03/08/17

Written by  Newsroom

Atandala mnyumba kamba ka manyazi

Mwamuna wina yemwe ndi mwini nyumba zina zochititsa lendi ku Ndirande mu mzinda wa Blantyre akukhalira kutandala mnyumba chifukwa cha manyazi.

03
August

Nkhaniyi ikuti mwamunayo ali nyumba zake zopitilira khumi zochititsa lendi mderalo koma chodandaulitsa kwa nthawi yayitali akhala akuchitila nkhanza zosiyana-siyana anthu omwe amakhala mnyumba-zo. Mwa zina wakhala akukweza nyumba zake akazindikira kuti anthu khumi akukhala mnyumba imodzi ngati banja ati ponena kuti nyumba yake imaonongeka mofulumila ndi kuchuluka kwa anthu komanso ati anthuwo amachititsa kuti ntchito zaukhondo zisamayende bwino. Miyezi ingapo yapitayi anthu okhala mnyumbazo akasonkherana ndalama zogulira magetsi olipiliratu mwamunayo amazimitsa dala-dala switchi ya magetsi ati ngati njira imodzi yokhaulitsila anthuwo chikhalireni anthuwo amagula okha magetsiwo. Pa chifukwachi anthuwo tsiku lina anapangana zokhaulitsa mkuluyo pomuuza kuti akuchoka mnyumba zake nthawi imodzi ndipo izi amazichita mogwirizana ndi mikoko yogona komanso anthu ena omwe akhala asakusangalala ndiza khalidwe la mwamunayo. Apa mwamunayo anasala pang’ono kudziipitsila uku akunjenjemera. Kumapeto kwake mwamunayo anasowa mosadziwika bwino pakhomopo ndipo malipoti ati pakadali pano akukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.

 

Mtengwa wina udabwitsa anthu

Mtengwa wina ku Area 24 mu mzinda wa Lilongwe wadabwitsa anthu pa zomwe wachita. Nkhaniyi ikuti maiyo atamangitsa banja lake ndipo patadutsa masiku ochepa mwamuna wake anapita ku Joni ndipo anasiya maiyo m’manja mwa makolo ake. Zinthu zitayamba kuyenda bwino ku Joni-ko mwamunayo anatumiza ndalama mcholinga choti mkazi wake amutsatile ndipo zinathekadi. Mkaziyo ndalama zitafika anali ndi chimwemwe chodzaya tsaya koma osadziwa kuti anali ndi kampeni ku mphasa. Tsiku lonyamuka litakwana mkaziyo anayamba kuimbilana foni ndi njonda inanso yomwe imakhala mdziko lomwelo mpakana kuchingamilana mu mzinda wa Durban. Masiku angapo atapita mwamuna wake anali odabwa kuti sakuthanso kulumikizana ndi mkazi wake uja. Koma paja pali mau oti palibe chinsinsi pansi pa thambo munthu winanso yemwe amadziwa za ubwenzi wa anthuwo anaimbila foni mwamuna wake ndikumufotokozera kuti anamuona ndi njondayo. Apa mwamunayo sanakhumudwe koma kuimbila foni mwamuna mzakeyo koma njondayo inauza mzakeyo kuti asade nkhawa njoleyo ili manja mwake. Nkhaniyi itafika kwa makolo a mbali zonse zinali zokhumudwitsa ndipo pakadali pano makolo a mkaziyo akusowa poyambila.

 

Adzukulu akana kukumba manda

Anafedwa ena mdera la Lisanjala m’boma la Zomba anaona ngati kutulu adzukulu atakana kukumba manda. Nkhaniyi ikuti anthu ambiri mderalo kuphatikizapo adzukulu akhala akudzudzula banjalo kuti sililabadila zosonkha-sonkha zina zili zonse mavuto osiyana-siyana akachitika mderalo. Pa chifukwachi adzukuluwo mderalo komanso mikoko yogona akhala akukambilana kukachipinda komata kuti banjalo adzalikhaulitse likadzakomana ndi vuto lina lirio lonse. Masiku apitawo munthu wina wapa banjapo anamwalira ndipo anafedwa anakadziwitsa nyakwawa ya mderalo ndipo nayonso inakadziwitsa adzukulu. Tsiku loika maliro litakwana adzukulu anapita kumanda kuti akagwire ntchito yao koma chodabwitsa anangokhala osagwira ntchito ili yonse zomwe zinachititsa kuti anafedwa akhale odabwa. Koma anthu ena kuphatikizapo mikoko yogona sanabise mau koma kukumbutsa banjalo za zomwe akhala akuchita. Apa banjalo linapepesa ndikunena kuti sadzayambilanso zomwe zinapangitsa kuti ntchito yokumba manda ipitilire koma nthawi itatha kale komanso kuchititsa kuti mwambo wa maliro uchedwe komanso zinadzetsa mpungwepungwe waukulu pakati pa ampingo ndi anthu ena omwe amatumikira pa zovutazo. Anafedwawo kumapeto kwake anawalipitsa thumba la chimanga, tambala komanso ndalama.

 

Atsikana achichepere adabwisa anthu

Anthu ena m’dera la Nyambi ku Machinga akukhala mwa mantha ndi zomwe achita atsikana ena achichepere awiri m’deralo. Nkhaniyi ikuti mderalo munali mwambo wa mapemphero koma mwambowo unathera ali mkwao-mkwao atsikana ena omwe anafika mwadzidzidzi pa malopo uku akuvina modabwitsa ngati momwe ichitila mbalame ikamauluka mwamba kenako nkuchoka pa malopo mosadziwika bwino. Pamene amachita izi anthu ambiri omwe anali pa malopo anaona ngati akulota zomwenso zinadzetsa mantha aakulu kwa mamembala apa mpingopo. Patadutsa nthawi yochepa atsikanawo anatulukiranso pa malopo ndikuyamba kufotokozera anthu omwe anasonkhana pa malopo kuti amayerekezera zomwe amachita nthawi zina kuti ngati zili zothekadi masana. Malinga ndi yemwe watitumizila nkhaniyi anthu ambiri ati akukhala mwa mantha komanso ati sakumvetsa ndi zomwe achita atsikanawo. Anthu ambiri mderalo ati akukhulupilira kuti anawo amachita zamatsenga ndipo mikoko yogona yagwirizana zopondaponda kuti anawo awachotse ziwanda komanso kuthana ndi aliyense yemwe anachita zachipongwezo.

Get Your Newsletter