwa likuswa mtengo. Ku bwaloko maiyo anangoti kukamwa yasa kusowa choyankhula. Pamene amafuna kuti akalowe banja ndi njonda ya nchuuno ija anamva kuti njondayo inangobwera mderalo kudzamanga sukulu ndipo yabwerela kwao m’boma la Phalombe.

Atandala mnyumba kamba ka manyazi
Gulupa wina ntaunishipi ya Ndirande mu mzinda wa Blantyre akukhalira kutandala mnyumba chifukwa cha manyazi. Nkhaniyi ikuti mwamunayo ngozipereka kwambiri pa maso pa Ambuye kuphatikizapo kutumikira komanso kulalikira mau a Mulungu koma osadziwa kuti ngakhale amachita zonsezo amabisa manga ake. Kwa nthawi yayitali gulupayo wakhala akukaikitsa mamembala ambiri paza khalidwe lake la nchuuno komanso kumwa mowa wa midoli ngati kulibe mawa. Chifukwa cha ntchito zabwino zomwe mwamunayo amagwira pa mpingopo mamembala amzake amasowa poyambira kuti angamudzudzule. Paja pali mau oti fisi ndi fisi amaoneka ndi manga ake, masiku apitawa gulupayo anapita kopapila mowa wa midoliwo mpakana mbandakucha ndipo kumapeto kwake anakagona kunyumba kwa mai wina oyenda-yenda. M’mawa kutacha mwamunayo anatumiza uthenga kwa banja lake kuti anakagona ku ntchito ndipo anawatsimikizila kuti akakumana kunyumba ya chauta pa tsikulo lomwe linali lopemphera. Chifukwa choti mwamunayo mowa unatsalira m’mutu pa nthawi yazopereka njondayo inakapereka chishango m’malo mwa ndalama. Apa anthu adongosolo anaona ngati kutulo ndipo ananong’oneza mkulu wapa mpingopo kuti adzagawane malodzawo. Powafunsa za yemwe anachita izi anthuwo sanabise Chichewa koma kuloza gulupayo. Mphepo itampeza gulupayo paza nkhaniyi analiatsa liwiro la mtondo wodooka ngati analibe mafupa. Mamembala ambiri apa mpingopo ati sakumvetsa ndi zomwe wachita gulupayo ndipo pakadali pano gulupayo akukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi.

 

Ayaluka mwana atawapezelera akuchita za dama
Mayi wina kwa Chigaru mboma la Blantyre wayaluka mwana wake atamupeza akuchita chisembwere ndi mphongo ina ku chipinda. Nkhaniyi ikuti mayiyo ali pa banja koma mwamuna wake anapita kukazisaka ku Joni. Pachifukwachi mayiyo anapezerapo mwayi wochita chibwenzi ndi mwamuna wina ndipo chibwenzicho chitafika pa mpondachimera anaiwala zoti ali pa banja nkumalowetsa mphongoyo m’nyumba. Mwana wake yemwe amakhala naye pakhomopo amanyansidwa ndi zimenezi ndipo anawachalira kuti tsiku lina adzawachititse manyazi. Patsikulo mpongoyo itafika usiku, mayiyo anapita kukatsegula chitseko poganiza kuti mwana wakeyo wagona. Atakomedwa ku chipindako mwanayo anadzambatuka nkukangofikira pakhosi pa mkuluyo kwinaku akumubulasha ndi mateche. Apatu mwamunayo sanachitire mwina koma kukuwa kuti anthu amuthandize ndipo mwa mwayi anthu ena oyandikana nawo nyumba anathamangira kumeneko. Pamenepa mkuluyo anapeza mpata nkuthawa koma ali wefuwefu. Apongozi ake a mayiyo atamva nkhaniyi, anatchaira lamya mwana waoyo ku joni kumufotokozera zonse koma akuti waakhumudwitsa chifukwa wangowayankha kuti ndamva ndikuuzani chochita. Pakadali pano anthu pamudzipo ali tcheru kuti amve zomwe mwamuna wa mayiyo anene pa nkhaniyi.

Banja litha kamba ka ulesi
Tili kwa Chigaru komweko mboma la Blantyre, banja lina latha mwamuna atalephera kupilira khalidwe la ulesi la mkazi wake. Nkhaniyi ikuti mwamuna wina m’mudzimo anakakwatira ku Mwanza ndipo anamutenga nkumakhala naye kwawo ngati mtengwa. Tsono vuto lomwe linalipo ndi loti mkaziyo anali wamanja lende chifukwa kuti samatha kulima ngakhale kuphika kumene. Pomukonda mkazi wakeyo, mwamunayo wakhala akumuphunzitsa ntchitozo ndipo ataona kuti zikukanika anauza mchemwali wake kuti amulankhulire kwa mkaziyo. Koma m’malo momva malangizowo, mayiyo anapsya mtima mpaka kutenga chingwe kukadzikhweza. Mwa mwayi anthu ena anamuona msanga ndipo anamupulumutsa. Pochita mantha ndi zimenezi, mwamuna wakeyo walandula kuti banja walilephera moti panopa anakamutula kwawo ku Mwanza poopa kuti atha kumupezetsa mavuto.

Get Your Newsletter