07/08/17

Written by  Newsroom

Mkulu wina abindikila mnyumba kamba ka manyazi
Mkulu wina yemwe akumuganizila kuti ndi mbala yothelatu kwa Mchinguza kufupi ndiku Nayuchi mboma la Machinga akubindila m’nyumba chifukwa cha manyazi.

07
August

Nkhaniyi ikuti mkuluyo ananamiza anthu m’mudzimo kuti achifwamba amuvulaza kwambili. Anthu anayamba kukhulupilila koma kenaka zinadziwika kuti mkuluyo amanama malinga anthu anaulula kuti mkuluyo anapita koba n’gombe kwa mkulu wina wochita bwino mdelalo. Kumeneko akuti anamugwila ndikuyamba kumuphika ndipo kenaka anayamba kumugwaza ndi chikwanje m’malo osiyanasiyana. Ngakhale anapita ku chipatala mkuluyo akuonekabe kuti ali pa ululu. Anthu a mdelalo akuti amadziwa bwino zakhalidwe la mkuluyo pobela anthu katundu osiyanasiyana kuphatikizapo zifuyo kotelo ena akuti tsopano walandila satifiketi kotelo kuti mwina sadzabanso ngakhale amati wachake ndi wa chake. Mkuluyo waululabe kuti amaba limodzi ndi sing’anga wina yemwe amawapatsa mankhwala ogonetsa tulo ndipo panopa wathawiola ku Mozambique. Panopa, mkulu-yo akubindikila m’nyumba chifukwa cha manyazi atadziwa kuti anthu akumulozaloza chifukwa cha nkhani-yi.

 

 

Gule wamkulu alira ng'ombe zitamutsotsombetsa
Gule wina wamkulu mdera la Chimutu m’boma la Lilongwe analira chokweza ng’ombe komanso bulu zitamutsotsombetsa mpaka kutsala pang’ono kukwela mu mtengo. Nkhaniyi ikuti mderalo munali mwambo omanga ziliza ndipo amai ambiri anachita chinmvano cha mavu kupita ku chigayo motsogozedwa ndi gulu wamkuluyo. Koma mwadzidzidzi ng’ombe ina yomwe inali itangobereka kumene itaona guleyo inayamba kuthamangitsa guleyo poganizila kuti amafuna kumulanda mwana wake. Apa gulu wamkulu uja analiatsa liwiro la mtondo odooka nkukadzikwirila pa mulu wa mapesi a chimanga ndipo ng’ombe ija itafika pa mulupo imaona ngati gule wankulu uja akuthamangabe ndipo inangopitilira . Cha mafupi ndipa malopo naye bulu anaona gule wamkuluyo uja ndipo apa anathamangira pomwe anadzigwetsa gule wamkulu uja uku akulira chifukwa chodabwa ndi gule wamkuluyo. Choseketsa gule wamkuluyo analiatsanso liwiro ngati analibe mafupa mpakana kukalowa mbafa momwe mai wina amasamba mpakana maiyo kukuwa kuti gule wamkulu akufuna kumugwirira. Apa chipwilikiti chinabuka pakati pa amaiwo ndipo kumapeto kwake gule wamkuluyo zinamukoka manja mpakana anayamba kupumila madzala mphuno. Gule wamkuluyo wanenetsa kuti wachimina ndipo akuganiza kusiya zotumikira kudambwe. Pakadali pano gule wamkuluyo akukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.

 

Mnyamata wina asowa mosadziwika bwino
Anthu a mdera la Namadzi m’boma la Zomba akukhala mwa mantha ndi kusowa kosadziwika bwino kwa mnyamata wina. Nkhaniyi ikuti mnyamatayo zaka zapitazo anapita ku Joni kogwira ntchito ndipo anasiya banja lake mbuyo. Ali ku Joni-ko mkazi wake wakhala akuvutitsa poimba terefoni komanso kulemba kalata kuti mwamunayo abwerere chifukwa choti ati anali ndi chifundo kuti amuone. Izi zitachita kwa nthawi yayitali mwamunayo anabwereladi kuno kumudzi ndipo tsiku lofika anakafikira kwao kwa mkaziyo. Koma zodabwitsa makolo a mkaziyo sanasangalale ndikufika kwa mkamwiniyo chifukwa mwa zina akhala akulangiza mwana waoyo kuti asamange banja ndi mnyamatayo. Pofuna kumuonetsa kuti samamufuna makolo a mkaziwo anakasumila mkamwiniyo kuti akuumilira pakhomopo ndipo kwa iwo amaona kuti mkamwiniyo anali ndi maganizo ofuna kuzembetsa mwana waoyo. Nkhaniyi inakafika kwa mikoko yogona komanso achitetezo anaitanitsadi mnyamatayo kuti amve mbali yake pa nkhaniyi. Ku bwalo la milandi mlanduwo unamukomera mwamunayo ndipo anthu ambiri ati sakumvetsa kusowa mosadziwika bwino kwa mnyamatayo pamene ena ati akukhulupilira kuti mnyamatayo anasowa chifukwa chokhumudwa ndi zomwe akhala akumuchitila abale a mkaziyo kuphatikizapo makolo ake.

 

Mchembere ina ikuwidwa ngati fisi
Mchembere ina ya ana asanu anaikuwiza ngati fisi mdera la Chadza m’boma la Lilongwe. Nkhaniyi ikuti maiyo yemwe ngokwatiwa wakhala ali panja kwa zaka zochuluka ndipo zonse zimayenda bwino lomwe. Koma kwa zaka zambiri anthu mderalo kuphatikizapo anzake a mwamuna wa mkaziyo akhala akumuuza mwamunayo kuti mkazi wake akuyenda ndi njonda zina kuphatikizapo anyamata achichepere koma wakhala akuyankha kuti adzagwira yekha. Chifukwa chowawidwa mtima ndi nkhaniyi mwamunayo anakhazikitsa kagulu kake kuti adzilondola zochita za maiyo. Masiku apitawa kaguluko kanathamangira kunyumba kwa mwamunayo ndikukatsina khutu kuti akadzionere yekhe zomwe amachita mchembereyo ndi mnymatata wina okhala moyandikana ndi banjalo. Atakafika pa tchilero zinali zomvetsa chisoni komanso kukhumudwitsa atapezerela mkazi wakeyo ali buno-buno ndi mnyamatayo. Apa kunali kumenya kolapitsa mpakana anthu awiriwo kuyamba kulira ngati ana. Apa m’malo mwake mwamunayo anangothetsa banja koma akuwakwakwazila ku bwalo la nyakwawa. Njira yonseyo anthu ambiri amakuwiza anthuwo ngati aona fisi koma sizimawakhudza. Ku bwalo la nyakwawa mnyamatayo ndi maiyo anayankhula molimba mtima kuti ali okonzeka kupereka chindapusa chili chonse ndipo anamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sasiyana zomwe zinagwetsa mphwayi mwamunayo. Malinga ndi yemwe watitumizila nkhaniyi mnyamatayo athawitsana ndi mchembereyo.

Get Your Newsletter