04/08/17

Written by  Newsroom

Zilombo zilipila mbuzi kamba kolowa mtchalitchi
Zilombo ziwiri za gule wamkulu kwa Chakhadza mboma la Dowa azilipilitsa mbuzi imodzi chilichonse chifukwa cholowa mtchalitchi cha mpingo wina m’deralo.

04
August

Nkhaniyi ikuti zilombozo zinapita pa malo ena omwera mowa ndipo pochoka kumeneko zinakalowa mtchalitchi china chomwe chili kufupi ndi kumalowo. Anthu ena ataona izi anakadziwitsa akhrisitu a mpingowo omwe nthawi yomweyo anathamangira kutchalitchiko kukaona za malodzazo. Kumeneko akhristu-wo anakakomana nazo zikutuluka mtchalitchimo ndipo anakhumudwa kwambili mpaka anakatula nkhaniyi kwa akuluakulu a mpingowo. Apa akuluakuluwo anatengera nkhaniyi kwa mbusa wamkulu yemwe analamula kuti akhrisitu asalowemonso kukapemphera pokhapokha mbusa wa mpingowo atapita kukapemphera kuti ziwanda zoipa zichoke mtchalitchimo. Tsono pano mbusayo akuti anakapemphelera tchalitchicho ndipo pali chiyembekezo choti mawa lamulungu akhrisitu ayambanso kulowa mtchalitchimo. Pakadali pano zilombo ziwirizo zinakaonekera ku bwalo komwe azilamula kuti zipereke mbuzi imodzi chilichonse ndipo mfumu ya m’mudzimo ayilamulanso kuti ipereke mbuzi ziwiri ati kamba koti ikulekelera makhalidwe woipa m’mudzi mwake. Panopa sizikudziwika ngati mbuzizo zaperekedwa koma akuti mbuzi zinayi zonsezo zipita kwa gogo chalo komwe akuluakulu a mpingowo anakadandaula nkhaniyi.

Akakamila mkazi wake 
Mwamuna wina ku Zaone mboma la Zomba akumuganizira kuti anamudyetsa kondaine atakakamira kwa mkazi wake koma chonsecho anamupezelera ali ndi mphongo ina. Nkhaniyi ikuti mwamunayo amagwira ntchito ku Lilongwe ndipo mkaziyo atatsala, anapeza chibwenzi chomwe anthu akhala akumupeza nacho kangapo konse ngakhale njondayo ndi yokwatira. Tsono chomwe chachitika panopa nchakuti, mwana wa mwamuna wa mayiyo anapezelera awiriwo ali ngwindi pa malo ena ndipo apa anayamba kuthibula mwamunayo kenaka nkumuuza kuti amupatse foni. Mwa mantha njondayo inapereka foniyo ndipo kenaka inayamba kuthawa. Pamene mnyamatayo amafuna kuti azithamangitsa njondayo, mayi ake anamugwira koma akadadziwa sakadachita chifukwa anawatembenukira nkuyamba kuwaumbudza kwa chakwanuleka. Yemwe watumiza nkhaniyi wati m’mene izi zimachitika nkuti mwamuna wa mayiyo akubwera ku Lilongwe ndipo foni yochokera kwa abale ake kumufotokozera nkhaniyi inamupeza mu njira. Achibalewo analangiza wawoyo kuti asafikire kwa mkaziyo ndipo m’malo mwake akafikire kwawoko koma iye anangotayira malangizowo ku nkhongo. Atafika kwa mkazi wakeyo kumufunsa za nkhaniyi anayamba kuchita makani ndipo mwamunayo akuti sanapitilizenso kumufunsa nkhaniyi. Izi zinapsyetsa mtima mwana wakeyo ndipo nthawi yomweyo anayamba kuthibula mayi akewo kwinaku akudzudzula atate akewo chifukwa cholephera kukhaulitsa mayi akewo. Pakadali pano mayiyo akuti wachoka pakhomopo kusiya mwamunayo yekha ndipo komwe walowera sikukudziwika. Ndipo abale ake a mwamunayo ati apondaponda mwa sing’anga kuti waoyo achoke pakhomopo chifukwa ati zomwe zikuchitikazo zingooneteratu poyera kuti mayiyo anadyetsa mwamuna wakeyo konda ine.

 

Azimayi awiri ena azetsa chisokonezo pa maliro
Amayi awiri ku Blantyre awalamula kuti apereke chindapusa cha K10,000 aliyense chifukwa chodzetsa chisokonezo pa Maliro. Nkhaniyi ikuti mu September chaka chathachi, m’mudzi mwa Gulani mudachitika Maliro ndipo monga mwa mwambo, Mfumu imayenera kulankhula pa mwambowo. Koma nthawi yoti amfumu ayankhule itakwana, amayi awiriwo anayamba kukuwiza nyakwawa ya m’mudzimo kuti ikhale pansi ndipo isayankhulenso. Amayiwo akuti sadalekere pomwepo koma kulawilira ku nyumba ya nyakwawayo tsiku lotsatira kukayilalatira kotheratu. Izi zidachititsa kuti Nyakwawayo ikamang’ale ku polisi ndipo amayiwo anatengeredwa ku khothi. Tsiku lokaonekera m’khothilo, amayiwo adaukana mlanduwo koma mboni za boma zinapereka umboni wokwanira kuti chisokonezocho chidachitikadi. Ataunika maumboniwo,lachiwiri lapitali, oweruza mlandu m’khothi la midima ku Limbe,anapeza amayi awiri onsewo wolakwa ndipo anagamula kuti aliyense apereke chindapusa cha K10,000. Apa amayiwa anapempha bwalolo kuti liwaganizire powachepetsera ndalamayo ati kamba koti amayang’anira mabanja awo. Koma bwalolo silinamve zimenezi ndipo linati zomwe anachita amayiwo nkungowonjezera ululu m’mitima ya anamfedwa kotero kuti akuyenera kupereka chindapusacho, kuti anthu ena omwe ali ndi khalidweli atengerepo phunziro.

Azimayi akunthana kamba kolimbilana kasitomala

Amayi awiri athibulana koopsya pa msika wina ku Blantyre chifukwa cholimbirana kasitomala. Nkhaniyi ikuti m’modzi mwa amayiwo adayamba kalekale kugulitsa malonda pa msikapo ndipo akuti ali ndi makasitomala ambili. Tsono chomwe chachitika panopa nchakuti mayiyo wasintha malo omwe amakhala ndipo wamanga benchi patali pang’ono ndi malo ake oyambawo. Tsono dzulo laliwisili, kasitomala wina anafika pa malo akale a mayiyo ndipo atapezapo mayi wina wachilendo, anangogula pomwepo poganizira kuti mayiyo wasiyira nzake malondawo. Izitu akuti zimachitika mayiyo akukuwa kuitana kasitomalayo kuti ali pamalo atsopanowo koma vuto ndi loti kasitomalayo samamva chifukwa cha phokoso mu msikamo. Apatu mayiyo zinamuwawa kwambili chifukwa akuti mkuluyo ndi kasitomala wake wamkulu yemwe amagula zinthu zambili komanso samanenelera ndipo nthawi zina akuti amumusiyira change. Pachifukwachi mayiyo anayamba kulalatira nzakeyo koma kasitomalayo anakhumudwa kwambili ndipo anasiya amayi awiriwo akukangana. Mkanganowo utakula, amayiyo anayamba kumenyana koma poti mwamuna nzako mpachulu, umalinga utakwerapo, mayiyo anamenyedwa koopsya ndipo chifukwa cha thamo anthu sanamuleretse msanga mpaka anachoka pamalopo ali mbuu kutuwa malinga nkuti anamugwetsa pansi nkumupondelera uku akumuthibula. Pakadali pano amayi awiriwo akuonana ndi diso la nkhwezule ndipo kasitomalayo sakuonekanso mu msikamo chifukwa chokhumudwa ndi nkhaniyi.

 

Get Your Newsletter